Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Warwick Gawo 1 (Kuyambira May Mpaka August 2014)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Warwick Gawo 1 (Kuyambira May Mpaka August 2014)

A Mboni za Yehova akumanga likulu lawo latsopano ku Warwick munzinda wa New York. Kuyambira mu May mpaka August 2014, ntchito yomanga galaja, maofesi ndiponso nyumba zogona C ndi D yakhala ikuyenda mofulumira kwambiri. Zithunzi zotsatirazi zikusonyeza ntchito zina zomwe zinachitika m’miyeziyi.

Pulani ya nyumba za ku Warwick. Kuyambira kumanzere kupita kumanja:

  1. Galaja

  2. Nyumba Yoimikamo Magalimoto a Alendo

  3. Nyumba Yogona Komanso Malo Oimika Magalimoto

  4. Nyumba Yogona B

  5. Nyumba Yogona D

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona A

  8. Maofesi

May 1, 2014—Ku Warwick

Chithunzi chojambulidwa moyang’ana kunyanja yotchedwa Sterling Forest Lake (Blue Lake) yomwe ili cha kumpoto. Chapansipo ntchito yomanga nyumba yogona D ili mkati. Ndipo chakufupi ndi nyanja akuumba masilabu a konkire omangira nyuma yogona C.

May 14, 2014Malo opangirapo zinthu zina

Ogwira ntchito akulumikiza mbali zosiyanasiyana zopangira bafa. Bafali lili ndi mafulemu, makoma komanso m’makomamu abooleratu tinjira todutsa mapaipi amadzi ndi a magetsi. Bafali lilinso ndi malo odutsa mpweya. Akalimaliza kulumukiza, adzalinyamula kukaliika kumene likakhale.

May 22, 2014—Galaja

Ogwira ntchito akumangirira mapaipi. Malowa adzagwiritsidwa ntchito ngati chipinda chodyera pa nthawi yomwe ntchitoyi ili mkati ndipo muzidzakwana anthu pafupifupi 500, komanso m’malo ena m’nyumba yomweyi mudzatha kukhala anthu enanso 300. Chakumapeto kwa ntchitoyi malowa adzasiya kuwagwiritsa ntchito monga chipinda chodyera ndipo adzamaliza kuwakonza kuti akhale galaja.

June 2, 2014—Galaja

Ogwira ntchito akumwaza dothi lapadera kuti abzalepo zomera padenga. Denga lomwe amabzalapo zomera limathandiza kukatentha kapena kukazizira, kuthamanga kwa madzi a mvula ndiponso limasefa zinthu zoipa za m’madzi a mvula.

June 5, 2014—Maofesi

Nyumbayi idzakhala yolumikiza nyumba zitatu ndipo kukula kwake ndi masikweya mita 42,000. Chithunzichi chikusonyeza ogwira ntchito akuika zitsulo zolimbitsira chipilala.

June 18, 2014—Galaja

Ogwira ntchito ali pa denga ndipo akugwiritsa ntchito moto wa gasi pokonza dengalo. Iwo adzimanga ndi zodzitetezera kuti asagwe.

June 24, 2014—Nyumba yogona C

Ogwira ntchito akumangirira mapaipi amene amalowetsa mpweya wozizira ndi kutulutsa mpweya wotentha. A Mboni 35 pa 100 aliwonse omwe akugwira ntchito ku Warwick ndi akazi.

July 11, 2014—Montgomery, New York

Malowa anakonzedwa mu February 2014 kuti azigwiritsidwa ntchito monga mosungira katundu ndiponso momangirira zipangizo. Malowa ndi aakulu masikweya mita 20,000. Zipangizo zomwe zikuoneka zoyera, m’mwamba pachithunzichi ndi mabafa omwe awalumikiza kale ndipo akufuna kuwatumiza ku Warwick.

July 24, 2014—Nyumba yogona C

Chithunzichi chikuonetsa nyumba yogonayi tikaima kumpoto cha ku m’mawa. M’nyumbayi muzidzakhala anthu pafupifupi 200 ogwira ntchito pa likululi. Nyumba zambiri zogona zidzakhala zazikulu masikweya mita 30 kapena 55 ndipo zidzakhalanso ndi khitchini, bafa ndiponso kakhonde.

July 25, 2014—Nyumba yokonzera zinthu komanso koimika magalimoto

Kukonza malo omwe amangepo nyumba. M’mwamba pachithunzichi, mashini akuphwanya miyala yomwe aifukula pamalowa kuti idzagwiritsidwe ntchito zina. Pamene azidzamaliza ntchito yomanga ku Warwick, dothi lokwana matani 39, 000 lidzakhala litachotsedwa pamalowa. Magalimoto onyamula dothi pafupifupi 23 akumagwira ntchito pamalowa tsiku lililonse.

July 30, 2014—Galaja

Ogwira ntchito akubzala zomera padenga.

August 8, 2014—Ku Warwick

Chithunzi chosonyeza malo omwe akumangapo likulu ku Warwick moyang’ana kum’mwera cha kumadzulo. M’munsi cha kumanzere pachithunzichi ndi nyumba imene pazidzaima galimoto za alendo. Tsiku lililonse padakali pano nyumbayi imadzaza ndi galimoto za omwe akugwira ntchito kumalowa. A Mboni ena amayenda ulendo wa maola 12 pagalimoto kuti akathandize kugwira ntchito kumalowa kwa masiku atatu kapena 4.

August 13, 2014—Galaja

Ntchito yokonza chipinda chodyera chongoyembekezera yatsala pang’ono kutha. Masikilini (omwe sanamangiriridwe) ndiponso masipika zidzathandiza ogwira ntchito kumalowa kuti azilumikizidwa ku ofesi ya nthambi ya ku United States pa nthawi ya kulambira kwa m’mawa ndiponso pa mapulogalamu ena auzimu.

August 14, 2014—Maofesi osiyanasiyana

Ogwira ntchito akuika konkire. Wogwira ntchito amene ali chakumanja pachithunzipa akugwiritsa ntchito kamashini pofuna kuonetsetsa kuti konkire wagwirana bwino ndi zitsulo.

August 14, 2014—Maofesi osiyanasiyana

Ogwira ntchito akuikiratu mapaipi amagetsi kuti kenako aike silabu pamwamba pake.

August 14, 2014—Maofesi osiyanasiyana

Chithunzi chosonyeza ntchito yoika konkire itatsala pang’ono kutha. Konkire amene anathira pamenepa yemwe anali wolemera matani 540, anali wambiri zedi poyerekezera ndi amene anathira m’malo ena ku Warwick. Konkireyu ankamusakanizira pa malo ena kenako ankamunyamula pogwiritsa ntchito magalimoto 8 pomupititsa pamalowa ndipo panali mapampu awiri omwe ankawagwiritsa ntchito pothira konkireyu. Ntchitoyi inatenga maola 5 ndi hafu. Chimene amanga pakatipo chili ndi masitepe omwe anthu adzawagwiritse ntchito popita m’zipinda za m’mwamba.

August 14, 2014—Nyumba yogona C

Ogwira ntchito akumanga kampanda padenga la nyumba pomwe ogwira ntchito ena akumanga maziko a nyumba yogona.

August 15, 2014—Nyumba yogona C

Ogwira ntchito ali pa chipinda chachitatu kuchoka pansi ndipo akulandira bafa lolumikiza kale. Zinthu zambiri zimene akugwiritsa ntchito ku Warwick akumazilumikizira kumalo ena. Zimenezi zikuchititsa kuti ntchito iziyenda mofulumira komanso pamalowa pasamaunjikane katundu wambiri.

August 20, 2014—Nyumba yogona C

Ogwira ntchito akumangirira khoma lomwe analipanga kale. Konkire wopangira makomawa anamusakaniza kale ndi penti. Makomawa safunikanso kuwapenta ndipo angafunike kuwakonza mwa apa ndi apo. Kuika makomawa sikufuna nthawi yambiri ndipo zimenezi zithandiza kuti ntchito idzathe pa nthawi yake.

August 31, 2014—Ku Warwick

M’mene malowa akuonekera tikaima kum’mwera cha kumadzulo. Kutsogolo kwa chithunzichi kukuonetsa ogwira ntchito akuyala mawaya kuti adzawonjezerepo chipinda china chosanja pa nyumba yogona D. Chakumbuyoko kukuoneka nyumba yogona C yomwe aimaliza kale.