Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Warwick—Gawo 4 (Kuyambira May Mpaka August 2015)

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Warwick—Gawo 4 (Kuyambira May Mpaka August 2015)

Zithunzizi zikusonyeza mmene ntchito inayendera kuyambira May mpaka August 2015 pomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova komanso zimene anthu anachita podzipereka kuti athandize pa ntchitoyi.

Chithunzi cha mmene nyumba za ku Warwick zidzaonekere ntchitoyi ikadzatha. Kuyambira kumanzere kupita kumanja:

  1. Galaja

  2. Nyumba Yoimikamo Magalimoto a Alendo

  3. Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

  4. Nyumba Yogona B

  5. Nyumba Yogona D

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona A

  8. Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

May 6, 2015​—Ku Warwick

Munthu akulowetsa makina enaake m’nyanja ya Sterling Forest kapena kuti Blue Lake. Makinawa akaikidwa adzathandiza kuti zinyalala zochoka m’nyanjamo zisamatseke malo amene madzi ayenera kutulukira akadzaza.

May 6, 2015​—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Anthu akufayira konkire pambali ina ya denga la panyumbayi. Njirayi ndi yachangu kwambiri kuposa njira zina zothirira konkire m’malo otere.

May 15, 2015​—Ku Warwick

Mayi wina akujambula zithunzi zothandiza anthu kudziwa mmene ntchitoyi ikuyendera. Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limaona zithunzi zimenezi mlungu uliwonse.

May 30, 2015​—Ku Tuxedo

Banjali lachokera ku California ndipo langodzipereka kuti lidzathandize pa ntchito yoika mapaipi a madzi. Anthu ambiri anabwera ku Tuxedo pa tsiku limeneli. Ku Tuxedo n’kumene anthu amafikira kuti akonzekere kukagwira ntchito ku Warwick. Pa tsiku loyamba la mwezi wa August anthu okwana 707 anafika kuti adzagwire ntchito yomangayi. Chiwerengerochi chinali chokwera kuposa masiku ena onse.

June 9, 2015​—Nyumba Yogona B

Anthu analembedwa ntchito kuti alumikize khoma la nyumbayi pogwiritsa ntchito mashini okwezera zinthu m’mwamba. Nyumbayi inali yomaliza kuikidwa makoma komanso mawindo.

June 16, 2015​—Nyumba Zogona C ndi D

Anthu enanso olembedwa ntchito akuika njira yoti anthu azidutsa pakati pa Nyumba Zogona C ndi D.

June 25, 2015​—Nyumba Yogona C

Munthu akudzala kapinga mochita kuyala kumbali yakumadzulo kwa malowa.

July 2, 2015​—Ku Warwick

Anthu akukonza malo otulukira madzi akadzaza m’nyanja ija. Malowa anamangidwa koyamba m’zaka za m’ma 1950, ndiye akuwakonza kuti agwirizane ndi mmene nyengo ilili panopa. Masiku ano mvula imagwa kwambiri kuposa kale ndipo akufuna kuteteza malo awo ku Warwick komanso malo ena oyandikana nawo kuti asamawonongeke ndi madzi osefukira.

July 15, 2015​—Nyumba Yogona A

Kuti anthu asamapanikizane pogwira ntchito, ena akugwirabe ntchito zina mpaka usiku monga kupenta ndiponso kuika zinthu zina zotetezera mapaipi. Pa nthawi imene panali mashifiti awiri, anthu ambiri ankagwira ntchito kuyambira 3 koloko madzulo mpaka 2 koloko usiku.

July 20, 2015​—Nyumba Yogona D

Munthu wina akuphunzitsa mnzake ntchito yoika zinthu zotetezera mapaipi.

July 21, 2015​—Nyumba Yogona B

Munthu wina akupenta zitsulo za njira yothandiza anthu kudutsa pakati pa Nyumba Yogona B ndi Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu.

July 27, 2015​—Ku Tuxedo

Anthu akudikirira mabasi pamalo oimika magalimoto kuti apite kukagwira ntchito ku Warwick. Pali mabasi ambiri amene anthuwa amakwera popita ndiponso pobwera kuchokera ku Warwick.

July 27, 2015​—Ku Tuxedo

Amuna atatu amene amagwira ntchito ku Warwick akumetetsa tsitsi. Malo ometera ali ku Tuxedo, Warwick ndiponso ku Montgomery. Anthu oposa 400 amametetsa tsitsi kumalowa mlungu uliwonse.

August 3, 2015​—Ku Warwick

Akukonzekera kuthira konkire pamalo amene anakumbapo zitsime 120 zomwe ndi zakuya mamita 150. Adzagwiritsa ntchito zitsimezi pothandiza kutenthetsa nyumba m’nyengo yozizira ndiponso kuziziziritsa m’nyengo yotentha. Njira yotenthetsa ndi kuziziritsa imeneyi siwononga ndalama zambiri komanso chilengedwe.

August 7, 2015​—Ku Montgomery, New York

Kumalowa, amalonda amabweretsa zinthu zimene zidzagwiritsidwe ntchito pomanga ku Warwick.

August 14, 2015​—M’tauni ya Tuxedo Park ku New York

Banja lina limene limagwira ntchito ku Warwick likudyera limodzi ndi banja lina la ku Tuxedo Park. Mofanana ndi banjali, mabanja ambiri a Mboni za Yehova amalola kuti anthu ena ogwira ntchito ku Warwick afikire m’nyumba zawo..

August 17, 2015​—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Mayi wina akugwiritsa ntchito chipangizo chounikira kuti adziwe ngati malo enaake ndi otsetsereka kapena okwera.

August 20, 2015​—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Amaliza kuika mawindo kumalo amene alendo azidzafikira podzaona malo ku Warwick.

August 26, 2015​—Warwick site

Kuyambira May mpaka August, anaika makoma ndiponso madenga a Nyumba Yogona B, yomwe inali yomaliza. Anaikanso njira zonse zodutsa anthu popita kunyumba zina ndipo anayamba ntchito yodzala kapinga, maluwa ndi mitengo.