Pitani ku nkhani yake

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Warwick—Gawo 2 (Kuyambira September Mpaka December 2014)

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Warwick—Gawo 2 (Kuyambira September Mpaka December 2014)

Zithunzizi zikusonyeza mmene ntchito inayendera kuyambira September mpaka December 2014 pomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova.

Chithunzi cha mmene nyumba za ku Warwick zidzaonekere ntchitoyi ikadzatha. Kuyambira kumanzere kupita kumanja:

  1. Galaja

  2. Nyumba Yoimikamo Magalimoto a Alendo

  3. Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

  4. Nyumba Yogona B

  5. Nyumba Yogona D

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona A

  8. Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

September 11, 2014—Nyumba Yoimikamo Magalimoto a Alendo

Akulumikiza zitsulo zoti adzaike padenga la ku Nyumba Yogona C.

September 18, 2014—Ku Warwick

Chithunzi chojambulidwa kuchokera kum’mwera n’kuyang’ana kumpoto komwe kuli nyanja ya Sterling Forest kapena kuti Blue Lake. Nthawi zina mashini okwezera zinthu m’mwamba okwana 13 ankagwira ntchito nthawi imodzi. Pachithunzichi anthu akuthira konkire kuti ayale maziko a Nyumba Yogona B.

September 26, 2014—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Zitsulo zoti ziikidwe panyumbayi. Adzagwiritsa ntchito zitsulo zambiri panyumba imeneyi n’cholinga choti ikhale yamphamvu komanso imangidwe mwachangu.

October 9, 2014—Ku Warwick

Anthu akulumikiza denga limene lidzaikidwe pa Nyumba Yogona C. Akuika malata komanso zinthu zina zoteteza kuti madzi asamadzalowe. Chakumanzereko, anthu akulumikiza mbali inanso ya dengali.

October 15, 2014—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Anthu akuika zitsulo za kumbali yakum’mwera chakumadzulo kwa nyumbayi. Mbali imeneyi kudzakhala khitchini, chipinda chodyera, dipatiment yochapira zovala ndiponso madipatimenti ena.

October 15, 2014—Ku Warwick

Munthu amene akuika zolumikizira mapaipi odutsamo zinthu zonyansa, akulandira tsache.

October 20, 2014—Ku Warwick

Khomali analipanga mongoyerekezera n’cholinga choti asankhe njira yoti adzayalire njerwa komanso mtundu wa matope amene adzagwiritse ntchito. Anagwiritsanso ntchito khomali kuti likhale chitsanzo kwa anthu atsopano omwe anabwera kudzayala nawo njerwa. Pachithunzichi, akulichotsa chifukwa zimene ankafunazo zatheka.

October 31, 2014—Nyumba Yogona C

Mashini okweza zinthu anyamula mbali ina ya denga ndipo akuiika pamalo ake. Denga losongoka limene lidzakhale kumapeto kwa nyumba iliyonse yogona lidzathandiza kuti nyumbayo izioneka bwino.

November 7, 2014—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Thanki limene limalowa malita 95,000 a mafuta likuikidwa pamalo ake. Mafuta a m’matankiwa azidzagwiritsidwa ntchito m’makina otenthetsera madzi komanso nyumba.

November 12, 2014—Nyumba Yogona C

Chithunzi chosonyeza mbali yakum’mwera ya nyumbayi ndipo nyanja ija ikungooneka pang’ono kumanzere kwa chithunzichi. Nyumbayi aikongoletsa pogwiritsa ntchito mitundu yosiyanasiyana ya penti.

November 21, 2014—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Banja lina likugwira ntchito limodzi poika mapaipi a madzi kuti anthu ena ayambe kuthira konkire.

November 28, 2014—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Akuchotsa sinowo, kapena kuti chipale chofewa, padenga.

December 1, 2014—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Banja linanso likuona pulani ya mapaipi a madzi.

December 10, 2014—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Ngakhale kuti nyengo sili bwino, anthu akugwirabe ntchito yokumba, akuika zitsulo pokonzekera kuthira konkire ndipo pamalo ena akuthira konkire. Pamwamba chakumanzere kwa chithunzichi atseka malo ena a nyumba ya maofesi ndi malona n’cholinga choti pa nyengo yozizira apitirize kugwira ntchito zina monga kuthira konkire kuti apange makonde ndiponso kupaka zotetezera moto.

December 12, 2014—Nyumba Yogona D

Anthu akumata zoteteza kuti madzi asamalowe pamakoma. Kenako adzaika zinanso kuti kunja kwa nyumbayo kuzioneka bwino.

December 15, 2014—Ku Warwick

Chithunzi chojambulidwa kuchokera m’mwamba moyang’ana kumadzulo. Nyumba zogona n’zimene zikuoneka zazitalizo. Nyumba yaikulu imene ikuoneka yoyerayo chapakati pa chithunzichi ndi maofesi ndiponso malo a zinthu zina. Malo onse a ku Warwick ndi a maekala 253 koma akumanga pambali yochepa chabe n’cholinga choti asawononge kwambiri nkhalangoyo.

December 15, 2014—Ku Warwick

Chithunzi chojambulidwa kuchokera m’mwamba moyang’ana kum’mawa. M’munsi mwa chithunzichi mukuoneka Nyumba Zogona C ndi D. Anthu akuika denga la Nyumba Yogona C.

December 25, 2014—Nyumba Yogona C

Munthu wina akuika zinthu zooneka ngati matabwa pansi m’chipinda chimene adzagwiritse ntchito monga chitsanzo. Anthu adzatha kusankha pakati pa mitundu 4 ya penti, matailosi, zinthu zina zoika pansi, zoika m’khitchini ndiponso m’bafa.

December 31, 2014—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Akumalizitsa kusalaza konkire ndi manja kuti malowo akhale otsetsereka pang’ono n’cholinga choti madzi akagwerapo asamangoima.

December 31, 2014—Nyumba Yogona C

Bambo wina wazaka 77 akulumikiza nthambo ya magetsi yokhala ndi timawaya tambiri. Pamalo onse padzafunika kuikidwa nthambo ngati zimenezi zotalika makilomita 32.