Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Philippines—Gawo 1 (Kuyambira February 2014 Mpaka May 2015)

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Philippines—Gawo 1 (Kuyambira February 2014 Mpaka May 2015)

Mboni za Yehova akumanga nyumba zatsopano komanso kukonzanso zina zakale ku ofesi yawo ya ku Philippines yomwe ili mumzinda wa Quezon. Poyamba ofesi ya ku Philippines inkasindikiza yokha mabuku koma panopa ofesi ya ku Japan ndi imene ikugwira ntchitoyi. Choncho akusintha nyumba yakale yosindikizira mabuku ku Philippines kuti ikhale ya Dipatimenti ya Makompyuta, Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, Yotumiza Mabuku ndiponso Dipatimenti Yomasulira Mabuku. Zithunzizi zikusonyeza ntchito zina zimene anthu agwira kuyambira February 2014 mpaka May 2015. Anthu a ku ofesiyi akuganiza kuti adzamaliza ntchitoyi pofika mu October 2016.

Chithunzi chosonyeza mmene ofesi ya ku Philippines idzaonekere akamaliza ntchitoyi. Nyumba zimene zikumangidwa kapena kukonzedwanso ndi izi:

  • Nyumba Nambala 4 (Zipinda Zogona)

  • Nyumba Nambala 5 (Dipatiment ya Utumiki ndiponso Yojambula Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera)

  • Nyumba Nambala 6 (Dipatiment Yosamalira Maluwa, Yokonza Magalimoto ndiponso ya Ntchito Yowotcherera)

  • Nyumba Nambala 7 (Dipatimenti ya Makompyuta, Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, Yotumiza Mabuku ndiponso Yomasulira Mabuku)

February 28, 2014​—Nyumba Nambala 7

Anthu akuika zinthu zinazake m’mapulasitiki n’cholinga choti zisanyowe. Zinthuzi zimaikidwa kukhoma kuti ziteteze nyumba koma munthu akazikhudza zimapangitsa khungu kuyabwa. N’chifukwa chake anthuwa avala zowateteza.

April 2, 2014​—Nyumba Nambala 7

Anthu akumalizitsa denga la situdiyo yojambula zinthu m’chinenero chamanja cha ku Philippines. Mabowo amene akuonekawo adzaikamo zipangizo zothandiza kuti mpweya wozizira uzifika paliponse m’situdiyomo.

October 21, 2014​—Pamalo a Ofesi

Akukumba malo oti aikemo mapaipi kuti madzi ozizira azidzadutsamo. Izi zizithandiza kuti madzi ozizira azifika kunyumba zonse za pa ofesiyi.

December 19, 2014​—Njira zodutsa m’mwamba zothandiza kuti anthu azitha kukafika ku Nyumba Nambala 1, 5, ndi 7

Njira zam’mwambazi zizithandiza kuti anthu azitha kukafika ku nyumba zikuluzikulu monga Nyumba Nambala 1, komwe kuli malo odyera. Zithandiza kwambiri anthu oposa 300 omwe amagwira ntchito mu Nyumba Nambala 7.

January 15, 2015​—Nyumba Nambala 5

Galimoto yolemera pafupifupi 5, 000 kilogalamu ikukweza malata padenga. Analemba ntchito anthu okhala ndi magalimoto osiyanasiyana okwezera zinthu kuti aziwathandiza.

January  15, 2015​—Nyumba Nambala 5A

Nyumba yansanjikayi ndi ya masikweya mita 125 ndipo adzaikamo zimbudzi ziwiri, masitepe komanso chikepe, m’malo moziika m’Nyumba Nambala 5 yomwe ili pafupi. Izi zidzathandiza kuti m’Nyumba Nambala 5 mukhale malo ambiri komanso kuti phokoso la chikepecho lisamasokoneze akamajambula mavidiyo ndiponso zinthu zina.

January  15, 2015​—Nyumba Nambala 5A

Anthu afunda ambulera chifukwa cha dzuwa ndipo akuika zitsulo zothandiza kuti konkire ikhale yolimba. Nthawi zambiri m’mwezi wa January kumatentha ndi madigiri pafupifupi 29 ndipo m’mwezi wa April kumatentha ndi madigiri pafupifupi 34.

March 5, 2015​—Nyumba Nambala 5

Anthu akuika matabwa padenga ndipo panyumbayi panalowa matabwa pafupifupi 800.

March 17, 2015​—Nyumba Nambala 5

Akusakaniza simenti pamanja kuti akagwiritse ntchito pa kantchito kenakake. Pali anthu oposa 100 amene akugwira nawo ntchito yomangayi omwe anachokera kumayiko ena monga Australia, Canada, France, Japan, New Zealand, South Korea, Spain ndiponso United States.

March 25, 2015​—Nyumba Nambala 5

Akukhoma malata padenga la Nyumba Nambala 5 yomwe poyamba inali ya Dipatimenti Yomasulira Mabuku. Nyumbayi ikukonzedwanso n’cholinga choti ikhale ya Dipatiment ya Utumiki ndiponso Yojambula Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera.

May 13, 2015​—Nyumba Nambala 5

Akudula tizitsulo tokaika pamakoma a maofesi ndipo akugwiritsa ntchito kachipangizo kenakake.

Onaninso

KODI NDANI AKUCHITA CHIFUNIRO CHA YEHOVA MASIKU ANO?

Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?

Alendo amaloledwa kudzaona maofesi athu. Tikukupemphani kuti inunso mupite kukaona zimene zimachitika kumeneko!