Pitani ku nkhani yake

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Warwick—Gawo 3 (Kuyambira January Mpaka April 2015)

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Warwick—Gawo 3 (Kuyambira January Mpaka April 2015)

Zithunzizi zikusonyeza mmene ntchito inayendera kuyambira January mpaka April 2015 pomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova.

zidzaonekere ntchitoyi ikadzatha. Kuyambira kumanzere kupita kumanja:

  1. Galaja

  2. Nyumba Yoimikamo Magalimoto a Alendo

  3. Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

  4. Nyumba Yogona B

  5. Nyumba Yogona D

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona A

  8. Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

January 2, 2015​—Galaja

Harold Corkern, yemwe amathandiza m’Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku ya Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yochokera m’Baibulo ya mutu wakuti, “Chitani Zonse Zimene Mungathe.” Anthu amapita ku Warwick kukakamba nkhani n’cholinga choti azikalimbikitsa anthu ogwira ntchito kumeneko.

January 14, 2015​—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Mbali ina ya nyumbayi yakutidwa ndi lona n’cholinga choti anthu azitetezedwa n’kumagwirabe ntchito pa nyengo yozizira. Mbaliyi kudzakhala chipinda chodyera, chipatala, khitchini komanso malo ochapira zovala.

January 16, 2015​—Nyumba Yogona D

Anthu akukonzekera kuti aike nthambo zamagetsi. Nthambo zokwana mamita 12,000 zaikidwa kale m’nyumba zogona. Ku Warwick, anthu anayamba ntchito zamagetsi malowo atangogulidwa kumene ndipo aipitiriza mpaka ntchito yonse itatha.

January 16, 2015​—Nyumba Yogona A

Munthu akumata tepi pakhonde kuti athire mankhwala oteteza kuti lisamawonongeke ndi madzi. Amathira mankhwalawa pa makonde am’mwamba okha.

January 23, 2015​—Nyumba Yogona A

Bambo ndi mwana wake wamkazi akugwira ntchito limodzi poika nthambo zamagetsi m’nyumbayi.

February 6, 2015​—Galaja

Anthu akudya m’chipinda chodyera chongoyembekezera. Tsiku lililonse, anthu oposa 2,000 amalandira chakudya.

February 12, 2015​—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Anthu akuika zitsulo pokonzekera kuthira konkire pamene padzakhale dipatiment yokonza zinthu.

February 12, 2015​—Nyumba Yogona C

Makalata ochokera kwa ana othokoza ntchito zimene anthu akugwira ku Warwick. Anthu ambiri amakathandiza pa nthawi yochepa moti anthu 500 amafika kumeneko mlungu uliwonse. Mu February 2015, anthu pafupifupi 2,500 ankagwira ntchito ku Warwick tsiku lililonse.

February 24, 2015​—Ku Warwick

Panopa ntchito yambiri inatha. Kuyambira January kufika April 2015, anamaliza kumanga makoma ndi madenga a nyumba zonse zogona komanso anamaliza kuika zitsulo za nyumba ya maofesi komanso malo a zinthu zina. Pa nthawi imeneyo, anthu anayambanso kulumikiza khoma la nyumba ya dipatiment yokonza zinthu, kukonza njira zopita kunyumba zogona komanso kukonza zoti madzi a m’nyanja ya Sterling Forest, kapena kuti Blue Lake, asamasefukire.

February 25, 2015​—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Apa m’pamene padzakhale masitepe opita maofesi am’mwamba. Kampani inayake ndi imene anaipatsa ntchito yomanga nyumbayi yomwe ili ndi nsanjika 5 ndipo a Mboni ndi amene anathira konkire.

February 26, 2015​—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Ngakhale kuti tsiku lina kunazizira kwambiri, anthu anagwirabe ntchito yoika zitsulo pokonzekera kuti adzathire konkire. Kuyambira January mpaka March sinowo, kapena kuti chipale chofewa, chinkagwa kwambiri. Anthu ankayesetsa kuchotsa chipalecho pamalo omwe ena ankagwirapo ntchito. Panalinso zipinda zina zimene ankazitenthetsa n’cholinga choti anthu ogwira ntchito azilowamo akazizidwa kwambiri.

March 12, 2015​—Nyumba Yoimikamo Magalimoto a Alendo

Munthu akuika malata padenga. Chakumapeto kwa April, pafupifupi madenga onse osongoka a nyumba zogona anali ataikidwa. Koma madenga ena a Nyumba Yogona B adzaikidwa m’mwezi wa June.

March 18, 2015​—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Chithunzichi chinajambulidwa ndi munthu amene anali m’mashini okwezera zinthu m’mwamba. Kutsogolo kwake kukuoneka Nyumba Yogona B.

March 18, 2015​—Nyumba ya Dipatiment Yokonza Zinthu Komanso Malo Oimika Magalimoto

Anthu aima pafupi ndi nyumba yoimikamo magalimoto ndipo akukambirana za pulani ya mapaipi a madzi. Kuti ntchito yonse ya ku Warwick iyende bwino pakufunika mapulani oposa 3,400.

March 23, 2015​—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Anthu anyamulidwa ndi mashini ndipo akukuta nyumbayi ndi lona kuti itetezedwe. Ku Warwick kuli maphunziro othandiza anthu ogwira ntchito kuti adziwe mmene angayendetsere mashini okweza zinthu m’mwamba komanso kugwiritsa ntchito mashini ena popanda kuchita ngozi. Amaphunziranso zimene angachite kuti asagwe akamagwira ntchito m’mwamba, kuti azigwiritsa ntchito zinthu zodzitetezera akakhala pamalo afumbi kapena ampweya woipa komanso kugwiritsa ntchito zizindikiro polankhula ndi ena ngati ali kutali kapena pali phokoso.

March 30, 2015​—Ku Warwick

Chithunzichi chinajambulidwa moyang’ana kumadzulo ndipo kukuoneka nyumba zogona. Chakumapeto kwa April, anali atayamba ntchito zina monga kuika mapaipi a madzi komanso magetsi m’Nyumba Zogona A, B, ndi D, zomwe zikuoneka pachithunzichi. Koma m’Nyumba Yogona C (yomwe sikuoneka pachithunzichi) anali atayamba kuika pulasitala, matailosi komanso kupenta.

April 15, 2015​—Nyumba Yogona B

Mashini okwezera zinthu m’mwamba anyamula anthu awiri ndipo akupaka pakhoma lakunja zinthu zoteteza kuti mphepo isamalowe m’nyumbayi. Ntchito imeneyi itenga miyezi pafupifupi iwiri panyumba iliyonse yogona.

April 27, 2015​—Maofesi Komanso Malo a Zinthu Zina

Anthu akumanga khoma lamiyala. Mbali ya nyumbayi idzakhala ya malo olandirirako katundu komanso ya madipatimenti ena.

April 30, 2015​—Ku Warwick

Munthu amene anamulemba ntchito akusintha chipangizo chotsekera komanso kutsegulira madzi m’nyanja ya Blue Lake. Achita zimenezi n’cholinga choti akadina kabatani kenakake nyanjayo iziphwera madzi akayamba kusefukira.