Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 1 (Kuyambira January Mpaka August 2015)

Zithunzi za Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 1 (Kuyambira January Mpaka August 2015)

A Mboni za Yehova ku Britain akusamutsa ofesi yawo ya nthambi ku Mill Hill, mumzinda wa London, kupita kumalo ena chakum’mawa pafupi ndi mzinda wa Chelmsford m’dera la Essex. Malowa ali pa mtundu wa makilomita 70 kuchokera ku Mill Hill. Kuyambira mu January kufika mu August, anthu anakonza malo ndiponso nyumba zimene adzagwiritse ntchito pa nthawi yomanga ofesiyi.

January 23, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Atalandira chilolezo kuchokera kwa akuluakulu a boma m’derali, anthu anagwetsa mitengo pokonzekera kuti amangepo. Anayesetsa kuti amalize ntchitoyi nyengo yoti mbalame ziyambe kumanga zisa m’mitengoyi isanafike. Zidutswa za mitengoyi zidzagwiritsidwa ntchito popanga tinjira todutsamo ndipo matabwa ake adzagwiritsidwa ntchito pomanga ofesiyi.

January 30, 2015​—Malo odyera pa nthawi yomanga

Munthu wogwira ntchito zamagetsi akulumikiza zofunikira kuti anthu ogwira ntchito yomanga azidzaonera kulambira kwa m’mawa ndiponso Phunziro la Nsanja ya Olonda la pa Beteli pamasikirini. Kale nyumbayi inali yogona anthu a pa ulendo koma panopa akuisintha kuti ikhale khitchini ndiponso malo odyera.

February 23, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Anthu akuika mpanda wamawaya womwe udzazungulire malo amene akumanga. Kuderali kuli tchire ndiye akuyesetsa kuti asasokoneze kwambiri moyo wa zinyama zakumeneko. Mwachitsanzo, asiya mpata wa masentimita 20 pansi pa mpandawu n’cholinga choti tizinyama tina timene timasewera pamalowa usiku tizitha kudutsa bwinobwino.

February 23, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Akukonza msewu wodutsa pakati pa malo ogona anthu omanga ndi malo amene adzamangepo ofesi ya nthambi.

March 5, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Chithunzi chojambulidwa kuchokera kum’mawa chosonyeza msewu umene akonzawo. Msewuwu ukukafika kumalo amene adzamangepo ofesi ya nthambi, omwe akuoneka m’mwamba mwa chithunzichi chakumanja. Nyumba zimene zikuoneka m’munsi akuzikonza kuti zikhale malo ogona a anthu ogwira ntchito yomanga. Adzaikanso nyumba zina zogona m’mabwalo apafupi ndi nyumbazi.

April 20, 2015​—Nyumba zogona anthu ogwira ntchito

Wina wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limodzi ndi wina wochokera kulikulu lathu anabwera kudzalimbikitsa anthu ogwira ntchito yomanga. Chakumapeto kwa mlunguwu kunali msonkhano wapadera umene unaulutsidwa m’Nyumba za Ufumu zonse za m’dziko la Britain ndi Ireland. Pamsonkhanowu, analengeza kuti akuluakulu a boma amumzinda wa Chelmsford anali atangowavomereza kumene kuti akhoza kuyamba kumanga ofesi yawo ya nthambi.

May 13, 2015​—Malo omwe akugwiritsa ntchito pa nthawi yomanga

Anthu akuika zinthu zoteteza mizu ya mitengo ikuluikulu iwiri yomwe ili kumbali zonse za njirayi. Njirayi imapita kumalo amene akumanga ofesi ya nthambi. Zimene akuikazi zithandiza kuti pazidutsa magalimoto olemera popanda kuwononga mizu ya mitengoyo.

May 21, 2015​—Nyumba zogona anthu ogwira ntchito

Akukumba ngalande zoti aikemo mapaipi opita kunyumba zogona anthu ogwira ntchito yomanga. Nyumba zonse zidzakhalapo 50 ndipo kumbuyo kwa anthuwa kukuoneka zina mwa nyumbazi.

June 16, 2015​—Nyumba zogona anthu ogwira ntchito

Munthu akuika mapaipi a madzi panyumba ina yogona.

June 16, 2015​—Nyumba zogona anthu ogwira ntchito

Chithunzi chojambulidwa kuchokera kum’mawa chomwe chikusonyeza nyumba zogona zimene zangoikidwa kumene. Chapansipa pakuoneka malo amene adzaike nyumba zinanso. Chakumanzere kuli nyumba yodyera ndiponso nyumba zina zomwe anthu ogwira ntchito yomanga azidzagwiritsa ntchito. Ofesi ya nthambi idzamangidwa pabwalo limene likuonekera chapakati kutsogoloko.

June 16, 2015​—Nyumba zogona anthu ogwira ntchito

Munthu akulumikiza mawaya a intaneti. Izi zinafunika mwamsanga kuti ntchito yomanga iziyenda bwino, kuti anthu azilankhulana ndi akumaofesi a mayiko ena komanso ndi akulikulu lathu lapadziko lonse.

July 6, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Munthu akugwiritsa ntchito GPS kuti ayeze malo amene adzakumbe maenje othandiza pofufuza zinthu zakale. Akatswiri ofukula zinthu zakale adzafufuza zinthuzi ntchito yomanga isanayambike. Ngakhale kuti mzinda wa Chelmsford ndi wakalekale ndipo kunkakhala Aroma, akatswiriwo sanapeze zinthu zakale m’maenje okwana 107 amene akumbidwa kale pamalowa.

July 6, 2015​—Malo omwe akugwiritsa ntchito pa nthawi yomanga

Akudula zinazake zoika pafelemu la chitseko. Nyumba zina zomwe zinalipo kale pamalowa zikukonzedwanso kuti zikhale malo ogwirira ntchito zosiyanasiyana komanso maofesi.

July 6, 2015​—Malo omwe akugwiritsa ntchito pa nthawi yomanga

Akuthira dothi m’chigalimoto kuti akakwirire maenje.

July 7, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Chithunzi chojambulidwa kuchokera kum’mwera kwa malowa, omwe ndi aakulu maekala 85. Pafupi ndi malowa pali msewu (sukuoneka pachithunzichi) womwe anthu amadutsa popita kunyanja, kumabwalo a ndege ndiponso kumzinda wa London.

July 23, 2015​—Malo a ofesi ya nthambi

Anthu olembedwa ntchito akuchotsa nyumba zakale kuti ntchito yomanga ofesi ya nthambi iyambike.

August 20, 2015​—Malo omwe akugwiritsa ntchito pa nthawi yomanga

Mashini okwezera zinthu m’mwamba olemera matani 60 akutsitsa kanyumba kenakake. Maziko oti adzaikepo tinyumba tina akuonekanso. Tinyumbati tigwiritsidwa ntchito monga maofesi a anthu ogwirizanitsa ntchito yomanga ofesi ya nthambi.