Pitani ku nkhani yake

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Wallkill Gawo 1 (Kuyambira July 2013 Mpaka October 2014)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Wallkill Gawo 1 (Kuyambira July 2013 Mpaka October 2014)

A Mboni za Yehova akugwira ntchito yowonjezera maofesi awo ndi nyumba zina ku Wallkill mumzinda wa New York. Zithunzizi zikusonyeza ntchito zina zomwe iwo anagwira kuyambira mu July 2013 mpaka October 2014. Iwo akonza zoti ntchitoyi idzakhale itatha pofika mu November 2015.

Mmene ku Wallkill kunkaonekera pofika pa October 21, 2013.

  1. Chigayo (chomwe anachisamutsa mu January 2014)

  2. Nyumba yochapira ndi kusitiramo zovala yomwe anawonjezera

  3. Chipinda chodyera

  4. Nyumba yogona E

  5. Holo ndi Maofesi

  6. Nyumba yosindikiziramo mabuku

  7. Mtsinje wa Shawangunk Kill

 

July 12, 2013—Kukulitsa nyumba yochapira ndi kusitiramo zovala

Galimoto ya makako ikunyamula makoma amene awapangira padera.

July 19, 2013—Nyumba yogona E

Ogwira ntchito akuika zipangizo (fiber-reinforced polymer strip) pa konkire zotetezera kuti kukachitika chivomezi nyumba isagwe. Zipangizozi zinali zazitali pafupifupi mamita 7,600.

August 5, 2013—Nyumba yogona E

Ogwira ntchito akukonza khoma la njerwa lomwe linawonongeka.

August 30, 2013—Kukulitsa nyumba yochapira ndi kusitiramo zovala

Ogwira ntchito akumangirira zitsulo m’malo amene padzaikidwe makina ogwiritsa ntchito pochapa ndi kusita.

September 17, 2013—Nyumba yogona E

Wogwira ntchito ali padenga ndipo akudula chilabala chotetezera kuti madzi asamalowe m’nyumba.

October 15, 2013—Nyumba yogona E

Ogwira ntchito akuonetsetsa kuti zipangizo zotetezera nyumba ku chivomezi zagwirana kwambiri ndi konkire. Akaona kuti malo ena sanagwirane bwino amawonjezerapo zipangizo zina.

November 15, 2013—Kukulitsa nyumba yochapira ndi kusitiramo zovala

Ogwira ntchito akuika fani yotulutsa mpweya wotentha.

December 9, 2013—Nyumba yogona E

Ogwira ntchito akumata timing’alu. Ntchito yonse yoika zinthu zotetezera nyumbayi ku chivomezi inatenga pafupifupi chaka ndi hafu.

December 11, 2013—Kukulitsa nyumba yochapira ndi kusitiramo zovala

Wogwira ntchito akukonza malo oti amangiriremo mapaipi okoka madzi ochokera m’munsi kupititsa m’mapaipi a m’mwamba.

January 10, 2014—Chigayo

Chigayo chimene akuchichotsa, chinakhala chikugwira ntchito kuyambira m’ma 1960 mpaka m’ma 2008. Koma chinasiya kugwira ntchito atasiya kuweta nkhuku, ng’ombe za mkaka ndi nkhumba ku Wallkill.

January 22, 2014—Holo komanso maofesi

Ogwira ntchito akuchotsa mipando pofuna kukonzanso holoyi.

January 29, 2014—Chigayo

Nkhokwezi ankazigwiritsa ntchito posungiramo chakudya cha ziweto.

March 3, 2014—Nyumba yosindikiziramo mabuku

Ogwira ntchito akukonza malo amene adzagwiritsidwe ntchito pophunzitsirako ntchito za manja.

July 4, 2014—Holo komanso maofesi

Wogwira ntchito akuwotcherera zitsulo zolimbitsira nyumba.

September 19, 2014—Chipinda chodyera (Nyumba yogona E)

Ogwira ntchito akuyala kapeti m’chipinda chimene ogwira ntchito ku Wallkill ankadyeramo chakudya.

September 22, 2014—Nyumba yogona E

Ntchito yomalizitsa khoma la kachipinda kozungulira mu nsanjika yoyamba.

September 24, 2014—Maofesi

Wogwira ntchito akumangirira zitsulo zolimbitsira makoma a njira yodutsamo chikepi chatsopano.

October 2, 2014—Chipinda chodyera (Nyumba yogona E)

Chipindachi achikulitsa ndipo tsopano mungakhale anthu okwana 1,980.

October 22, 2014—Holo komanso maofesi

Wogwira ntchito akukumba kuti athire konkire wolimbitsira zipirira zothandiza kuteteza nyumbayi ku chivomezi.