Pitani ku nkhani yake

Kusamutsa Likulu la Padziko Lonse Ndi Mbiri Yosaiwalika

Kusamutsa Likulu la Padziko Lonse Ndi Mbiri Yosaiwalika

Ntchito yomanga maofesi omwe akhale likulu la Mboni za Yehova la padziko lonse ili m’kati ku Warwick m’dera la New York. Ntchitoyi ikugwirika mwakathithi ndipo anthu ambiri amene akuigwira ndi ongodzipereka, ochokera m’madera osiyanasiyana m’dziko la United States. Anthuwa akugwira ntchitoyi mofunitsitsa, mwakhama komanso popanda malipiro aliwonse. Anthuwa sakunyinyirika chifukwa akuona kuti umenewu ndi mwayi wawo wotumikira Mulungu. Taonerani vidiyoyi kuti muone ntchito yaikulu imene gululi lagwira.