Magulu a anthu ongodzipereka anasonkhana kuti ayambe kumanga Nyumba za Ufumu ziwiri za Mboni za Yehova. Nyumba imodzi inamangidwa kudera lina la anthu olankhula Chifulenchi lomwe lili pa mtunda wa makilomita 25 kuchokera kugombe la Newfoundland, m’dziko la Canada. Nyumba ya Ufumu ina inamangidwa m’tauni ya Happy Valley-Goose Bay, m’dera la Labrador.