Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Nyumba za Ufumu Zakwana 1,000 Ndipo Zina Zikumangidwabe

Nyumba za Ufumu Zakwana 1,000 Ndipo Zina Zikumangidwabe

Pofika mu August 2013, a Mboni za Yehova ku Philippines anali atamanga Nyumba za Ufumu zokwana 1,000 m’dzikolo. Monga mmene zilili m’mayiko ambiri, mipingo yochuluka ya Mboni za Yehova ku Philippines siikanatha kupeza ndalama komanso amisiri oti n’kumanga Nyumba ya Ufumu yawo popanda kuthandizidwa. Kwa zaka zambiri, mipingo ina inkasonkhana m’nyumba za anthu ndipo ina inkasonkhana muzisakasa zomangidwa ndi msungwi.

Nyumba za Ufumu zochuluka ndiponso zabwino zinayamba kufunika kwambiri chifukwa anthu a Mboni za Yehova anayamba kuchuluka zedi ku Philippines komanso m’mayiko ena ambiri. Izi zinachititsa kuti mu 1999, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova liyambitse dongosolo lomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka. Potsatira dongosololi, anthu a Mboni a m’dzikolo amapereka ndalama zimene angathe ndipo ndalama zina zimachokera ku zopereka za anthu a m’mayiko ena. Kenako pamakonzedwa magulu a amisiri odziwa ntchito yomanga n’cholinga choti athandize mipingo kumanga Nyumba za Ufumu zawo. Ku Philippines, dongosolo limeneli linayamba mu November 2001.

Nyumba ya Ufumu ya nambala 1,000 inamangidwa pampingo winawake wa m’tauni ya Marilao m’boma la Bulacan. Bambo Iluminado, a mumpingo umenewu anati: “Ndinasangalala ndi ubale weniweni wachikhristu. Panali anthu ambiri omwe anabwera kudzagwira nawo ntchitoyi mongodzipereka. Pa gululi panali amuna ndi akazi, akuluakulu ndi ana omwe. Tonse tinkagwira ntchito mwakhama ngakhale kuti kunkakhala dzuwa loswa mtengo. Pamapeto pa tsiku lililonse tinkakhala otopa, komabe tinkakhala osangalala chifukwa tinkaona kuti ntchitoyo ikuyenda.”

Nawonso anthu omwe si a Mboni ankachita chidwi akaona mmene ntchitoyi inkayendera. Mwachitsanzo, mwini wa galimoto imene inkadzasiya mchenga ndi miyala pamalo pamene pankamangidwa Nyumba ya Ufumu anati: “Anthu inu mumagwira ntchito ngati nyerere. Pamalo ano pabwera anthu ambiri ndipo aliyense akugwira nawo ntchitoyi. Izitu n’zosowa kwabasi!”

Nyumba ya Ufumu

Nyumba ya Ufumu inatha kumangidwa pasanathe n’komwe milungu 6. Popeza Nyumba ya Ufumuyo inatha mwachangu, zinathandiza kuti anthu a mumpingowo asasokonezeke pa ntchito yawo yofunika kwambiri, yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.Mateyu 24:14.

Mayi winanso wa mumpingo womwewo, dzina lake Ellen, anati: “Nyumba ya Ufumu yathu yakale inali yaing’ono kwambiri, moti sitinkakwanamo. Anthu ambiri ankakhala panja. Koma Nyumba ya Ufumu yatsopanoyi ndi yokongola komanso yaikulu. Izi zithandiza kuti tonse tizipindula ndi malangizo olimbikitsa amene timapatsidwa pamisonkhano yathu.”

Onaninso

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA)

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Philippines

Onani zimene zinalimbikitsa anthu ena kuti asiye ntchito yawo komanso kugulitsa katundu wawo n’kukakhala kumadera akumidzi ku Philippines.