Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

M’nkhalango ya Amazon Munamangidwa Nyumba Yochitira Misonkhano

M’nkhalango ya Amazon Munamangidwa Nyumba Yochitira Misonkhano

Mkatikati mwa nkhalango ya Amazon, momwe mumagwa mvula kawirikawiri, munamangidwa Nyumba Yochitira Misonkhano ya Mboni za Yehova yokongola kwambiri. Malowa ndi aakulu maekala 128 ndipo ali chakumpoto kwa mzinda wa Manaus, m’dziko la Brazil. Mbali yaikulu ya malowa ndi yodzadza ndi mitengo yachilengedwe moti kumamveka phokoso losangalatsa la mbalame zosiyanasiyana. Koma n’chifukwa chiyani anamanga Nyumba Yochitira Misonkhano m’nkhalangoyi.

Mumzinda wa Manaus womwe uli pamtunda wa makilomita 1,450 kuchokera kumene mtsinje wa Amazon umakathira m’nyanja, muli anthu pafupifupi 2 miliyoni. Nyumba Yochitira Misonkhanoyi izigwiritsidwa ntchito ndi a Mboni pafupifupi 7,000 ochokera ku Manaus, ndi mizinda yoyandikana nayo. Izigwiritsidwanso ntchito ndi anthu ochokera m’mbali mwa mtsinje wa Amazon ndi mitsinje ina yomwe imakathera mumtsinje wa Amazon. Anthu amene aziyenda mtunda wautali kwambiri ndi amene azichokera m’tawuni yotchedwa São Gabriel da Cachoeira yomwe ili pa mtunda wa makilomita 800 kuchokera mumzinda wa Manaus. A Mboni ena ochokera m’tawuniyi amayenda paboti kwa masiku atatu kuti akachite msonkhano ku Nyumba Yochitira Misonkhanoyi.

Sinali ntchito yamasewera kumanga Nyumba Yochitira Misonkhano m’nkhalango ya Amazon. Panafunika kunyamula makontena 13 a zipangizo zomangira kuchokera kudoko la Santos, m’chigawo cha São Paulo, kudutsa m’mphepete mwa nyanja ya Brazil, kenako kuwoloka mtsinje wa Amazon n’kukafika nazo pamalo amene ankamanga nyumbayi.

Nyumbayi ndi ya nambala 27 pa Nyumba Zochitira Misonkhano zomwe zamangidwa ku Brazil. Inatseguliridwa pa May 4, 2014 ndipo anthu 1,956 anapezeka pamwambowu. Anthu ambiri anasangalala chifukwa kanali koyamba kuchitira msonkhano m’nyumba yotereyi.

Anthu amene anafika pamwambowu ankatha kuona munthu amene akukamba nkhani m’malo momangomva mawu. Kumeneku kunali kusintha kwakukulu chifukwa poyamba, misonkhano ikuluikulu inkachitikira pamalo oti anthu ambiri sankatha kuona wokamba nkhani komanso pulatifomu. Wa Mboni wina anati: “Ndakhala ndikupita kumisonkhano ikuluikulu kwa zaka zambiri. Komatu sindinaonereko sewero la m’Baibulo. Ndinkangomva mawu okha basi.” Panopa aliyense amatha kuona zimene zikuchitika kupulatifomu.