Pitani ku nkhani yake

Amapempha Kuti Agwire Ntchito Koma Safuna Kulipidwa

Amapempha Kuti Agwire Ntchito Koma Safuna Kulipidwa

Kwa zaka zoposa 28 zapitazi, anthu a Mboni za Yehova oposa 11,000 anasiya nyumba zawo ngakhalenso kusamuka m’mayiko awo n’kupita kukagwira ntchito yomanga nyumba zosiyanasiyana m’mayiko 120. Anthu onsewa amagwira ntchitoyi mongodzipereka ndipo amasangalala kwambiri.

Ambiri mwa anthuwa amalipira okha ndalama zoyendera popita kukagwira ntchitoyi. Ena anagwiritsa ntchito masiku awo a tchuthi kuti agwire nawo ntchitoyi ndipo ena amafika popempha tchuthi chopanda malipiro.

Iwo sachita zimenezi chifukwa chokakamizidwa, koma amadzipereka mwakufuna kwawo. Amadziwa kuti ntchito yawoyo imathandizira kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, yomwe ikuchitika padziko lonse lapansi, iziyenda bwino. (Mateyu 24:14) Anthuwa anamanga maofesi, nyumba zogona komanso nyumba zosindikizira Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo. A Mboni za Yehova amanganso Nyumba za Msonkhano zokwana anthu 10,000 ndiponso Nyumba za Ufumu zokwana anthu 300.

Ntchito yomangayi ikupitirirabe. Anthuwa akafika pamalo amene akufuna kumanga, ofesi ya nthambi ya m’dzikolo imawathandiza kuti apeze malo ogona, zakudya ndi zinthu zina zofunika pamoyo wawo. A Mboni amene amakhala kumalo amene kukuchitika ntchitoyo amathandiza kugwira ntchitoyo mosangalala.

Pofuna kuti ntchito yaikuluyi, yomwe ikuchitika padziko lonse, iziyenda bwino, m’chaka cha 1985, panakhazikitsidwa pulogalamu yapadera. Anthu a Mboni za Yehova a zaka zoyambira 19 mpaka 55, omwe ali ndi luso la zomangamanga, ndi amene amaloledwa kudzipereka n’kumagwira nawo ntchitoyi. Nthawi zambiri anthu amadzipereka kugwira nawo ntchitoyi kuyambira milungu iwiri mpaka miyezi itatu, ngakhale kuti nthawi zina munthu akhoza kugwira kwa chaka kapena kuposerapo.

Akazi a anthu ogwira ntchitoyi amaphunzitsidwa kugwira ntchito zing’onozing’ono monga kuika matailosi kapena kupenta. Ena amaphika zakudya kapena kusamalira m’zipinda zogona.

Ntchitoyi ikatha n’kubwerera kwawo, ena mwa anthu ogwira ntchito mongodziperekawa amalemba makalata oyamikira kuti anapatsidwa mwayi wogwira nawo ntchitoyi. Banja lina linalemba kuti: “Tikukuthokozani kwambiri chifukwa chotipatsa mwayi wogwira nawo ntchito ku ofesi ya mumzinda wa Budapest. Abale ndi alongo a m’dziko la Hungary ankatisonyeza chikondi komanso kuyamikira ntchito yathu. Titakhala nawo kwa mwezi umodzi, zinatiwawa kuwatsanzika, komabe sitikanachitira mwina. Tikukhulupirira kuti tidzapitanso kukagwira ntchito kumalowa m’miyezi ikubwerayi. Nthawi iliyonse imene tapatsidwa mwayi wogwira nawo ntchito yomanga, timachita kumva ngati tayamba moyo watsopano.”