A Mboni za Yehova ku Britain ayamba kumanga ofesi yawo yanthambi yatsopano kufupi ndi mzinda wa Chelmsford m’dera la Essex. M’derali muli zinthu zachilengedwe zambiri ndipo zimatetezedwa ndi lamulo lokhudza zinthu zachilengedwe la dziko la United Kingdom. (Wildlife and Countryside Act 1981) Kodi pa nthawi yomangayi a Mboni za Yehova akuchita chiyani potsatira lamuloli komanso poteteza zinthu zam’chilengedwezi?

Akukonza kanjira koti tinyama tizidutsa

Pofuna kunyengerera tinyama tinatake tofanana ndi makoswe kuti tichoke pamalo ogwirira ntchitowo, a Mboni anakhoma tinyumba toti tinyamati tizikhalamo pogwiritsa ntchito matabwa akale omwe anali pamalowo n’kukatiika patali ndi malo ogwirira ntchitowo. Anakonzanso kanjira koti tinyamati tizidutsa popita ku kankhalango komwe tinazolowera n’cholinga chofuna kuonetsetsa kuti asasokoneze tinyamati. A Mboniwa akuyesetsanso kusamalira maheji n’cholinga chofuna kuthandiza tinyamati. Chaka chilichonse nthawi yozizira ikafika, tinyamati timabisala m’maenje ndipo pa nthawiyi a Mboni amadulira mbali inayake ya mahejiwo. Zimenezi zimathandiza kuti tinyamati tisamasokonezeke, tizikhala motetezeka komanso tizipeza chakudya nthawi zonse.

Akuika tinyumba toti tinyama tizikhalamo

A Mboniwa akutetezanso njoka zomwe zimapezeka m’maudzu, abuluzi komanso abuluzi ang’onoang’ono ooneka ngati nyongolotsi. Akatswiri ena a zachilengedwe anachotsa tinyamati pansi pa matailosi a denga omwe tinkakhalamo mongoyembekezera ndipo anakatisiya ku malo ena otetezeka kutali ndi malo ogwirira ntchitowo. Malo atsopanowo muli malo ena omwe tinyamati timabisalamo m’nthawi yozizira komanso anatchinga ndi kampanda kuti zinyama zina zisamalowemo. Pofuna kuonetsetsa kuti tinyamati tisabwerere ku malo ogwirira ntchito komanso tisavulazidwe, a Mboni amakayendera mpandawu pafupipafupi.

Kanyama kofanana ndi khoswe (Hazel dormouse)

Pamalowa anaikapo mababu ochepetsa kuwala pofuna kupewa kusokoneza mileme ina yomwe imayendayenda usiku. Mababuwa amawala galimoto ikamadutsa ndipo zimenezi zimathandiza kuti pakhalebe m’dima wokwanira kuti milemeyi izionabe bwinobwino. Popeza nthawi zambiri mileme imasakasaka chakudya m’maheji pamalowa usiku, maheji ambiri sawachotsapo ndipo adzadzala maheji atsopano pamalo oposa makilomita awiri ndi hafu. Mitengo ina inachotsedwa pamalowa choncho ogwira ntchito pamalowa anakonza tinyumba tamatabwa kuti milemeyi isasowe malo okhala ngati zisa zake zitaonongedwa.

Akuika tinyumba ta mileme

A Mboniwa akuyesetsa kusamala mitengo yofunika kwambiri yomwe ndi yakale. Iwo amachita zimenezi poonetsetsa kuti galimoto zogwiritsidwa ntchito pomanga zikuyenda kutali ndi kumene mitsitsi ya mitengoyi ili. M’mitengo yakaleyi mumakhala tinyama tosiyanasiyana monga mitundu yambiri ya tizilombo, mileme ndiponso mbalame. Zonsezi zikusonyeza kuti a Mboni ndi otsimikiza mtima kupitiriza kuteteza zachilengedwe mumzinda wa Chelmsford.