Mkulu waboma atayendera ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu mumzinda wa Sydney ku Australia, ananena kuti: “Ntchito yomangayi ikuchitika mwadongosolo kwambiri komanso motsatira malangizo onse othandiza kupewa ngozi. Pa ntchito zonse za zomangamanga zimene ndakhala ndikuyendera, n’kale kwambiri pamene ndinapeza anthu otsatira malangizo onse opewera ngozi ngati amenewa.”

Mkulu wabomayo analemba kuti: “Zinthu zinkachitika mwadongosolo pamalo amene a Mboni ankamanga . . . Malo onse anali aukhondo kwambiri, sindinaone zipangizo zitasiyidwa m’tinjira, mawaya onse amagetsi anadutsa m’mwamba kuti asakole anthu komanso panali zozimitsira moto zambiri . . . Anthu onse amene anali pamalopo anali atavala zovala zodzitetezera monga malaya aatali manja, mathalauza, zipewa zachigoba ndiponso magalasi oteteza maso. . . . Anthu onse pamalowo ankachita zinthu mwadongosolo.

A Victor Otter, omwe ndi munthu wa Mboni yemwe amatsogolera pa ntchitoyo anati: “A Mboni amaona nkhani yokhudza kupewa ngozi kuti ndi yofunika kwambiri. Tikamayesetsa kupewa ngozi pogwira ntchito, timasonyeza kuti timaona moyo ngati mmene Mulungu amauonera komanso zimathandiza kuti tikhalebe ogwirizana ndi osangalala kwambiri. Madzulo ndikamabwerera kunyumba, nthawi zambiri ndimakhala ndi chimwemwe chodzadza tsaya.

Ntchito yomanga Nyumba ya Ufumuyo, yomwe mungakwane anthu 127, inatha mu April 2012.