Pitani ku nkhani yake

Anthu Omwe si Mboni Anasangalala Kugwira Ntchito Ndi Mboni za Yehova ku Warwick

Anthu Omwe si Mboni Anasangalala Kugwira Ntchito Ndi Mboni za Yehova ku Warwick

Anthu ambiri omwe ankaona pamene ntchito yomanga inkachitika ku Warwick, anadabwa kwambiri ndi mmene a Mboni ankadziperekera pogwira ntchitoyo. Mkulu wa kampani ina yomwe inaika zikepi pa malowa, anauza mmodzi mwa anthu amene ankagwira ntchitowo kuti: “Gulu lanu likuchita zinthu zogometsa. Anthu ambiri masiku ano alibe nthawi yoti agwire ntchito yongothandiza osalipidwa.”

Mkulu wa kampaniyu komanso anthu ena atamva koyamba kuti amene akumanga likulu la Mboni za Yehova ku Warwick ndi anthu ongodzipereka, anaganiza kuti anthuwo ndi a Mboni a m’deralo ndipo azigwira ntchitoyo Loweruka ndi Lamlungu basi. Koma iwo anadabwa atakumana ndi anthu amene anasiya ntchito zawo ndipo anachokera m’madera ambiri a m’dzikolo kudzagwira nawo ntchito yomangayo kwa miyezi ngakhalenso kwa zaka.

Pamene chaka cha 2015 chinkatha, a Mboni ongodzipereka okwana 23,000 anali atagwira ntchito ku Warwick limodzi ndi abale ndi alongo a m’banja la Beteli la ku United States. Kuonjezera pamenepo, anthu enanso omwe si a Mboni okwana 750 anathandiza pa ntchitoyi ndipo zimenezi zinachititsa kuti zinthu zonse zizichitika pa nthawi yake. Anthuwa anasangalala kwambiri kugwira ntchito ndi a Mboniwo.

Malo Abwino Kwambiri

Bwana wa kampani ina imene imapanga mawindo komanso zinthu zokhudza makoma analemba kuti: “Munthu aliyense wa pakampani yathu amene akugwira nawo ntchitoyi akudabwa kwambiri ndi mmene a Mboni akuchitira zinthu. Ambirife tikufuna kugwira nanu ntchito chifukwa cha zimenezi.”

Kampani ina inabweretsa antchito omwe anathandiza kumanga nyumba zogonamo zansanjika. Ntchito imene anthuwa ankagwira itatha, anthu atatu a ku kampaniyo ananena kuti akufunitsitsa kuti apitirize kugwirabe ntchito pamalowo. Choncho iwo anasiya ntchito ku kampaniyo ndipo anayamba ntchito ku kampani ina imene inkapitirizabe kugwira ntchito.

Makhalidwe abwino amene a Mboni anasonyeza anathandiza kwambiri anthu ena amene ankagwira ntchito ndi a Mboniwo. Bambo wina ankagwira ntchito ndi kampani imene inamanga maziko a nyumbazi. Atagwira ntchito ku Warwick kwa miyezi yochepa, mkazi wake anazindikira kuti mwamuna wake wasintha kwambiri mmene akuyankhulira komanso mmene akuchitira zinthu ndi ena. Ndi chisangalalo, ananena kuti: “Akungokhala ngati si mwamuna wanga yemwe uja.”

“Akazi Omwe Ndi a Mboni Adzabwera Kudzagwira Ntchito”

Ambiri mwa a Mboni omwe ankagwira ntchito ku Warwick anali akazi. Iwo ankagwira ntchito zosiyanasiyana monga kuyendetsa mabasi, kukonza m’nyumba, usekilitale, kulozera oyendetsa galimoto koti alowere, kuyendetsa zimagiledala, kulumikiza mawaya, kukutira mapaipi, kumangirira makoma a matabwa, kuika mapaipi a madzi komanso kuthira konkire. Ankagwiradi ntchito mwakhama.

Munthu wina yemwe si wa Mboni ndipo ankagwira ntchito yokhoma denga la nyumbazo, anaona kuti a Mboni apabanja akamatsika basi ankagwirana manja ndi mkazi kapena mwamuna wawo popita ku malo awo ogwirira ntchito. Zimenezi zinamukhudza kwambiri. Komanso anaona kuti akazi ankagwira ntchito mwakhama kwambiri. Munthuyo ananena kuti: “Poyamba munthu akhoza kuganiza kuti akaziwo akungoperekeza amuna awo. Koma akaziwo akayamba kugwira ntchito, amachita khama. Ndakhala ndikugwira ntchito ya zomangamanga mu mzinda wonse wa New York, koma sindinaonepo zinthu ngati zimenezi.”

Mu nyengo yozizira ya mu 2014 ndi 2015 anthu ankangolakalaka atakhala panyumba osapita kukagwira ntchito chifukwa kunja kunkazizira kwambiri. Bambo Jeremy, omwe ndi a Mboni ndipo ankayang’anira ntchito yomangayi, ananena kuti: “Pa masiku ena amene kunkazizira kwambiri, woyang’anira anthu ogwira ntchito pa kampani ina imene inkamanga maziko a nyumbazo ankandifunsa kuti, ‘Kodi akazi nawonso adzabwera kudzagwira ntchito mawa?’

Ndinkamuyankha kuti: ‘Inde.’

Ankandifunsanso kuti: ‘Ngakhale amene amaima kunja n’kumathandiza oyendetsa magalimoto aja?’

Ndinkamuuza kuti: ‘Inde.’

Kenako woyang’anirayo ananena kuti akamva zimenezi, ankauza amuna amene ankawayang’anira kuti tsiku lotsatira adzabwere kudzagwira ntchito chifukwa ngakhale akazi omwe ndi a Mboni adzabwera kudzagwira ntchito.”

Oyendetsa Mabasi Ankasangalala Ndi Ntchito Yawo

Oyendetsa mabasi okwana 35 anapangidwa hayala kuti azinyamula ogwira ntchito ku Warwick popita ku malo antchito kenako n’kumakawasiya kumene ankagona.

Tsiku lina asananyamuke, dalaivala wina anaimirira n’kuyang’ana anthu omwe anali m’basimo kenako ananena kuti: “Ndasangalala kwambiri kukuyendetsani inu a Mboni. Chonde alembereni uthenga abwana anga kuti ndipitirizebe kukunyamulani. Ndaphunzira zinthu zambiri zokhudza Baibulo kuchokera kwa inu. Ndisanakumane nanu, sindinkadziwa dzina la Mulungu komanso zoti kudzakhala paradaiso. Panopo sindikuopanso imfa. Kugwira nanu ntchito kwandisangalatsa kwambiri. Tikaonana ku Nyumba ya Ufumu pa tsiku lotsatira limene sindidzabwera ku ntchito.”

Damiana, yemwe ndi mmodzi wa a Mboni amene anagwira nawo ntchito ku Warwick ananena kuti: “Tsiku lina titakwera basi, dalaivala wathu ananena kuti pali zinazake zimene akufuna kutiuza. Iye ananena kuti wakhala akuyendetsa a Mboni okwana 4,000, pokawatenga komanso kukawasiya m’malo osiyanasiyana omwe ankakhala ku New York. Iye ananenanso kuti: ‘Munthu aliyense amalakwitsa, koma anthu inu mumakambirana ngati pali kusemphana maganizo ndipo mumagwira ntchito mogwirizana. Zimenezi n’zosangalatsa kwambiri.’ Iye ananenanso kuti ankasangalala kucheza nafe.

Dalaivalayo atamaliza kuyankhula, mmodzi mwa a Mboni omwe anali m’basimo anamufunsa kuti, ‘Kodi mumasangalalanso tikamaimba nyimbo?’

Iye anayankha kwinaku akusekerera ndipo anati, ‘Inde. Moti tiyeni tiyambire kuimba nyimbo nambala 134.’” *

^ ndime 22 Nyimbo nambala 134 ili m’buku la nyimbo lakuti Imbirani Yehova ndipo ili ndi mutu wakuti “Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano.” Nyimboyi imafotokoza chisangalalo chimene anthu amene adzakhale m’dziko latsopano la Mulungu adzakhale nacho.