Pitani ku nkhani yake

Mwambo wa Omaliza Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Giliyadi ya Nambala 138

Mwambo wa Omaliza Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Giliyadi ya Nambala 138

Pa 14 March, 2015, anthu anachita mwambo wa omaliza Sukulu ya Giliyadi ya nambala 138. Mwambowu unachitikira kulikulu la maphunziro la Mboni za Yehova ku Patterson m’dziko la United States. Anthu oposa 14,000 anamvetsera mwambowu, kuphatikizapo amene anaonera pa vidiyo kumalo ena. Msonkhanowu unayamba ndi nyimbo zomvetsera ndipo 4 zinali zatsopano. Kenako onse anaimbira limodzi nyimbo zatsopanozi. *

M’bale Geoffrey Jackson, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene anali tcheyamani. M’mawu ake oyamba, analimbikitsa omaliza sukuluwa kuti azigwiritsa ntchito zimene aphunzira pothandiza ena.—2 Timoteyo 2:2.

M’bale Jackson anafotokoza mmene chitsanzo cha Mose chingawathandizire. Iye ananena kuti poyamba hema wa Mose ankagwiritsidwa ntchito ngati malo amene Aisiraeli ankalambirira Yehova. Koma chihema chopatulika chitamangidwa, iwo anayamba kuchigwiritsa ntchito monga likulu la kulambira koona. Zikuoneka kuti Mose sankaloledwa kulowa Malo Oyera Koposa a m’chihemacho. Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaloledwa kuchita zimenezi. Komabe Baibulo silinena kuti Mose ankadandaula nazo. M’malomwake, Aroni atakhala mkulu wa ansembe Mose ankamulemekeza ndiponso kumuthandiza. (Ekisodo 33:7-11; 40:34, 35) Ndiyeno, M’bale Jackson anafunsa kuti kodi mungaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Mose chimenechi? Kenako anati, nanunso “muyenera kusangalala ndi mwayi uliwonse wa utumiki umene muli nawo koma musamadandaule ngati zinthu zingasinthe.”

“Kodi Mudzachita Mantha ndi Phokoso la Tsamba?” Uwu unali mutu wa nkhani imene inakambidwa ndi M’bale Kenneth Flodin, yemwe amathandiza m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira. Iye ananena kuti ophunzirawo akhoza kukumana ndi mavuto monga kuzunzidwa kapena kupatsidwa utumiki ungaoneke wovuta. M’baleyu anagwiritsa ntchito mawu a m’lemba la Levitiko 26:36 polimbikitsa ophunzirawo. Anawauza kuti asamaone kuti mavuto awo ndi ovuta kuwagonjetsa koma azingowaona ngati tsamba lofota basi. M’bale Flodin anawalimbikitsanso pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mtumwi Paulo amene anatha kupirira mavuto ambiri chifukwa chodalira Yehova.—2 Akorinto 1:8, 10.

“Kodi Mukuyembekezera Chiyani?” M’bale Mark Sanderson, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anakamba nkhani imeneyi. Iye anafotokoza mfundo ya m’lemba la Miyambo 13:12 limene limati: “Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.” M’nkhaniyi ananena kuti n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sakhala osangalala chifukwa amayembekezera zinthu zomwe sizikuchitika, monga kupeza chuma kapena kutchuka.

M’nthawi ya Yesu, ena ankayembekezera zinthu zolakwika zokhudza Yohane M’batizi. (Luka 7:24-28) N’kutheka kuti ena ankayembekezera kuti iye akhala katswiri wa nzeru za anthu n’kumawasangalatsa ndi mfundo zozama. Ngati zinali choncho, ayenera kuti anakhumudwa naye chifukwa ankangophunzitsa uthenga wabwino wosavuta kumva. N’kuthekanso kuti ena ankayembekezera kuti Yohaneyo akhala munthu wooneka bwino kwambiri. Koma iye ankangovala zovala za anthu osauka. Komabe anthu amene ankayembekezera kuti Yohane akhala mneneri sanakhumudwe chifukwa analidi mneneri komanso ndi amene anakonzera njira Mesiya.—Yohane 1:29.

Ndiyeno M’bale Sanderson analimbikitsa ophunzirawo kuti aziyembekezera zinthu zoyenera. M’malo mofunafuna kuti akhale otchuka kapena kuti azipatsidwa zinthu zapadera kumene akupita, ayenera kukhala ndi cholinga choti azithandiza ena ndi zimene aphunzira. Iwo angachite zimenezi akamalimbikitsa ena ndi zimene aphunzira ku Giliyadi, akamakonda kwambiri abale ndi alongo komanso akamawathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. M’bale Sanderson anawauzanso kuti: “Yesetsani kuthandiza abale ndi alongo anu modzichepetsa komanso kuchita zonse zimene mungathe potumikira Yehova. Mukamachita zimenezi ndiye kuti simudzakhumudwa ngakhale pang’ono.”

“Dyetsani Anjala.” Umenewu unali mutu wa nkhani ya M’bale James Cauthon, yemwenso ndi mlangizi m’Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu. M’bale Cauthon ananena kuti aliyense amafunitsitsa kuti ena azimukonda, kumuyamikira ndiponso kumulemekeza. Tinganene kuti amakhala ndi njala ya zinthu zimenezi. Nayenso Yesu ankafuna zinthuzi ndipo Yehova anamuchitira zimenezi pamene anamulankhula mwachikondi pa nthawi imene ankabatizidwa.—Mateyu 3:16, 17.

Yehova anatipatsa mphamvu kuti tizilimbikitsa ena ndi mawu athu ndipo amayembekezera kuti tizichita zimenezi. (Miyambo 3:27) M’bale Cauthon anati: “Yesetsani kuona zabwino zimene anthu ena akuchita ndipo muziwayamikira.” Tikamayamikira Akhristu anzathu, timawathandiza kudziwa kuti zimene akuchita sizikupita pachabe.

“Anadzipereka Mpaka pa Mapeto.” M’bale Mark Noumair, yemwe amathandiza m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa, ndi amene anakamba nkhani imeneyi. M’bale Noumair anagwiritsa ntchito chitsanzo cha mtumwi Paulo polimbikitsa ophunzirawo kuti azichita zonse zimene angathe potumikira Yehova. Ananenanso kuti mofanana ndi Paulo, iwo adzakhala osangalala kwambiri akamadzipereka pothandiza ena.—Afilipi 2:17, 18.

Paulo sanabwerere m’mbuyo ngakhale pa nthawi imene anakumana ndi mavuto. Iye anapitiriza kudzipereka kwambiri mpaka imfa yake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.” (2 Timoteyo 4:6, 7) M’bale Noumair analimbikitsa ophunzirawo kuti azitsatira chitsanzo cha Paulo pogwira ntchito ya Ufumu mokhulupirika.

Zokumana nazo mu utumiki. M’bale Michael Burnett, yemwenso ndi mlangizi wa Giliyadi, ndi amene anachititsa mbali imeneyi. Ena mwa ophunzirawa anachita zitsanzo za zimene anakumana nazo mu utumiki pamene anali pa sukuluyi.

Zinthu zinkawayendera bwino mu utumiki chifukwa chakuti ankakhala tcheru kwambiri kuti apeze mipata yolalikira ndiponso ankayesetsa kulankhula kwa anthu m’chilankhulo chawo. Mwachitsanzo, m’bale wina anamva kuti kumene ankafuna kukalalikira kuli anthu ambiri olankhula Chisipanishi. Choncho tsiku lina asanapite mu utumiki anaphunzira mawu angapo achisipanishi pogwiritsa ntchito Pulogalamu Yophunzirira Chinenero ya JW. Tsiku lomwelo anakumana ndi munthu wina wolankhula Chisipanishi. Ndiyeno m’baleyu anagwiritsa ntchito mawu ochepa amene anaphunzira aja kuti akambirane naye. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi munthuyo limodzi ndi anthu ena 4 a m’banja lake.

Kucheza ndi ophunzira. Kenako M’bale William Turner, Jr., yemwe amathandiza m’Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira anacheza ndi ophunzira 4. Iye anawafunsa zomwe anakumana nazo asanafike ku Giliyadi ndiponso zokhudza zimene anaphunzira pa sukuluyi.

Ophunzirawa anafotokoza mfundo za m’sukuluyi zimene zinawalimbikitsa kwambiri. Mwachitsanzo, wina anafotokoza zimene anaphunzira m’chaputala 10 cha Luka. Iye ananena kuti Yesu anatumiza ophunzira ake 70 kukalalikira ndipo iwo anasangalala kwambiri ndi zimene anakumana nazo. Nayenso Yesu anasangalala, koma anawauza kuti azisangalala makamaka chifukwa chodziwa kuti Yehova akuyamikira zimene akuchita. Izi zikusonyeza kuti timakhala osangalala chifukwa choti Yehova akusangalala nafe osati chifukwa cha mmene zinthu zikuyendera pa moyo.

M’bale Turner ananena mawu a pa Afilipi 1:6 pouza ophunzirawo kuti Yehova wayamba kuwagwiritsa ntchito pa zinthu zabwino ndipo adzapitiriza kuchita zimenezi.

“Musasiye Kuyang’ana Yehova.” M’bale Samuel Herd, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anakamba nkhani yaikuluyi. Iye anafunsa kuti kodi zingatheke bwanji kuyang’ana Yehova popeza kuti sitingamuone?

Choyamba, tingachite zimenezi poyang’ana zinthu zimene Yehova analenga zomwe zimatiphunzitsa za iye. Yehova ‘waunikiranso maso a mtima wathu.’ (Aefeso 1:18) Tikutero chifukwa chakuti tikamawerenga Baibulo timayamba kumudziwa bwino ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.

Ananenanso kuti tiyenera kuwerenga kwambiri mabuku a Uthenga Wabwino chifukwa ndi omwe amafotokoza mawu ndiponso zochita za Mwana wa Mulungu. Tikamudziwa bwino Mwanayo, timadziwanso bwino Yehova. Tikutero chifukwa Yesu anati: “Amene waona ine waonanso Atate.”​—Yohane 14:9.

M’bale Herd ananena kuti si bwino kungodziwa Yesu komanso Yehova koma tiyenera kutsatiranso chitsanzo chawo. Mwachitsanzo, Yesu anadzipereka kuti athandize anthu ena. Ifenso tiyenera kudzipereka kuti tithandize ena ndi zimene taphunzira.

Koma kodi kuyang’ana Yehova n’kothandiza bwanji? Kumatithandiza kukhala ndi maganizo omwe wolemba masalimo anali nawo. Iye anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.”​—Salimo 16:8.

Mawu omaliza. Ophunzirawo atalandira masatifiketi, wophunzira wina anawerenga kalata yochokera kwa ophunzira onse yothokoza kwambiri mwayi wolowa nawo m’sukuluyi. Kenako M’bale Jackson anawauza kuti asamaone kuti nthawi zonse ayenera kuphunzitsa anthu mfundo zatsopano kapena zozama kwambiri. Koma nthawi zambiri mfundo zimene azikaphunzitsa zidzakhala zongokumbutsa abale ndi alongo zinthu zomwe akuzidziwa kale. M’bale Jackson ananenanso kuti kudzichepetsa n’kofunika kwambiri. Iye anati ophunzirawo sayenera kugometsa anthu ndi zimene anaphunzira ku sukuluyi, koma ayenera kuwathandiza kuti adziwe zimene Baibulo kapena mabuku athu ofotokoza Baibulo amaphunzitsa. Izi zingathandize kuti asamakhumudwitse anthu amene sangakhale ndi mwayi wopita ku Sukulu ya Giliyadi. M’malomwake, azikalimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito bwino zinthu zimene ali nazo zomwe zimawathandiza kutumikira Yehova. Onse amene anapezeka pamsonkhanowu analimbikitsidwa kwambiri ndipo anachoka ali ofunitsitsa kukatumikira abale ndi alongo awo.

^ ndime 2 Anthu analandiriratu nyimbo zatsopano zomwe zinaimbidwa pamsonkhanowu.

Anthu analandiriratu nyimbo zatsopano zomwe zinaimbidwa pamsonkhanowu.

Mayiko ena sanasonyezedwe pamapu.

Mayina ena a ophunzira sanalembedwe.