Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 136 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 136 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Ophunzira a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo a kalasi nambala 136, anamaliza maphunziro awo Loweruka pa March 8, 2014. Anthu a Mboni za Yehova omwe amaitanidwa kudzaphunzira kusukuluyi, ndi amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali. Kusukuluyi amaphunzira mwakathithi kwa miyezi 5, ndipo zimenezi zimawathandiza kuti azigwira ntchito yolalikira mwaluso komanso azithandiza a Mboni anzawo kuti chikhulupiriro chawo chilimbe kwambiri. Pa tsiku limene ophunzira a kalasi nambala 136 imeneyi anamaliza maphunziro awo, panachitika mwambo wapadera ndipo anthu amene anamvetsera pulogalamu ya mwambowu anali okwana 11,548. Mwambowu unachitikira ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, m’dera la New York, ndipo anthu ena ankaonera mwambowu pa vidiyo ya pa Intaneti m’madera osiyanasiyana a m’dziko la United States komanso m’mayiko ngati Canada, Jamaica ndi Puerto Rico.

“Khalani ndi Maganizo Amenewa.” A David Splane, omwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene anali tcheyamani pa mwambowu. Iwo anakamba nkhani yoyambirira papulogalamuyi, yomwe inachokera pa mawu a pa Afilipi 2:5-7, omwe amati: “Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo.” Pamene Yesu anali padziko lapansi, sankafuna udindo uliwonse koma ankagwira mwakhama ntchito imene Mulungu anamupatsa.

Mwachitsanzo, pa nthawi imene Yesu ankayesedwa ndi Mdyerekezi, iye anakana mayesero onsewo ponena mawu akuti “Malemba amati.” Mawu amenewa Yesu anawatenga mu uthenga umene Mose anauza mtundu wa Isiraeli. (Mateyu 4:4, 7, 10; Deuteronomo 6:13, 16; 8:3) Ngakhale kuti Yesu akanatha kulankhula pogwiritsa ntchito mphamvu zake monga Mwana wodzozedwa wa Mulungu, iye anadzichepetsa n’kugwiritsa ntchito mawu amene Mose analemba. Ifenso tizichita zinthu mosonyeza kuti tikuzindikira zimene ena achita kapena zimene angachite, ndipo tisamaumire kuwayamikira.

M’bale Splane anatsindikanso mfundo yakuti Yesu anasonyeza kuti anali woganiza bwino mpaka kumapeto kwa moyo wake pano padziko lapansi. Popemphera, Yesu anati: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa. Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.” (Yohane 17:4, 5) Apa Yesu sanapemphe kuti apatsidwe udindo woonjezera. M’malomwake, anangopempha kuti akabwerera kumwambako, apatsidwe malo amene anali nawo poyamba, kapena kuti ‘ntchito imene ankagwira’ asanabwere padziko lapansili. Nawonso anthu amene anamaliza maphunziro awo ku Giliyadi analimbikitsidwa kuti atsanzire Yesu. M’malo mofuna udindo, analimbikitsidwa kuti azigwira ndi mtima wonse ntchito iliyonse imene angapatsidwe, ngakhale zitakhala kuti sanapatsidwe udindo uliwonse akabwerera kwawo.

“Dziperekeni ndi Mtima Wonse ndipo Simudzanong’oneza Bondo.” A William Malenfant, omwe amathandizira m’komiti ya Bungwe Lolamulira yoona za ntchito yophunzitsa, analimbikitsa ophunzirawo kuti azitsanzira mtima wodzimana umene mtumwi Paulo anali nawo. Paulo sankadandaula ndi zimene anasiya kuti azitumikira Mulungu nthawi zonse. Mtumwiyu anati: “Chinthu chimodzi ndimachita: kuiwala zambuyo ndikuthamangira molimba zinthu zimene ziri m’tsogolo, ndiri kuthamangira kokathera kuti ndikalandire mphotho.”—Afilipi 3:13, 14, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Ngati ophunzirawo atapewa kudandaula zinthu zimene anasiya kuti azitumikira Mulungu nthawi zonse, ndiye kuti angakhale akutsanzira atumiki okhulupirika a Mulungu, amene anakhalapo kalekale komanso a m’nthawi yathu ino. Pokamba nkhani yake, M’bale Malenfant anatchula mawu amene analankhulidwa ndi mayi Clara Gerber Moyer, omwe anatumikira Yehova kuyambira ali mwana. Mayiwa analemba kuti: “Ndatumikira Mulungu kwa zaka zoposa 80 ndipo sindikudandaula ngakhale pang’ono. Ndikuona kuti umenewu ndi mwayi waukulu zedi! Zikanakhala kuti n’zotheka kuti ndikhalenso kamwana, ndikanasankhabe kutumikira Mulungu nthawi zonse ngati mmene ndikuchitira panopa.”

“Kulalikira Uthenga wa Ufumu ndi Angelo Komanso Ngati Angelo.” Bambo Gerrit Lösch, omwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anathandiza ophunzirawo kumvetsa mfundo yoti aliyense amene akugwira ntchito yolalikira amakhala ndi maudindo awiri apadera. Choyamba, iwo akamauza ena uthenga wabwino wa Ufumu, amakhala akutumikira Mulungu ngati angelo ake. Izi zili choncho chifukwa mawu achiheberi komanso achigiriki amene m’Baibulo anawamasulira kuti “mngelo,” angamasuliridwenso kuti “wotumidwa kukapereka uthenga.” Chachiwiri, ophunzirawo akamalalikira uthenga wabwino, amatsogoleredwa ndi angelo akumwamba, ngati mmene zinalili ndi wophunzira wina wa Yesu, dzina lake Filipo.Machitidwe 8:26-35.

Kenako M’bale Lösch anafotokoza nkhani zosiyanasiyana zimene zinachitikira anthu ena a Mboni za Yehova pogwira ntchito yawo yolalikira. Mwachitsanzo, wa Mboni wina wa ku Mexico, dzina lake Gabino, yemwe akamalalikira amakonda kupereka odi kamodzi kapena kawiri panyumba iliyonse imene wafika, atafika panyumba ina anapereka odi mpaka maulendo 4, ndipo bambo wapanyumbapo anayankha. Bamboyo anamuuza Gabino kuti anali atatsala pang’ono kudzipha. Iye anati: “Pamene umapereka odi ka chi 4, ndinali nditakoloweka chingwe m’khosimu, moti ndangochichotsa n’cholinga choti ndidzaone kaye alendonu. Zikomo chifukwa chosatopa n’kupereka odi. Ukanangopereka odi kamodzi kapena kawiri kokha, ndiye kuti ine ndikanadzipha basi.”

Si zinthu zonse ngati zimenezi zomwe zimangochitika mwamwayi. M’malomwake, nkhani zoterezi zimapereka umboni wakuti angelo a Mulungu amatsogolera anthu omwe akugwira ntchito yolalikira.—Chivumbulutso 14:6.

“Munthu Wolemezeka Adzadalitsidwa.” Nkhani ya mutu umenewu inakambidwa ndi M’bale Michael Burnett, yemwe ndi mphunzitsi wa kusukulu ya Giliyadi. M’nkhaniyi, m’baleyu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Yabezi, wafuko la Yuda, amene “anali wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake.” Yabezi anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndipo dzanja lanu likhale ndi ine, [komanso munditeteze ku tsoka].”1 Mbiri 4:9, 10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Ophunzirawa angatsanzire chitsanzo cha Yebezi ngati popemphera atamatchula mosapita m’mbali zimene akufuna, makamaka popempha Mulungu kuti awathandize kugwiritsa ntchito zimene aphunzira kusukulu ya Giliyadi. Angapemphenso Mulungu kuti awateteze ku tsoka, osati kuti awatchingire kuti asakumane ndi tsoka lililonse koma kuti awathandize kupirira akakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mulungu anayankha pemphero la Yabezi, ndipo adzachita chimodzimodzi ndi mapemphero a ophunzira a ku Giliyadiwo.

“Moto Wanu Usazime.” A Mark Noumair, omwe ndi mphunzitsi wa sukulu ya Giliyadi komanso amathandizira mu komiti ya Bungwe Lolamulira yoona za ntchito yophunzitsa, anakamba nkhani yochokera pa 1 Atesalonika 5:16-19. Kuti moto uyake, iwo anafotokoza kuti pamafunika zinthu ngati nkhuni, mpweya komanso kutentha. Choncho ophunzirawo angagwiritse ntchito njira zitatu zotsatirazi kuti nthawi zonse azikasangalala ndi utumiki.

Chinthu choyamba ‘n’kukhala okondwera nthawi zonse.’ (1 Atesalonika 5:16) Kukhala okondwera, kapena kuti kukhala ndi chimwemwe kuli ngati nkhuni zomwe zimathandiza kuti moti uziyaka. Nachonso chimwemwe chingathandize ophunzirawo kuti azitumikira Mulungu mwakhama poganizira madalitso amene munthu amakhala nawo ngati munthuyo ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Chinthu chachiwiri ‘n’kupemphera mosalekeza.’ (1 Atesalonika 5:17) Pemphero lili ngati mpweya umene umathandiza kuti moto usazime. Ifenso tikamapemphera kwa Mulungu, tizitenga nthawi ndithu, ndipo tizimuuza zonse zimene zili mumtima mwathu. Chinthu chachitatu ‘n’kuyamika pa chilichonse.’ (1 Atesalonika 5:18) Mtima woyamikira umatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso ndi abale athu. Choncho M’bale Noumair analimbikitsa ophunzirawo kuti: “Mupitirize kukhala ndi mtima woyamikira, osati mtima wosayamika wokonda kupezera ena zifukwa.”

“Inuyo Pamodzi ndi Zinthu za Mlengalenga Tamandani Yehova.” M’bale Sam Roberson, yemwe ndi mphunzitsi wa kusukulu zophunzitsa Baibulo, anayamba nkhani yake ndi mawu ochokera m’Baibulo osonyeza kuti dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zimatamanda Yehova. (Salimo 19:1; 89:37; 148:3) M’baleyu anati ophunzirawo ali ndi mwayi wotamanda Yehova. Kenako anaitana ophunzira ena kuti achite zitsanzo zoyerekezera zinthu zimene anakumana nazo pamene amagwira ntchito yolalikira pa nthawi yomwe anali kusukuluyi. Mwachitsanzo, wophunzira wina yemwe ankayendetsa galimoto anayamikira munthu yemwe amayenda panjinga ya olumala chifukwa choti munthuyo anathokoza wophunzirayo ataimika galimoto pomupatsa mpata woti adutse msewu. Kenako anthu awiriwo anayamba kucheza, ndipo munthuyo anavomera zoti ayambe kuphunzira Baibulo popanda kupereka ndalama iliyonse. Wophunzira wa ku Giliyadiyo anaphunzira ndi munthu woyenda panjinga uja kwa milungu ingapo, ndipo pa nthawi yonseyi ankathanso kulalikira anthu osiyanasiyana omwe ankabwera kudzaona munthuyo. Pamapeto pake, anthu 7 anayamba kuphunzira Baibulo.

“Pitirizani Kuphunzira Mawu a Mulungu Kuti Mukhalebe ndi Mphamvu.” M’bale Donald Gordon, yemwe amathandizira mu komiti ya Bungwe Lolamulira yoona za ntchito yofalitsa mabuku, anafunsa mafunso mabanja awiri a m’gulu la ophunzirawa. M’bale m’modzi pa anthu ofunsidwa mafunsowo ananena kuti pa nthawi yonse imene maphunziro awo anali mkati kusukuluyi, anakambirana lemba la Aefeso 3:16-20 mobwerezabwereza. Zimenezi zinathandiza ophunzirawo kuti ‘akhale amphamvu’ mwa kuyesetsa kukhala odzichepetsa ndi ochezeka komanso zinawathandiza kuti azikumbukira zoti Yehova adakali ndi ntchito yaikulu imene akufuna kuti wa Mboni aliyense aigwire. Mlongo wina amene anali m’gulu la anthu ofunsidwa mafunsowo anasangalala ndi mmene mphunzitsi wina wa ku Giliyadi anawalimbikitsira. Mphunzitsiyo anawachenjeza kuti asakhale ngati chinsomba chimene chili m’madzi m’kabeseni momwe sichingathe kukula. M’malomwake, anawalimbikitsa kuti akhale ngati kansomba kamene kali m’nyanja yaikulu. Mlongoyo anati: “Pa zimene mphunzitsiyu ananena ndaphunzirapo kuti ndikakhala wodzichepetsa m’gulu la Yehova, Yehovayo adzandithandiza kuti ndikule mwauzimu.”

“Yehova Adzakukumbukirani.” A Mark Sanderson, omwe ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yaikulu pamwambowu ndipo inachokera pa pemphero la Nehemiya, lakuti: “Mulungu wanga, mundikumbukire.” (Nehemiya 5:19; 13:31) Mawu amenewa sakutanthauza kuti Nehemiya ankaopa kuti mwina Yehova Mulungu angamuiwale kapenanso angaiwale ntchito imene ankagwira pomutumikira. M’malomwake, iye ankapempha Mulungu kuti apitirize kumukonda komanso kumudalitsa.

Nawonso ophunzirawo sangakayikire zoti Yehova adzawakumbukira ngati iwowo akugwiritsa ntchito mfundo zonse zimene aphunzira ku Giliyadi. Mwachitsanzo, iwo akufunika kuti azitumikira Mulungu ndi mtima wonse chifukwa choti amamukonda kuchokera pansi pa mtima. (Maliko 12:30) Abulahamu ankakonda Yehova Mulungu ndi mtima wake wonse, ndipo Mulunguyo anamukumbukira. Ngakhale kuti panapita zaka pafupifupi 1,000 Abulahamu atamwalira, Mulungu ananena kuti Abulahamu anali ‘bwenzi lake.’Yesaya 41:8.

Kenako M’bale Sanderson analimbikitsa ophunzirawo kuti azikonda anthu ena, makamaka abale ndi alongo awo achikhristu. (Maliko 12:31) Mofanana ndi Msamariya wachifundo yemwe “anakonda munthu amene anakumana ndi achifwamba,” ophunzirawo anauzidwa kuti aziyesetsa kuthandiza anthu amene akufunikira thandizo. (Luka 10:36) Pofuna kuti mfundoyi imveke bwino, a Sanderson anagwiritsa ntchito chitsanzo cha M’bale Nicholas Kovalak, yemwenso anaphunzira kusukulu ya Giliyadi ndipo anatumikira monga woyang’anira chigawo. M’bale Kovalak ankadziwika bwino kuti anali munthu wachikondi. Pa nthawi ina, iye analimbikitsa woyang’anira woyendayenda wina pamodzi ndi mkazi wake kuti azichita utumiki wawo mwakhama. Iye anawalimbikitsa kuti, “Utumiki wanu muziuyamba kumayambiriro kwa tsiku m’mawa kwambiri, kumayambiriro kwa mlungu, kumayambiriro kwa mwezi komanso kumayambiriro kwa chaka.” M’baleyu ataona mmene mkazi wa woyang’anira woyendayendayo amachitira zinthu mu utumiki wake kwa masiku angapo, anamuuza kuti: “Mlongo, iwalani zija ndinakuuzani. Mukugwira kale ntchito mwakhama kwambiri. Chofunika panopa n’choti muchepetseko moto pang’ono. Zimenezi zikuthandizani kuti utumikiwu muuchite kwa nthawi yaitali.” Malangizo amenewa, omwe m’baleyo anawapereka mokoma mtima, athandiza mlongoyu kuti achite utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambirimbiri.

Pomaliza, M’bale Sanderson analimbikitsa ophunzirawo kuti akagwiritse ntchito zimene aphunzira kusukuluyi pophunzitsa ndi kuthandiza ena. (2 Timoteyo 2:2) Ophunzirawo akamachita zimenezi kulikonse kumene angatumizidwe, angathandize kuti abale ndi alongo awo akhale olimba mwauzimu, ndipo sangakayikire zoti Yehova akuwakumbukira.Salimo 20:1-5.

Mawu Omaliza. Kenako ophunzira onse analandira masatifiketi awo. Izi zitatha, m’modzi mwa anthu amene anamaliza maphunzirowo anawerenga kalata yoyamikira imene iwo analemba. Ndiyeno anthu 15 a m’gulu la anthu amene anamaliza maphunzirowo, anaimba nyimbo nambala 123 yomwe inali yomaliza pamwambowu. Nyimboyi inachokera m’buku la nyimbo lakuti Imbirani Yehova, ndipo ili ndi mutu wakuti “Abusa Ndi Mphatso za Amuna.” Iwo anaimba nyimboyi ndi mawu okha popanda kugwiritsa ntchito zida kapena nyimbo ya pa CD.