Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi, Kalasi ya Nambala 134—“Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo”

Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi, Kalasi ya Nambala 134—“Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo”

Ophunzira a ku Sukulu ya Giliyadi, a m’kalasi ya nambala 134, anamaliza maphunziro awo Loweruka pa March 9, 2013. Mwambo wa omaliza maphunzirowa unachitikira kumalo amene kuli masukulu a Mboni za Yehova ku Patterson, m’dera la New York. Sukuluyi imathandiza anthu a Mboni za Yehova omwe akhala akugwira ntchito yolalikira kwa zaka zambiri kuti akhale ndi luso kwambiri pogwira ntchito yawoyi. Ku mwambowu kunabwera achibale a ophunzirawo, anzawo ndiponso alendo osiyanasiyana ndipo anthu onse amene anasonkhana analipo 9,912.

Amene anali tcheyamani pa mwambowu ndi Mark Sanderson, yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Iye anakumbutsa anthu amene anasonkhana pa mwambowo kuti Sukulu ya Giliyadi inayamba zaka 70 zapitazo, pa February 1, 1943. Pa nthawiyo, pulezidenti wa sukuluyi anali Nathan Knorr, ndipo anafotokoza cholinga cha sukuluyi kuti: “Pali anthu ochuluka zedi amene tingawalalikire [uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu] koma tikufunikira anthu ambiri ogwira ntchitoyi. Ambuye ndi wachisomo ndipo anthu ambiri ogwira ntchitoyi adzapezeka.” Kodi zimene M’bale Knorr ankakhulupirirazi zinatheka?

Taganizirani chitsanzo ichi. Sukuluyi itangoyamba kumene, M’bale Knorr anapita ku Mexico pofufuza malo amene angatumizeko amishonale ochokera ku Giliyadi. Paulendo wakewu, mipingo yonse yozungulira, yomwe ili pamtunda wamakilomita 240 kuchokera mumzinda wa Mexico City, inaitanidwa kumsonkhano, ndipo anthu 400 anafika pamsonkhanowo. Tsopano patha zaka pafupifupi 70 kuchokera pamene amishonale oyamba ochokera kusukulu ya Giliyadi anatumizidwa ku Mexico, ndipo ngati msonkhano umenewu utachitika masiku ano n’kuitana anthu a m’mipingo yozungulira deralo, pangafike anthu oposa 200,000.

“Chili M’dzanja Lakocho N’chiyani?” Anthony Griffin, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ku United States, anakamba nkhani yokhala ndi mutu umenewu, wochokera pa Ekisodo 4:2. Palembali, Mulungu anafunsa Mose kuti: “Chili m’dzanja lakocho n’chiyani?” Mose anayankha kuti: “Ndodo.” Yehova anagwiritsa ntchito ndodoyo monga chizindikiro cha udindo komanso mphamvu zimene anapereka kwa Mose. (Ekisodo 4:5) Zinthu zinkamuyendera bwino Mose pa nthawi yonse imene ankagwiritsa ntchito bwino udindo wake polemekeza Mulungu. Koma Mulungu sanasangalale pamene Mose anagwiritsa ntchito udindowo molakwika podzibweretsera yekha ulemerero n’kumanyoza abale ake monga mmene anachitira pa “Meriba.”—Numeri 20:9-13.

M’bale Griffin anayerekezera ndodo ya Mose ndi zimene ophunzirawo anaphunzira ku Giliyadi. M’baleyu analimbikitsa ophunzirawo kuti asakagwiritse ntchito molakwika zimene aphunzirazo, ngati udindo woti azilamulira abale awo. M’malomwake, anawalangiza kuti: “Mukagwiritse ntchito zimene mwaphunzira potamanda ndi kulemekeza Yehova. Mukamachita zimenezi mudzapitiriza kukhala dalitso kwa anthu amene mukuwatumikira.”

“Kumbukirani Mana.” Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira, anafotokoza mfundo zinayi zimene tingaphunzire pa nkhani ya mana amene Mulungu ankapereka mozizwitsa kwa Aisiraeli m’chipululu.

  • Mukapitirize kugwira ntchito mwakhama. (Numeri 11:8) Kuti adye mana, Aisiraeli ankafunikira kugwira ntchito. Iwo ankafunikira kugwira ntchito yotola manawo mwachangu.—Ekisodo 16:21.

  • Mupewe kung’ung’udza ndi zimene Yehova akukupatsani. (Numeri 11:5, 6) Aisiraeli anayamba kudandaula ndi mana, ndipo Mulungu ankaona kuti anthuwo akung’ung’udzira iyeyo. Mofanana ndi mana, chakudya chauzimu chimene timalandira sikuti nthawi zonse chimakhala chosangalatsa. Koma nthawi zonse chimakhala chopatsa thanzi. Choncho nthawi zonse tiziyamikira zinthu zimene Yehova akutipatsa.

  • Muzikhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova adzakusamalirani. Tsiku ndi tsiku, Mulungu ankawapatsa Aisiraeli mana ndipo pa tsiku loti mawa lake ndi la Sabata, ankawapatsa mana okwanira kudya masiku awiri. (Ekisodo 16:22-26) Ifenso tizikhulupirira kuti Mulungu apitiriza kutipatsa zinthu zofunikira pa moyo wathu.—Mateyu 6:11.

  • Mulungu sangadalitse munthu wosamvera. (Ekisodo 16:19, 20, 25-28) Aisiraeli amene ankatola mana pa Sabata Yehova sanasangalale nawo. Komanso amene ankatola mana ochuluka kwambiri n’kusunga patsiku loti mawa lake si la Sabata, ankapeza kuti manawo achita mphutsi patsiku lotsatira ndipo ankanunkha kwambiri.

M’bale Lett kenako analimbikitsa ophunzirawo kuti asamaiwale mfundo zimene aphunzira pa nkhani ya mana. M’baleyu anawauza kuti: “ Yehova ‘adzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira.’”—Malaki 3:10.

“Konzekerani Moyo wa M’dziko Latsopano.” William Samuelson, yemwe ndi woyang’anira Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu, anafotokoza kuti n’zomveka kuti panopa tinganene kuti ndife okonzeka ndipo tikufunitsitsa kulowa m’dziko latsopano komabe aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wokonzekadi?’ Zimenezi zimafuna ‘kukhala oganiza bwino.’—1 Petulo 4:7.

Mmene timaonera zophophonya zathu zingasonyeze kuti ndife oganiza bwino kapena ayi. Pa zinthu zonse zimene tingalakwitse, tisamangonamizira Satana kapena dziko lakeli, n’kumaganiza kuti tidzayamba kuyesetsa kuchita bwino zinthu Mulungu akadzachotsa Satana ndi dziko loipali. Panopa n’zotheka kulimbana ndi makhalidwe oipa, monga mtima wodzikonda. Tingachite zimenezi poyesetsa “kuvala umunthu watsopano.”—Aefeso 4:24.

“Siyani Pansi Cholembera Chanu.” Mark Noumair, yemwe ndi mphunzitsi wa sukulu ya Giliyadi, anagwiritsa ntchito fanizo la cholembera pofotokoza za “mtima umene tingakhale nawo wofunitsitsa kulemba za moyo wathu.” ‘Timasiya cholembera chathu pansi’ tikamalola kuti Yehova alembe za moyo wathu, osati ifeyo kulemba tokha.

Mfumu Sauli ndi chitsanzo chotichenjeza pa nkhani imeneyi. Pa nthawi imene ankasankhidwa kuti akhale mfumu, iye anali munthu wodzichepetsa kwambiri. (1 Samueli 10:22, 27; 11:13) Koma patapita nthawi, iye “anayamba kulemba yekha nkhani yofotokoza moyo wake,” kutanthauza kuti ankachita zimene iyeyo ankaona kuti n’zolondola ndipo ankadzibweretsera ulemerero. Popeza iye anasiya kumvera Mulungu, Mulunguyo anamukana.—1 Samueli 14:24; 15:10, 11.

Ngakhale kuti ophunzirawo anali okhulupirika mpaka patsiku limene ankamaliza maphunziroli, M’bale Noumair anawakumbutsa kuti apitirize kugwira ntchito ya Mulungu motsatira malangizo ake. M’baleyu anauza ophunzirawo kuti: “Mukhale osamala kwambiri. Musamaganize kuti Mulungu akamakugwiritsani ntchito ndiye kuti akusangalala nanu.” Mwachitsanzo, Mose analephera kutsatira malangizo a Mulungu pamene ankafuna kutulutsa madzi m’thanthwe m’njira yozizwitsa. Iye anatulutsadi madziwo koma Mulungu sanasangalale naye.—Numeri 20:7-12.

“Lengezani Mofuula Mawu Amene Ankalengezedwa ndi Mngelo Yemwe Ankauluka Chapafupi M’mlengalenga.” Sam Roberson, yemwe ndi mphunzitsi winanso wa sukulu ya Giliyadi, anakamba nkhani yake yochokera palemba la Chivumbulutso 14:6, 7. Kenako m’baleyu anatsogolera ophunzirawo pamene ankachita zitsanzo zoyerekezera zimene ankakumana nazo pamene amagwira ntchito yolalikira za Ufumu pa nthawi imene anali kusukuluyo. Mwachitsanzo, wophunzira wina anachitidwa opaleshoni ndipo atayamba kupeza bwino, analalikira kwa nesi wina m’chipatala. Nesiyo anali wochokera ku Peru, choncho wophunzirayo anayamba n’kumuonetsa chithunzi chosonyeza ntchito yolalikira ku Chachapoyas m’dziko la Peru, chomwe chili pawebusaiti ya jw.org. Izi zinachititsa kuti nesiyo pamodzi ndi mwamuna wake ayambe kuphunzira Baibulo.

“Mwandidabwitsa . . . Ndipo Ndadabwa.” (Yeremiya 20:7) Allen Shuster, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya dziko la United States, anafunsa mafunso mabanja awiri a m’kalasiyi. Ophunzirawo anafotokoza kuti Yehova ‘anawadabwitsa.’ Anawadabwitsa bwanji? Iwo anafotokoza kuti poyamba, ankaopa kuti sangakwanitse kumaliza maphunziro a ku Giliyadi chifukwa kumakhala zambiri. Koma sukuluyo itayamba, iwo anadabwa kwambiri ndi thandizo lomwe analandira. Zimenezi zinawathandiza kuti akwanitse kumaliza maphunziro a kusukuluyi. Mlongo Marianne Aronsson, ananena mawu otsatirawa poyamikira Mulungu chifukwa cha zimene anaphunzira ku Giliyadi. Mlongoyu anati: “Sindidzavutikanso n’kuganizira kuti ndiphunzira zotani m’Baibulo. Ndazindikira kuti vesi lililonse la m’Baibulo lili ngati chuma cha mtengo wapatali.”

“Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo.” David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yaikulu pa mwambowu, yomwe inachokera palemba la Aheberi 13:7, lomwe limati: “Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu. Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani chikhulupiriro chawo.” Kodi anthu amene ‘ankatsogolera’ ntchito ya Mboni za Yehova, zaka 70 zapitazo anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro?

Pa September 24, 1942, Nathan Knorr anachititsa msonkhano wa akuluakulu omwe ankayendetsa mabungwe awiri a Mboni za Yehova. Pamsonkhanowu, M’bale Knorr anapereka maganizo oti ayambitse sukulu yatsopano yotchedwa “Giliyadi,” n’cholinga choti aziphunzitsa amishonale omwe azitsogolera ntchito yolalikira m’madera amene uthenga wabwino unali usanalalikidwe. Koma malinga ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, zinkaoneka ngati zimene M’bale Knorr ankaganizazo sizingatheke. Pa nthawiyo n’kuti nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ili m’kati, ndipo zinkaoneka kuti n’zosatheka kutumiza amishonale kumayiko ambiri. Kuwonjezera pamenepo, chuma cha padziko lonse chinali chisakuyenda bwino kuyambira m’zaka za m’ma 1930, ndipo gululi linali ndi ndalama zokwanira kuyendetsera sukuluyi kwa zaka 5 basi. Ngakhale zinali choncho, abale onsewo anagwirizana kuti sukuluyi iyambe ndipo izi zinasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro.

Anthu a m’makalasi oyambirira omwe anamaliza maphunziro awo ku Giliyadi anasonyezanso chikhulupiriro chofunika kuchitsanzira. Iwo anali okhutira ndi zinthu zimene anali nazo ndipo ankapewa kukonda ndalama. (Aheberi 13:5, 6) Ambiri ankaona kuti sadzaonananso ndi achibale awo chifukwa abale awowo sakanakwanitsa kupeza ndalama zowatumizira kuti ayendera pobwerera kwawo kuti akacheze. Ndipotu kwa zaka 10 mpaka 15, amishonale ena sanabwerere kwawo kukaonana ndi achibale awo. Komabe, iwo sankakayikira zoti Yesu apitiriza kuwasamalira pamodzi ndi achibale awowo ngati mmene wakhala akusamalirira anthu amene amamutsatira.—Aheberi 13:8.

Ophunzira a m’kalasi yoyamba ya Giliyadi, 1943

Atafotokoza zimene ophunzira ena anakumana nazo kumadera ovuta amene ankalalikira asanabwere kusukuluyi, M’bale Splane anauza ophunzirawo kuti: “Abale ndi alongo achinyamata inu mukulowa m’gulu la anthu amene akhala akumaliza maphunziro awo kusukulu ya Giliyadiyi kwa zaka 70 tsopano. . . . Mukhale osangalala kutumikira Yehova kulikonse kumene mungatumizidwe.”

M’bale Splane anamaliza nkhani yake poonetsa vidiyo ya zithunzi za anthu 77 amene anamaliza maphunziro awo ku Giliyadi ndipo tsopano akutumikira ku ofesi ya nthambi ya ku United States ya Mboni za Yehova. Pagulu la anthu 77 amenewo panali anthu awiri amene anamaliza maphunziro awo m’kalasi yoyambirira imene inachitika m’chaka cha 1943. Muvidiyo ya zithunziyo munalinso nyimbo zimene a Mboni za Yehova ankaimba polambira Mulungu pa zaka 70 zapitazi.

Ophunzirawo atalandira madipuloma awo, wophunzira wina anawerenga kalata yawo yoyamikira Yehova ndi gulu lake chifukwa cha zimene anaphunzira kusukuluyi. Kenako M’bale Sanderson anamaliza pulogalamuyi ndi mfundo yakuti ngakhale kuti padutsa zaka 70, zimene M’bale Knorr ananena kwa ophunzira a kalasi yoyambirira zikugwirabe ntchito. M’baleyo anati: “Kulikonse kumene angakutumizeni muzikumbukira kuti ntchito yanu . . . n’kulengeza za Ufumu. Ndipotu kugwira ntchito imeneyi komanso kuimba nyimbo zotamanda Mulungu ndi mwayi waukulu zedi pamene tikuyembekezera nkhondo ya Aramagedo. . . . Mukapeza mwayi woti n’kulalikira, lalikirani.”