Pa October 5 ndi 6, 2013, anthu a m’mayiko 31 okwana 1,413,676 anachita nawo msonkhano wapachaka bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Msonkhanowu unali wanambala 129 ndipo unachitikira m’Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ya mumzinda wa Jersey City, New Jersey, m’dziko la United States of America, ndipo anthu ena anaonera msonkhanowu pa vidiyo kudzera pa Intaneti.

M’bale Guy Pierce, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi amene anali tcheyamani wa msonkhanowu. Iye anachititsa kuti anthu amene anali pamsonkhanowu akhale ndi chidwi pamene anawatsimikizira kuti msonkhanowo uwathandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri a m’Baibulo, uwonjezera kuwala kwa choonadi, komanso kuti “chakudya [chauzimu] cha pa nthawi yoyenera” chiperekedwa pa msonkhanowu.Mateyu 24:45; Miyambo 4:18.

“Malo Okhala ndi Zinthu Zotithandiza Kulemekeza Yehova.”

M’bale Mark Sanderson, wa m’Bungwe Lolamulira ananena za malo atsopano oonetsa zinthu zosiyanasiyana amene ali kulikulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, m’dera la New York m’dziko lomweli la America. Malowa anawapatsa mutu wakuti “Dzina la Mulungu M’Baibulo,” ndipo akusonyeza malo oyenerera amene dzina la Mulungu limapezeka m’Malemba Achiheberi ndi m’Malemba Achigiriki. M’malo amenewa, omwe ali ngati chipinda, muli Mabaibulo akale ambirimbiri, zinthu zina zakale, komanso masamba a m’Baibulo a zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500.

Zinthu zinanso zochititsa chidwi zimene zili m’chipinda chimenechi ndi masamba a Baibulo la zaka za m’ma 1500 limene linamasuliridwa ndi William Tyndale. William anali womasulira Baibulo woyamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu m’Chingelezi. Pali tsamba linanso limodzi la Baibulo lachisipanishi limene linamasuliridwa mu 1602, lomwe linkadziwika kuti Baibulo la Reina-Valera. M’Baibuloli anaikamo dzina la Mulungu ndipo m’malo onse analilemba kuti “Iehova.” M’chipindachi anaikamonso Mabaibulo osiyanasiyana achingelezi, monga lotchedwa Great Bible (linasindikizidwa mu 1549), 12-language Bible (Linatulutsidwa mu 1599 ndipo limatchedwanso kuti Nuremberg Polyglot) lomasuliridwa ndi Elias Hutter. Mulinso Baibulo la Geneva Bible (linasindikizidwa mu 1603). M’Mabaibulo onsewa muli dzina la Mulungu.

M’bale Sanderson analimbikitsa aliyense kuti adzaone zinthu zomwe zili m’malowa. M’baleyu anati: “Pemphero lathu ndi lakuti . . . malowa athandize anthu a mitima yabwino, a misinkhu yonse komanso a maphunziro osiyanasiyana kuti abwere adzayambe kukonda zinthu ziwiri zimene tonsefe timakonda. Zinthuzi ndi mawu a Mulungu omwe ndi a mtengo wapatali ndiponso dzina lake lakuti Yehova, lomwe ndi lolemekezeka.”

Lemba la Chaka cha 2014.

Pambuyo pakuti M’bale Gerrit Lösch, wa m’Bungwe Lolamulira watsogolera pophunzira Nsanja ya Olonda mwachidule mlungu umenewo, M’bale Pierce analengeza lemba lachaka cha 2014, lakuti “Ufumu wanu Ubwere.” (Mateyu 6:10) Ngakhale kuti ife a Mboni za Yehova takhala tikuona kuti lemba limeneli ndi labwino kwambiri, ndi lapadera kwambiri chaka chino cha 2014 chifukwa chakuti patha zaka 100 kuchokera pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba.

“Mphatso Yamtengo Wapatali Yochokera Kwa Mulungu.”

Kenako anthu anasangalala kuonera vidiyo yofotokoza nkhani yokhudza Baibulo la Dziko Latsopano lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Anthu ena amati Baibuloli lili m’gulu la Mabaibulo amene anamasuliridwa bwino kwambiri. Nthawi imene Nathan Knorr ankatulutsa mbali yoyamba ya Baibulo la Dziko Latsopano m’chaka cha 1950 pamsonkhano wamayiko, anapereka malangizo amene ndi othandizabe mpaka pano. Iye analangiza anthuwo kuti aliwerenge lonse, aliphunzire ndiponso azithandiza ena kuliphunzira chifukwa zimenezi zidzawathandiza kuti aziitanira pa dzina la Yehova.

“Zinthu Zosangalatsa Zimene Zinachitika M’mbuyomu.”

Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yamutu omwe uli pamwambawu. Nkhaniyi inali ndi mbali yomwe inaijambuliratu yokhudza kucheza ndi anthu 4 a pa Beteli ya ku United States of America, amene analipo pa nthawi imene magawo 6 a Baibulo la Dziko Latsopano ankatulutsidwa kuyambira mu 1950 mpaka mu 1960.

Eunice Timm amakumbukira nthawi imene ankagwiritsira ntchito Baibulo la Dziko Latsopano pamisonkhano yampingo. Iye anasangalala kwambiri ndi Baibuloli chifukwa lili ndi zinthu zothandiza munthu pofufuza, monga malifalensi amene amapezeka padanga lapakati pa Baibuloli. Popeza kuti zinali zovuta kunyamula magawo 6 a Baibuloli kumisonkhano yampingo, iye ananena kuti ankangonyamula magawo okhawo amene ankafunika kuwagwiritsa ntchito pa tsikulo, kuphatikizapo Baibulo laling’ono la King James Version.

Baibulo la Dziko Latsopanoli linakhudzanso mbali zina za kulambira kwathu. Mwachitsanzo, M’bale Fred Rusk anafotokoza kuti chaka cha 1950 chisanafike, anthu amene ankapemphera moimira banja la Beteli ankagwiritsa ntchito mawu ochokera m’Baibulo la King James Version, monga akuti “Ufumu wanu udze.” Kungoyambira nthawi imene Baibulo la Dziko Latsopanoli linatulutsidwa, popemphera anayamba kugwiritsira ntchito mawu osavuta kumva amene anthu amalankhula tsiku ndi tsiku.

M’bale John Wischuk anachita chidwi ndi Baibuloli chifukwa linamasuliridwa bwino kwambiri komanso anthu amene anali m’komiti yomasulira Baibuloli anali odzichepetsa kwambiri. Iye anati: “Anthu a m’komitiyi sanafune kuti adziwike pa nthawi imene anali moyo kaya atamwalira, chifukwa ankafuna kuti ulemelero wonse upite kwa Yehova Mulungu.” Ndiyeno M’bale Charles Molohan anagwirizana ndi anthu ena onse amene ankafunsidwawo ponena kuti; “Baibulo la Dziko Latsopanoli latithandiza kuti choonadi chizitifika pa mtima, kuti chikhulupiriro chathu chilimbe komanso kuti tizithandiza anthu ena kuti nawonso akhale ndi chikhulupiriro.”

“Tikuwamva Akulankhula Zinthu Zazikulu za Mulungu M’zinenero Zathu.” (Machitidwe 2:11)

M’bale Geoffrey Jackson, wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani, ndipo nkhaniyo ili mkati, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano limene linakonzedwanso. Pomaliza nkhani yake onse amene anali pa msonkhanowo, kuphatikizaponso amene ankaonera msonkhanowo pa vidiyo kudzera pa Intaneti m’madera osiyanasiyana analandira Baibuloli.

M’bale Jackson anafotokoza kuti zaka 60 zadutsa tsopano kuchokera pamene gawo loyamba la Baibulo la Dziko Latsopanoli linatuluka. Kuyambira nthawi imeneyo chinenero cha Chingelezi chakhala chikusintha, choncho panafunika kumasulira Baibulo momveka bwino, m’Chingelezi chimene anthu amalankhula popanda kusintha tanthauzo lake.

M’chaka cha 2005, Bungwe Lolamulira linayamba kulimbikitsa ntchito yomasulira Baibulo m’zinenero zosiyanasiyana. Kungoyambira m’chaka chimenechi, Baibulo la Dziko Latsopanoli lamasuliridwa m’zinenero zambiri, kuchoka pa 52 kufika pa 121. Komanso ntchito yomasulira Baibuloli ili mkati m’zinenero zina zokwana 45. Anthu akamamasulira Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero zina, amafunsa mafunso kuti azimvetsa mawu ena. Padakali pano mafunso okwana 52,000 afunsidwa ndiponso kuyankhidwa. Ambiri mwa mafunsowa anathandiza kudziwa mavesi amene anafunika kuwasintha pang’ono.

Mwachitsanzo, M’bale Jackson anafotokoza kuti Baibulo lakale la Dziko Latsopano la m’Chingelezi palemba la 1 Samueli 14:11, limanena kuti Yonatani ndi mtumiki wake womunyamulira zida “anadziulula kumudzi wa asilikali a Afilisiti.” Pofuna kuti lembali lizimveka bwino, Baibulo la Dziko Latsopano limene lakonzedwanso lili ndi mawu akuti, “anadzionetsera.” Mofanana ndi zimenezi, mawu a palemba la Mika 2:6 poyamba anali omasuliridwa liwu ndi liwu, ndipo linali lakuti: “Anthu inu musatulutse mawu. Iwo atulutsa mawu.” Koma tsopano palembali pali mawu akuti: “Anthu inu musalosere. Aneneri amalosera.”

Zaka 5 zapitazo Bungwe Lolamulira linasankha komiti yoti ikonzenso Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi ndipo zotsatira za ntchito yawo ndi Baibulo latsopanoli. Baibuloli ndi losangalatsa, losavuta kuwerenga komanso ndi lolimba kwambiri. M’bale Jackson analengeza kuti Baibulo lachingelezili posachedwapa liyamba kusindikizidwa lalikulu lokhala ndi zilembo zikuluzikulu, komanso lina laling’ono kwambiri lokwana m’thumba.

‘Kuphunzitsa ndi Kufotokoza Bwino Mawu a Choonadi’.

M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira anafotokoza zinthu zothandiza zopezeka m’Baibulo latsopanoli, ndipo mutu wa nkhani yake unachokera palemba la 2 Timoteyo 2:15. Mawu akuti “kufotokoza bwino” amene ali palembali amatanthauza “kudula moongoka.” Tikufunika kugwiritsa ntchito “lupanga la mzimu” m’njira yoongoka komanso molondola. (Aefeso 6:17) Kenako M’bale Lett anasonyeza mmene zinthu zina zomwe zili m’Baibuloli zingatithandizire kuchita zimenezi.

  1. Gawo limene lili kumayambiriro kwa Baibuloli, lamutu wakuti “Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani?” lili ndi mavesi a m’Baibulo amene akuyankha mafunso okwana 20 okhudza ziphunzitso zoyambirira za Baibulo.

  2. Mbali ya Zakumapeto A, ikufotokoza zinthu zina zokhudza Baibulo latsopanoli monga, mawu ena amene asintha komanso malo amene pali dzina la Mulungu.

  3. Mbali ya Zakumapeto B ili ndi mbali zokwana 15 zokhala ndi mapu ndiponso zithunzi zothandiza pophunzira patokha komanso pophunzitsa ena.

  4. Kumayambiriro kwa buku la m’Baibulo lililonse kuti gawo la “Zokhudza Bukuli.” Gawoli lizifotokoza zokhudza bukulo mwachidule ndipo zimenezi zizithandiza munthu kupeza mbali imene akufuna kuwerenga mosavuta. Gawo limeneli lalowa m’malo mwa timitu timene tinkakhala pamwamba pa tsamba lililonse la Mabaibulo oyamba.

  5. Gawo la “Matanthauzo a Mawu Ena” limafotokoza mwachidule matanthauzo a mawu ambirimbiri amene ali m’Baibulo.

  6. Gawo lakuti “Kalozera wa Mawu a M’Baibulo” tsopano lachepetsedwa. Pagawoli tsopano pali mawu komanso mavesi amene amagwiritsidwa ntchito kwambiri polalikira komanso kuphunzitsa.

  7. Malifalensi amene amapezeka pakati pa tsamba lililonse achepetsedwanso. Panopa pali mawu okhawo omwe ndi othandiza kwambiri mu utumiki.

  8. Mawu a m’munsi amafotokoza mawu ofanana ndi amene ali pavesi, amamasulira chiganizo mongotsatira mmene chalembedwera, komanso amafotokoza zina ndi zina zokhudza vesilo.

JW Library.

M’bale John Ekrann, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anafotokoza zokhudza pulogalamu yatsopano ya JW Library imene ingagwiritsidwe ntchito zipangizo zamakono monga mafoni ndi matabuleti. Papulogalamuyi pali Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwansoli komanso Mabaibulo ena osiyanasiyana okwana 5. Pulogalamuyi inatulutsidwa kwa ulele pa October 7, 2013, kudzera m’mapulogalamu ena akuluakulu a pakompyuta.

“Kumasulira Mawu a Mulungu Molondola.”

M’bale Anthony Morris, wa m’Bungwe Lolamulira ananena zimene zinathandiza anthu a m’Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano pokonzekera kumasuliranso Baibuloli. Iye anafotokoza kuti komitiyi inagwiritsa ntchito mfundo zopezeka pa 1 Akorinto 14:8, 9 n’cholinga choti Baibuloli likhale losavuta kumva. Komitiyi yapewanso kumasulira liwu lililonse mmene lilili m’malo amene kuchita zimenezo kukanasokoneza tanthauzo la mawuwo.

Mwachitsanzo, ngati akanamasulira lemba la Genesis 31:20 potengera mmene mawuwo alili, ndiye kuti akanamasulira kuti: “Yakobo anaba mtima wa Labani.” Koma mwambi wachiheberi umene unagwiritsidwa ntchito palembali umasiyana tanthauzo lake ndi mwambi wachingelezi. N’chifukwa chake M’Baibulo la Dziko Latsopano lembali analimasulira kuti: “Yakobo anachoka mozembera Labani.” Chimodzimodzinso ndi lemba la 1 Akorinto 7:39. Akanakhala kuti mawu a m’lembali anawamasulira potengera mmene alili, zikanatanthauza kuti mkazi akhoza kukwatiwa ndi mwamuna wina ngati mwamuna wake “atagona.” Popeza m’Baibulo mawu akuti “kugona” nthawi zina amatanthauza kumwalira, Baibulo la Dziko Latsopano linamasulira mawuwa m’njira yothandiza munthu amene akuwerenga kuti asasokonezeke. Palemba limeneli Baibuloli linagwiritsa ntchito mawu akuti “akamwalira.”

M’bale Morris ananena kuti: “Baibuloli analilemba pogwiritsa ntchito mawu amene anthu monga alimi, abusa ndi asodzi amalankhula tsiku ndi tsiku. Umu ndi mmene Baibulo lomasuliridwa bwino liyenera kukhalira. Losavuta kumva kwa anthu ofunitsitsa kuliphunzira, kaya anapita kusukulu kapena ayi.”

Kugwiritsa Ntchito ‘Mawu Okoma’ Ndiponso ‘Mawu Olondola a Choonadi.’ ”

M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani ya mutu umenewu kuchokera palemba la Mlaliki 12:10. Iye anati anthu amene analemba Baibulo anaonetsetsa kuti alemba zimene Mulungu anawauza, choncho Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inamasulira Baibuloli mosamala kwambiri. Komitiyi inamasulira “mawu olondola a choonadi” komanso inaonetsetsa kuti uthenga wa Mulungu wafotokozedwa momveka bwino.

M’bale Splane ananena kuti: “Mawu ambiri achingelezi amakhala ndi matanthauzo angapo. Mwachitsanzo, Mabaibulo a Dziko Latsopano a m’mbuyo anagwiritsa ntchito mawu akuti “chitsanzo cha mawu olondola” palemba la 2 Timoteyo 1:13. Mawu akuti “chitsanzo” ali ndi matanthauzo ambiri. Mawuwa angatanthauze “chinthu chimene anthu opanga zinthu angaonere pofuna kupanga zinthu zina.” Ngati titamva lembali potengera tanthauzo limeneli, ndiye kuti mawu a palembali amatanthauza kasanjidwe komanso kalembedwe ka mawu kokongola kamene munthu angakapeze m’Baibulo. Komabe, tanthauzo limene limagwirizana kwambiri ndi mawu amene ali m’Baibulo loyambirira ndi lakuti “mfundo . . . zofunika kuchitsatira.” Choncho palembali, Baibulo lokonzedwansoli limati “mfundo za mawu abwino.”

M’bale Splane anafotokozanso mawu ena amene asinthidwa kuti agwirizane ndi mmene chinenero Chingelezi chilili masiku ano. Mwachitsanzo, mawu achingelezi amene pa Chichewa anawamasulira kuti “kupachika” m’Baibulo la Dziko Latsopano la m’mbuyomu ponena za mmene Yesu anaphedwera, nthawi zambiri amatanthauza kuboola munthu ndi chimtengo chosongoka n’kumusiya pomwepo. Popeza Yesu sanabooledwe ndi mtengo wozunzikirapo, komiti yomasulira Baibuloli yagwiritsa ntchito mawu akuti “kukhomedwa pamtengo,” ponena za mmene Yesu anaphedwera.Mateyu 27:22, 23, 31.

M’bale Splane anamalizitsa ndi mawu akuti: “Pemphero lathu ndi lakuti mukamawerenga ndiponso kuphunzira Baibulo la Dziko Latsopano limene lakonzedwansoli, likuthandizeni kuyandikira kwambiri Yehova. Ndipo lolani kuti akhale Atate wanu ndiponso Bwenzi lanu.”

Mawu Omaliza.

M’bale Pierce ananena kuti Baibulo la Dziko Latsopano limene lakonzedwansoli lili ngati chakudya chofunika kwambiri “pa phwando la zakudya zabwinobwino.” (Yesaya 25:6) Kenako anamalizitsa popempha anthu onse amene anali pamsonkhanowo kuti ayimbe nyimbo nambala 114 yochokera m’buku la Imbirani Yehova, yamutu wakuti “Buku la Mulungu ndi Chuma Chamtengo Wapatali.”