Pitani ku nkhani yake

Msonkhano wa “Padziko Lonse Lapansi”

Msonkhano wa “Padziko Lonse Lapansi”

Zaka 50 zapitazo, anthu 583 a Mboni za Yehova anayamba ulendo wa milungu 10 woyenda padziko lonse lapansi. Cholinga cha ulendowu sichinali kungoona mayiko. Iwo ankafuna kulimbikitsana ndi Akhristu anzawo omwe anapita kumsonkhano wa chaka cha 1963 wakuti, “Uthenga Wabwino Wosatha.” Anthu amene anapezeka pamsonkhanowu anali ochokera m’mayiko oposa 20. Pa chifukwa chimenechi, msonkhanowo anaupatsa dzina lakuti Msonkhano wa “Padziko Lonse Lapansi.”

Pamsonkhano uliwonse pankakambidwa nkhani yaikulu yomwe mutu wake unali wakuti, “Mulungu Akadzakhala Mfumu ya Padziko Lonse Lapansi.” Nathan Knorr, wochokera kulikulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, anakamba nkhaniyi pamisonkhano yambiri. Anafotokoza zinthu zoipa zimene zikuchitika padzikoli n’kuziyerekezera ndi lonjezo lalikulu la m’Baibulo lokhudza kubwezeretsedwa kwa Paradaiso padziko lapansili. Anthu onse amene anamvetsera nkhaniyi padziko lonse lapansi analipo 580,509.

Kuzungulira “Padziko Lonse Lapansi” kwa Milungu 10

Misonkhanoyi inayambira mumzinda wa Milwaukee m’dera la Wisconsin, m’dziko la U.S.A. Kenako anthu a Mboni 583 aja anapita ku New York. Atachoka kumeneko anaima ku England, Sweden, Germany ndi Italy. Anthuwo akafika m’dziko lililonse, ankalalikira nawo uthenga wabwino wochokera m’Baibulo.

Anthu ambiri a m’mayiko amene a Mboniwo anapita anayamikira kwambiri kuti a Mboniwo anapatula nthawi yawo kuti akawalalikire. Mayi wina wa ku Stockholm m’dziko la Sweden, ananena kuti: “Kubwera kwanuku sindidzakuiwala m’moyo wanga wonse. . . . Koma inu zoona munayenda ulendo wonsewu kuti mudzandiuze za chikhulupiriro chanu mwa Mulungu? Anthu inu ndinu osiririka kwambiri.”

Anthuwa koma anakhumudwa atafika ku Athens, m’dziko la Greece. Akuluakulu a boma anasintha zoti msonkhano ukachitikire ku sitediyamu ya ku Panathinaikos chifukwa choumirizidwa ndi atsogoleri achipembedzo a mumzindawo. Komabe zimenezi sizinalepheretse kuti msonkhano uchitike mumzindawu. Iwo anachita msonkhanowu m’nyumba za anthu komanso m’mipingo chakumapeto kwa mwezi wa August ndipo anthu pafupifupi 10,000 anapezekapo.

Atachoka ku Athens, anthuwa anapita ku Lebanon, Jordan, Israel ndi ku Cyprus. Akhristu anzawo anawalandira ndi manja awiri m’mayiko onsewa. Mwachitsanzo, mumzinda wa Nicosia m’dziko la Cyprus, wa Mboni wina pa anthu 583 aja ananena zinthu zochititsa chidwi zimene zinkachitika ndi nsapato yake. Iye anati: “Nthawi iliyonse ndikapita kunyumba kumene tinafikira n’kuvula nsapato . . . , zinkapezeka kuti zasowa . . . , pakadutsa mphindi 5, nsapatozo zinkapezeka koma zitapolishidwa ndipo zinkachita kunyezimira kwambiri.”

Pomaliza anapita zigawo za ku Asia ndi ku Pacific. Anayenda m’mayiko a India, Burma (masiku ano amati Myanmar), Thailand, Hong Kong, Singapore, Philippines, Indonesia, Australia, Taiwan, Japan, New Zealand, Fiji ndi Korea. M’mayiko amenewanso anthuwa analandiridwa ndi manja awiri komanso analandira a Mboni ena amene anabwera kudzamvetsera msonkhanowu. Anthu ambiri anachita khama kuti akwanitse kudzapezeka pamisonkhanoyi. Chitsanzo ndi mwamuna ndi mkazi wina omwe anali atatsala pang’ono kuchita ukwati wawo. Anthuwa anali ochokera mumzinda wa Yokosuka, m’dziko la Japan. Mwamunayo atapempha tchuthi kwa abwana ake kuti apite kumsonkhano womwe unali ku Kyoto, anamuuza kuti anthu amaloledwa kutenga tchuthi kuti apite kumaliro kapena kuukwati basi. Popeza mwamuna ndi mkaziyu anali atagwirizana kale zokwatirana, anakonza zoti akwatirane mwachangu kuposa nthawi imene ankafuna. Iwo atangokwatirana anathera masiku ena a tchuthi kumsonkhanowo.

Anthuwa anamaliza ulendowu kumayambiriro kwa mwezi wa September ndipo anamalizira ku Hawaii ndi ku California, m’dziko la U.S.A. komwe anakachitanso msonkhano. Ku malo omaliza kumene kunachitikira msonkhanowu kunali ku Pasadena, m’dera la California, ndipo kunasonkhana anthu ochuluka zedi kuposa amene ankayembekezeredwa. Izi zinachititsa kuti mumsewu mukhale magalimoto ambirimbiri msonkhanowo utatha. Ngakhale zinali choncho, m’nyuzipepala ina ya m’derali analembamo zimene wamkulu wa apolisi wina ananena. Iye anati: “Sindinaonepo msonkhano wokhala ndi anthu ambiri chonchi koma wopanda chisokonezo.”

Msonkhano Wosaiwalika

Pali zinthu zabwino zambiri zimene zinachitika pamsonkhanopo zimene panopa zimakumbukiridwabe. Mwachitsanzo, pamsonkhanowo panatuluka buku lofotokoza nkhani za m’Baibulo lachingelezi lakuti “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial” ndipo limagwiritsidwabe ntchito mpaka pano pamisonkhano yampingo ya Mboni za Yehova.

Harold King atangotulutsidwa kumene m’ndende ku China

Komanso ku msonkhano umene unachitika ku New York kunatulutsidwa nyimbo yatsopano. Nyimboyi inalembedwa ndi Harold King, munthu wa Mboni yemwe anatulutsidwa kundende ya ku China m’chaka cha 1963. Nyimboyi inali ndi mutu wakuti “Kumka Kunyumba ndi Nyumba.” Harold King analemba nyimboyi ali m’ndende ndipo a Mboni za Yehova amaimbabe nyimboyi yomwe masiku ano ili ndi mutu wakuti “Kunyumba ndi Nyumba.”

Misonkhano ya Mboni za Yehova masiku ano imachitika mosiyana kwambiri ndi mmene inkachitikira kale. Masiku ano misonkhano imachitika m’malo ambiri zomwe zimachititsa kuti pazikhala chiwerengero chocheperako. Zimathandizanso kuti anthu asamayende mtunda wautali. Zimenezi komanso zinthu zina zimapangitsa kuti anthu ambiri azimvetsera msonkhano popanda kudodometsedwa. Chaka chilichonse, anthu oposa 7 miliyoni a Mboni za Yehova komanso amene amawaitana amapezeka pa misonkhano yathu. Kodi mukufuna kudzakhala nawo pa msonkhano wotsatira. Mukhoza kupeza malo a msonkhano a pafupi ndi kumene mukukhala pawebusaitiyi.