Pitani ku nkhani yake

Bungwe Lolamulira Linalimbikitsa a Mboni ku Russia ndi ku Ukraine

Bungwe Lolamulira Linalimbikitsa a Mboni ku Russia ndi ku Ukraine

“Pa May 10 ndi 11, a Mboni za Yehova okwana 165,000 anasonkhana ku Ukraine kuti amvetsere nkhani zolimbikitsa zochokera m’Baibulo zokambidwa ndi a Stephen Lett a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Pa nthawiyi, a Lett anawerenganso kalata yolimbikitsa yochokera ku bungwe lolamulira. Atamvetsera kalatayo, mayi wina anati: “Tinkachita kumva mumtimamu kuti bungwe lolamulira limatikonda kwambiri.”

Nkhani zimene a Lett anakamba komanso kalata yomwe anawerenga, anazimasulira m’zinenero 5 ndipo anthu anamvetsera pa telefoni m’Nyumba za Ufumu zokwana 1,100 zomwe zili m’dzikoli.

Pamene a Stephene Lett amapita kukalimbikitsa a Mboni a ku Ukraine, a Mark Sanderson womwenso ndi a m’Bungwe Lolamulira anapita kukalimbikitsa a Mboni a ku Russia mlungu womwewo. Nawonso a Sanderson anakamba nkhani za m’Baibulo zolimbikitsa komanso anawerenga kalata yochokera ku bungwe lolamulira. Anthu okwana 180,413 anamvetsera pulogalamuyi pa telefoni m’mipingo yoposa 2,500 ku Belarus ndi ku Russia ndipo anaimasulira m’zinenelo 14.

Kalata imene Bungwe Lolamulira linalemba inawerengedwa ku mipingo yonse ya ku Russia ndi ku Ukraine. Poyamikira zomwe bungwe lolamulira linalemba m’kalatayo, ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Russia inati: “Abale ndi Alongo anakhudzika mtima kwambiri kuti Bungwe Lolamulira limawaganizira komanso kuwakonda choncho. Tonse tinamva ngati kuti Bungwe Lolamulira latihaga.”

Popeza kuti ku Rassia ndi ku Ukraine kwakhala kuli mavuto a zandale, Bungwe Lolamulira linalemba kalatayo pofuna kulimbikitsa a Mboni anzawo m’mayikowa. M’kalatayo, Bungwe Lolamulira linalimbikitsa a Mboniwo kuti apitirize kupewa ‘kukhala mbali ya dzikoli’ ndipo iwo angachite zimenezi popewa kulowerera zandale.—Yohane 17:16.

Bungwe Lolamulira linalimbikitsanso a Mboniwo kuti apitirize kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Kuti zimenezi zitheke, anawauza kuti apitirize kupemphera komanso kuphunzira Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene aphunzirazo. Bungwe Lolamulira linawalimbikitsa kuti ngakhale atakumana ndi mayesero otani, azikumbukira lonjezo la Yehova lopezeka pa Yesaya 54:17 lomwe limati: “Chida chilichonse chomwe chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.”

M’kalatayo, bungwe lolamulira linamaliza ndi mawu akuti: “Timakukondani kwambiri. Nthawi zonse muzikumbukira kuti timakuganizirani komanso kukupemphererani.”

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Ukraine inanena kuti: “Abale ndi alongo sanayembekezere kuti Bungwe Lolamulira lingawasonyeze chikondi chotere moti analimbikitsidwa kwambiri. Tinasangalala kulimbikitsidwa limodzi ndi abale athu a ku Russia pa masiku ofanana. Izi zinasonyeza kuti anthu a Mulungu ndi ogwirizana komanso kuti Yehova ndi Yesu amawasamalira. Kunena zoona tinalandira thandizo la pa nthawi yake ndipo tinalimbikitsidwa kwambiri. Tikudziwa kuti tipitirizabe kukumana ndi mavuto, koma ndife otsimikiza mtima kuti sitisiya kutumikira Yehova.”