Pitani ku nkhani yake

Akuluakulu a Mzinda wa Atlanta Analandira a Mboni za Yehova ndi Manja Awiri

Akuluakulu a Mzinda wa Atlanta Analandira a Mboni za Yehova ndi Manja Awiri

“Anthu a chipembedzo chanu ndimawatayira kamtengo chifukwa chokonda kuchita zinthu zopititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu. Mumathandiza a Mboni anzanu komanso anthu ena mowolowa manja. Zimenezi ndi zofunika kwambiri ndipo dziwani kuti timakuyamikirani.”

Mawu amenewa achokera m’kalata imene Meya wa mzinda wa Atlanta ku Georgia m’dziko la United States, dzina lake Kasim Reed analemba. Meyayu analemba kalatayi povomereza a Mboni za Yehova kuti apangire misonkhano yawo ikuluikulu itatu mumzindawu.

Nawonso oyang’anira mzindawu analandira anthu odzachita msonkhano ndi manja awiri. Iwo analemba kuti: “Padziko lonse pali a Mboni za Yehova pafupifupi 8 miliyoni ndipo ndi a . . . zikhalidwe zosiyanasiyana komanso amalankhula zinenero zosiyanasiyana. Ngakhale zili chonchi, . . . ndinu ogwirizana chifukwa muli ndi cholinga chofanana . . . Nonse mumafuna kulemekeza Yehova, Mulungu wotchulidwa m’Baibulo amene analenga zinthu zonse.”

Misonkhano itatu inachitikira mumzindawu mwezi wa July ndi wa August 2014, iwiri inali ya Chingelezi ndipo umodzi unali wa Chisipanishi. Anthu amene anapezeka pamisonkhanoyi anachokera m’mayiko pafupifupi 28 ndipo misonkhano imene inachitika m’Chingelezi inamasuliridwa m’Chirasha ndi m’Chijapanizi pofuna kuthandiza anthu amene amalankhula zinenerozi. Anthu onse amene anapezeka pa misonkhano itatu yonseyi anakwana 95,689.

M’chaka cha 2014, a Mboni za Yehova anachita misonkhano yamayiko yokwana 24 m’mayiko 9 komanso m’zigawo 16 za ku United States.