Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Wozimitsa Moto Yemwe Anali Patchuthi Anapulumutsa Anthu

Wozimitsa Moto Yemwe Anali Patchuthi Anapulumutsa Anthu

Lamlungu pa January 5, 2014, a Serge Gerardin a ku France anali pa ulendo wa pabasi wopita ku msonkhano wa Mboni za Yehova kufupi ndi mzinda wa Paris. Koma ali m’njira, anaona ngozi yoopsa kwambiri. A Gerardin anati: “Galimoto inagunda chipilala cha simenti chomwe chinali m’mbali mwa mlatho. Kenako inanyamuka m’malere ndipo itagwa pansi inayaka.”

A Gerardin akhala akugwira ntchito yozimitsa moto kwa zaka 40. Popeza ndi m’tsogoleri wa gulu la ozimitsa moto, iwo sanachedwe kuthandiza pa ngoziyo. A Gerardin anati: “Ngakhale kuti tinkayenda mbali ina ya msewu, ndinauza dalaiva wa basi yomwe ndinakwera kuti aimitse basiyo. Zitatero, ndinathamangira pa malo a ngoziwo.” Atafika pamalowo, a Gerardin anamva aliyense akufuula kuti: “Ndithandizeni! Ndithandizeni!” Popitiriza kufotokoza, a Gerardin anati: “Zinali zovuta kuti ndithandize anthuwo chifukwa ndinalibe zovala zodzitetezera komanso ndinali nditavala suti ndi taye. Komabe, nditamva kufuula kwa anthuwo, ndinaona kuti anthu angapulumuke ngati nditathandiza.”

A Gerardin anaona munthu wina wovulala pambali pa galimotoyo akuvutika kwambiri ndipo anamuchotsa pamalopo. Kenako munthuyo anauza a Gerardin kuti: “Anthu enanso awiri ali m’katimu.” A Gerardin anati: “Pa nthawiyi, anthu ambiri anali atafika pamalowa koma sakanatha kuthandiza anthuwo chifukwa galimotoyo inali ikuyakabe.”

Madalaiva ena a magalimoto akuluakulu anabweretsa zipangizo zozimitsira moto ndipo motsogoleredwa ndi a Gerardin, anakwanitsa kuchepetsako motowo. Dalaiva wa galimoto imene inachita ngoziyo anali atapsinjika pansi pa galimotoyo koma a Gerardin ndi anthu ena anakankha galimotoyo n’kumupulumutsa.

A Gerardin anati: “Kenako motowo unayambiranso kuyaka.” Koma munthu wina amafunikabe kupulumutsidwa. Zili choncho, munthu winanso wozimitsa moto amene anali patchuthi anafika pamalowa ndipo anali atavala zovala zimene munthu amavala akamayendetsa njinga ya moto. A Gerardin ananena kuti: “Ndiyeno ndinamuuza kuti galimotoyi ikhoza kuphulika nthawi iliyonse. Choncho tinagwira manja a munthuyo n’kumukokera kunja.” Mphindi imodzi isanathe, galimotoyo inaphulikadi.

Kenako gulu la anthu ozimitsa moto linafika pamalowo n’kuzimitsa motowo. Panafikanso anthu a zachipatala omwe anathandiza anthu ovulalawo. Nawonso a Gerardin anathandizidwa ndi a chipatala popeza anachekeka komanso kupsa m’manja. A Gerardin akukakwera basi ija kuti apitirize ulendo wawo wa ku msonkhano, anthu ambiri ankawathamangira kwinaku akuwathokoza chifukwa choyesetsa kuthandiza anthu pangoziyo.

A Gerardin anasangalala kwambiri kuti anathandiza pa nthawi ya ngoziyo. Iwo anati: “Ndinaona kuti ndinali ndi udindo wothandiza anthuwo ndipo ndikanakhala ndi mlandu kwa Yehova ndikanangopitiriza ulendo wanga. Ndimayamikira kwambiri kuti ndinakwanitsa kuthandiza kuti anthuwo apulumuke.”