Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ntchito Imene Inathandiza Anthu Kuti Asadziphe

Ntchito Imene Inathandiza Anthu Kuti Asadziphe

M’dera la Tabasco lomwe lili m’dziko la Mexico, chiwerengero cha anthu omwe amadzipha ndi chokwera kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, m’chaka cha 2017 a Mboni za Yehova anakonza zoti kwa miyezi iwiri, agwire ntchito yapadera yogawiranso magazini ya Galamukani! ya April 2014, ya mutu wakuti, “Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?” Anthu ambiri anayamikira kwambiri ntchito yapaderayi.

Anathandizidwa pa Nthawi Yoyenera

A Faustino omwe ndi a Mboni za Yehova, anagwira nawo ntchito yogawira magaziniyi. Iwo anacheza ndi mayi wina yemwe ankadandaula za mwana wake wamwamuna wa zaka 22. Mnyamatayo ankadwala matenda ovutika maganizo ndipo ankafuna kudzipha. Mayiyu sankadziwa mmene angathandizire mwana wakeyo. Ndiyeno a Faustino atamupatsa magaziniyi, iye anati, “Magaziniyi imuthandiza kwambiri mwana wanga.” Tsiku lotsatira, a Faustino anapita kukakumana ndi mnyamatayo ndipo anakambirana naye malangizo a m’Baibulo omwe anafotokozedwa m’magaziniyi. Atacheza naye kangapo, mnyamatayu anaoneka kuti wayamba kusintha kwambiri. A Faustino anati, “Panopa akuoneka womasuka komanso wosangalala kwambiri.” Kuwonjezera pamenepa, iye amafotokozeranso zimene amaphunzirazo mchimwene wake amenenso amadwala matenda ovutika maganizo.

Mtsikana wina dzina lake Karla, yemwe amakhala mu mzinda wa Huimanguillo anagwiritsa ntchito magaziniyi pothandiza mnzake wa m’kalasi. Karla anati: “Ndinazindikira kuti mtsikana wina wa zaka 14 akuoneka wosasangalala. Ndiye nditayankhula naye anandifotokozera zomwe zikuchitika m’banja lawo. Tikucheza choncho, ndinaona kuti ali ndi zipsera padzanja lake lamanzere.” Mtsikanayu anauza Karla kuti ali ndi chizolowezi chodzicheka m’manja ndi m’miyendo. Iye ankadziona kuti ndi wosaoneka bwino komanso wachabechabe. Choncho Karla anamupatsa magazini ya Galamukani! ndipo ataiwerenga, mtsikanayu anauza Karla kuti magaziniyi ikungokhala ngati analembera iyeyo. Akumwetulira, iye ananena kuti tsopano wayamba kuona zifukwa zomuchititsa kukhalabe ndi moyo.

Bambo wina wa mu mzinda wa Villahermosa anasowa mtengo wogwira chifukwa ntchito yake inali itatha komanso mkazi wake ndi ana ake anamuthawa. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize komabe ankaona kuti zinthu sizingasinthe pamoyo wake ndipo anaganiza zongodzipha. Koma atangotsala pang’ono kudzipha, a Martín ndi a Miguel omwe ndi a Mboni za Yehova anagogoda pakhomo pake. Bamboyu atatsegula chitseko, a Mboniwo anamupatsa magazini ya Galamukani! Iye ataona mutu wa magaziniyo, anangoona kuti Mulungu wayankha pemphero lake. A Martín ndi a Miguel anamulimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo ndipo patatha masiku angapo anapitanso kukamuona. Pa nthawiyi anam’peza akuoneka kuti mtima wake uli m’malo komanso ali wodekha. Panopa amaphunzira naye Baibulo kawiri mlungu uliwonse.

Akaidi Anamva Uthenga Wabwino

Pamene ankagwira ntchito yapaderayi, a Mboni anapitanso m’ndende zosiyanasiyana za m’dera la Tabasco. Iwo anachita zimenezi n’cholinga choti akafotokozere akaidi malangizo a m’Baibulo omwe angawathandize kuti aziona kuti moyo ndi wofunika. A Mboniwo anaonetsa mavidiyo, anakamba nkhani yochokera m’Baibulo, komanso anakambirana ndi akaidiwo mfundo zomwe zili m’magaziniyi zothandiza munthu kuona zifukwa zopitirizira kukhala ndi moyo. Akaidiwo komanso ogwira ntchito m’ndendezi anayamikira zimene a Mboni anachitazi. Mwachitsanzo, mkaidi wina ananena kuti: “Ndakhala ndikufuna kudzipha maulendo atatu. Anthu ena anandiuza kuti Mulungu amandikonda, koma sanandisonyezepo umboni wa zimenezi kuchokera m’Baibulo. Zimene mwanenazi zandilimbikitsa kwambiri.”

Anthu ambiri anadziwa za ntchito imene a Mboni ankagwirayi. Mlembi wa boma pa nkhani za umoyo anayamikira a Mboni chifukwa choyesetsa kuthandiza anthu a m’deralo. Ndipo nyuzipepala ina ya m’dzikolo inalemba nkhani yokhudza ntchito imene a Mboni anagwirayo. Mutu wa nkhaniyo unali wakuti: “Amathandiza Anthu Kuti Asadziphe.”