Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni za Yehova Anathandiza Pantchito Yoyeretsa Nkhalango Pafupi ndi Mzinda wa Lviv

A Mboni za Yehova Anathandiza Pantchito Yoyeretsa Nkhalango Pafupi ndi Mzinda wa Lviv

Pa 6 May, 2017, a Mboni za Yehova pafupifupi 130 anathandiza pantchito yoyeretsa Nkhalango ya Bryukhovych yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Lviv ku Ukraine. A Mboniwa anali a zaka zapakati pa 22 mpaka 80, ndipo amakhala komanso kugwira ntchito mongodzipereka pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova yomwe ili pafupi ndi nkhalangoyi. Iwo anagwira ntchitoyi kwa maola atatu ndipo anayeretsa malo okwana mahekitala 50 komanso kutola zinyalala zokwana makilogalamu 600.

Malinga ndi zimene a Mykhailo Splavinskyi ananena, omwe ndi katswiri wokonza zinthu ku Lviv Forest Breeding and Drilling Center, “a Mboni za Yehova anali oyambirira kuthandiza pantchito yoyeretsa nkhalangoyi yomwe imachitika chaka chilichonse, ndipo akhala akuchita zimenezi kuyambira mu 2014.”

Chifukwa Chake Nkhalangoyi Inkafunika Kuyeretsedwa

A Splavinskyi ananena kuti: “Pali njira ziwiri zimene zimachititsa kuti zinyalala zidzadze m’nkhalangoyi. Yoyamba, anthu ena sachotsa zinyalala akamaliza kugwira ntchito. Yachiwiri, zinthu zimene zatsala pantchito yomanga zimabweretsedwa m’nkhalango muno pamagalimoto kudzazitaya.”

Zinyalala ndi vuto lalikulu m’nkhalangoyi. A Splavinskyi ananena kuti: “Zinyalala zimatenga nthawi yaitali kuti ziwole.” Kenako zinyalalazi “zimakaipitsa madzi omwe ali pansi panthaka, ndipo izi zimachititsa kuti zamoyo zina zivutike.” Magalasi amene atayidwa m’nkhalangoyi amachititsa kuti mphamvu ya dzuwa ikafika pamagalasiwa, magalasiwa azitentha kwambiri zomwe zimayambitsa moto m’nkhalangoyi. Komanso magalasi osweka ndi masingano akuchipatala omwe amatayidwa m’nkhalangoyi, ndi oopsa kwambiri makamaka kwa ana aang’ono. A Splavinskyi ananenanso kuti: “Mavuto onsewa akhoza kupeweka zinyalala zikamachotsedwa.”

Kuyeretsa nkhalangoyi yomwe ndi yayikulu mahekitala 3,300 si ntchito yophweka. A Splavinskyi anafotokoza kuti: “Tili ndi alonda 5 okha a boma omwe amalondera nkhalangoyi, ndiye sitingakwanitse kuyeretsa malo aakulu kwambiri chonchi. Choncho timapempha anthu kamodzi pachaka kuti adzatithandize kuyeretsa nkhalangoyi.”

Ntchito Yotolera, Kusankha, Komanso Kutaya Zinyalala

A Mboni omwe adzipereka kugwira nawo ntchito yoyeretsa nkhalangoyi, amatolera zinthu monga mabotolo, matayala a galimoto, magalasi, zitsulo, mapepala, zinthu zapulasitiki, komanso masingano akuchipatala. Iwo amagwiritsa ntchito magulovesi, matumba a pulasitiki ndi zipangizo zina pogwira ntchitoyi. A Ihor Fedak, omwe amagwira ntchito yosamalira nkhalangoyi anati: “Malo omwe ayeretsedwa ndi a Mboni za Yehova amakhala ooneka bwino kwambiri.”

A Mboni akatolera zinyalalazi, amazisankha n’kuziika m’magulu osiyanasiyana monga magalasi, mapepala, komanso zinthu zapulasitiki, zomwe zingathe kugwiritsidwanso ntchito. Iwo amachita zimenezi ngakhale kuti palibe lamulo lonena zimenezi. Kampani ina yotaya zinyalala ndi imene imamalizitsa ntchito yotaya zinyalalazi. Kuyambira mu 2016, a Mboni amalipira ndalama zotayira zinyalala zimene amatolerazi. A Fedak ananena kuti: “Tikuthokoza a Mboni za Yehova chifukwa amatithandiza kwambiri.”

“Ntchitoyi Si Yonyozeka Kwa Ine”

A Mboni amasangalala kugwira nawo ntchito ya pachaka yoyeretsa nkhalangoyi. Iwo amasangalala kuthandiza pantchito yomwe cholinga chake ndi kuthandiza anthu a m’dera lawo komanso kukhala ndi nkhalango yaukhondo. A Volker anafotokoza maganizo omwe a Mboni enanso ali nawo. Iwo anati: “Ntchitoyi si yonyozeka kwa ine. Ukamathandiza anthu ena zimasonyeza kuti umawalemekeza ndipo ndimamva bwino ndikamachita zimenezi.”

A Anzhelika anawonjezera kuti: “Ineyo sindimangoganizira za amene anataya zinyalalazo, koma ndimaona kuti chinthu chofunika kwambiri n’kuona zimene ndingachite kuti ndizichotse.” A Lois omwe ali ndi zaka 78, anagwira nawo ntchito yoyeretsa nkhalangoyi. Iwo anati: “M’malo mokhumudwa ndi zinyalala ukapita kukayenda m’nkhalangoyi, ndi bwino kungozichotsa n’kuzitaya.”

A Wieslaw ananena kuti: “Nthawi zambiri anthu amationa titatchena komanso titavala matayi n’kumalalikira. Koma timakhalanso okonzeka kugwira nawo mwakhama ntchito yoyeretsa nkhalango ndi ntchito zina zothandiza anthu.”