Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni za Yehova Analimbikitsa Anthu ku France

A Mboni za Yehova Analimbikitsa Anthu ku France

Kuyambira pa 2 mpaka pa 24 July, 2016, ku France kunachitika mpikisano wa njinga wa nambala 103, koma pa nthawiyi anthu anali ndi mantha kwambiri. Zinali choncho chifukwa mu chaka cha 2015, m’dziko la France munachitika za uchigawenga maulendo angapo ndipo anthu opitirira 100 anaphedwa. Kenako pa 14 July, 2016, lomwe linali tsiku la holide, anthu ambirimbiri ankaonerera kuphulitsidwa kwa makombola mumzinda wa Nice ndipo chigawenga china chinayendetsa galimoto pamalopo n’kuponda ena mwa anthuwo. Anthu 86 anamwalira komanso ena ambiri anavulala.

Komabe, a Mboni za Yehova anali ofunitsitsa kutonthoza ndi kulimbikitsa anthu omwe anali ndi mantha komanso chisoni pa nthawi yovutayi. Choncho anaika mashelefu a mabuku m’malo osiyanasiyana kumalo ochitira mpikisanowu. A Mboni za Yehova opitirira 1,400 anadzipereka kuti agwire nawo ntchito yolalikirayi ndipo anapereka mabuku opitirira 2,000 kwa anthu omwe anali ndi mafunso ambirimbiri okhudza moyo.

‘Komatu Nde Muli Paliponse!’

Anthu amene ankatsatira ochita mpikisanowu anadabwa kuwona kuti kulikonse komwe apita kuli a Mboni za Yehova. Ena mwa anthu omwe an’kayang’anira mpikisanowu anathokoza a Mboni chifukwa chochita zinthu mwadongosolo ndipo ananena kuti: “Zikuoneka kuti pa nthawi ya mpikisanoyi munali paliponse!” Anthu enanso ambiri ankanena mokweza kuti: “Kunonso kuli a Mboni za Yehova!” Kwa masiku angapo dalaivala wina wa basi ankakana a Mboni ena akafuna kumupatsa kapepala ndipo ankawayankha kuti analandira kale timapepala 4.

Anthu ena anatenga mabuku pa timashelefuti koyamba chifukwa chochita chidwi ataona kuti a Mboni amakonda kupezeka pamalo a mpikisanowu. Mwachitsanzo, munthu wina wogwira ntchito ku siteshoni ya wailesi yakanema anakumbukira kuti chaka chatha anaonanso a Mboni pamalo a mpikisanowu. Ndiye ataona kuti abweranso anaganiza zopita pamene panali kashelefu kamabuku n’kutenga buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja chifukwa lili ndi nkhani zimene iyeyo ankafuna. Munthuyu anawerengako bukuli ali m’galimoto ndipo anauza anzake omwe amagwira nawo ntchito za timashelefu tamabukuti ndipo nawonso anakatenga mabuku osiyanasiyana.

Uthenga Wothandiza Kuti Anthu Akhale ndi Chiyembekezo

Alendo enanso amene anabwera kumwambowu anafufuza a Mboni ndipo atawapeza anawamasukira n’kuwauza zakukhosi kwawo. Mayi wina wachitsikana anauza a Mboni kuti ankaona kuti alibe tsogolo moti tsiku limeneli ankafuna kudziponya panjanji kuti sitima ingomupha. Koma atamva uthenga wa m’Baibulo womwe ndi wolimbikitsa komanso wonena za mtendere umene anthu adzapeze mu Ufumu wa Mulungu, anasiyiratu maganizo ofuna kudzipha aja. Mayi winanso anauza a Mboni kuti: “Pitirizani kugwira ntchito yabwinoyi!”

Bambo wina wolumala ananena kuti amakaikira munthu aliyense wachilendo, koma analola kuti mayi wina amuthandize chifukwa anamuuza kuti ndi wa Mboni. Bamboyu anati: “Zikomo chifukwa chomwetulira komanso kuvala mwaulemu. Munthu sangakukaikire ngakhale pang’ono.”