Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni za Yehova Analandira Satifiketi Yaulemu Chifukwa Choteteza Chilengedwe

A Mboni za Yehova Analandira Satifiketi Yaulemu Chifukwa Choteteza Chilengedwe

Anthu a Mboni za Yehova omwe akugwira ntchito kufakitale yosindikiza mabuku ku Mexico alandira satifiketi yaulemu kuchokera ku boma chifukwa choteteza chilengedwe. Ndipo a Mboniwa akhala akulandira satifiketiyi kwa zaka 7 zotsatizana.

Pa September 26, 2012, boma la Mexico linapereka satifiketi yaulemu yapadera kwambiri kwa Mboni za Yehova chifukwa a Mboniwo “amadzipereka kwambiri pa ntchito yoteteza chilengedwe.”

Boma la Mexico linayambitsa mwambo womwe cholinga chake n’kuthandiza makampani ndi mafakitale kuti azitsatira mfundo zothandiza kuti asamawononge chilengedwe. Chaka chilichonse, a Mboni za Yehova amapezeka pamwambowu ngakhale kuti bungwe lawo si la bizinezi. Mneneri wa fakitale yawo ku Mexico anati: “Kuti kampani kapena fakitale ipatsidwe satifiketiyi, imafunika kukwanitsa mfundo zonse 7 zofunikira. Imafunika kuti isamawononge mpweya, madzi, isamataye zinyalala mwachisawawa, isamatulutse mpweya kapena mankhwala owopsa, izitsatira mfundo zothandiza kupewa ngozi, izigwiritsa ntchito bwino mphamvu zamagetsi ndiponso iziphunzitsa anthu ake mmene angatetezere chilengedwe. Sikuti boma limakakamiza makampani ndi mafakitale kuti azipezeka pamwambowu ayi. Ife timapezeka pamwambowu mwakufuna kwathu.”

A Mboni za Yehova padziko lonse lapansi amayesetsa kuchita zinthu zoti asamawononge zinthu za chilengedwe zomwe ndi zamtengo wapatali.