Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuthandiza Anthu Othawa Kwawo Omwe Ali ku Central Europe

Kuthandiza Anthu Othawa Kwawo Omwe Ali ku Central Europe

M’zaka zaposachedwapa anthu ambiri omwe anathawa mavuto osiyanasiyana ku Africa, ku Middle East ndi ku South Asia, anapita ku Europe. Pofuna kuwathandiza, mabungwe ogwira ntchito limodzi ndi boma komanso anthu ena odzipereka, akuyesetsa kuwapezera chakudya, malo okhala komanso thandizo la kuchipatala.

N’zoona kuti anthu othawa kwawo amafunika zinthu ngati zimenezi. Koma ambiri amafunika kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kukhala ndi chiyembekezo chifukwa amakhala ndi mantha komanso amavutika maganizo. A Mboni za Yehova a ku Central Europe, akuyesetsa kuchita zimenezi powapezera zinthu zofunika komanso kuwalimbikitsa. Iwo amawamvetsera akamafotokoza mavuto awo ndipo amawalimbikitsa ndi uthenga wa m’Baibulo.

Analimbikitsidwa ndi Uthenga wa M’Baibulo

Kuyambira mu August 2015, a Mboni ochokera m’mipingo yoposa 300 ku Austria ndiponso ku Germany, akuyesetsa kulimbikitsa anthu amenewa. A Mboniwa amaona kuti anthuwa amasangalala kwambiri kukambirana nawo mayankho ochokera m’Baibulo pa mafunso ngati awa:

  • N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambirimbiri?

  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

  • Kodi m’Baibulo muli uthenga wotani?

  • Kodi Mulungu ali ndi dzina?

  • Kodi a Mboni za Yehova ndi anthu otani?

Kuyambira m’mwezi wa August mpaka mu October 2015, a Mboni okhala m’derali anaitanitsa mabuku okwana matani 4 ku nthambi ya ku Central Europe ndipo anagawira mabukuwa kwaulere kwa anthu omwe anathawa kwawo.

Kuthana ndi Vuto Losiyana Chinenero

Ambiri omwe amakhala pakampu ya anthu othawa kwawowa, amalankhula zinenero za kumayiko awo. Pofuna kulankhula ndi anthuwa, a Mboni amagwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org, pomwe pamapezeka nkhani ndi mavidiyo a m’zilankhulo zambirimbiri. Matthias ndi Petra omwe amachokera mumzinda Erfurt ku Germany, anadzipereka kudzathandiza anthuwa. Banjali linafotokoza kuti: “Nthawi zina timalankhula nawo pogwiritsa ntchito manja ndi zithunzi.” A Mboni amagwiritsanso ntchito pulogalamu yophunzitsa chinenero ya JW Language kuti alalikire anthuwa m’chinenero chawo. Enanso amagwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Library yomwe imapezeka m’zinenero zambiri, pofuna kuwerenga malemba komanso kuonetsa anthuwo mavidiyo a m’chinenero chawo.

Anasangalala Kwambiri ndi Mabuku Athu

Banja lina la Mboni lochokera mumzinda wina wotchedwa Schweinfurt ku Germany, linanena kuti: “Tsiku lina tikulalikira anthuwa anachita kutizungulira moti pamene pankatha maola awiri ndi hafu, n’kuti titagawira anthuwo mabuku ndi magazini okwana 360. Ambiri ankati akalandira mabukuwo, ankaweramitsa mitu yawo posonyeza kutithokoza.” A Wolfgang amene kwawo ndi m’tauni ya Diez ku Germany anadzipereka kukathandiza anthu othawa kwawo. Iwo ananena kuti: “Anthuwa amasangalala akaona kuti pali winawake amene amawaganizira. Nthawi zina amatipempha kuti tiwabweretsere mabuku a m’zinenero 5 kapena 6.”

Ambiri ankayambiratu pompo kuwerenga mabuku athu pomwe ena ankabwera kudzatithokoza akamaliza kuwerenga. Wa Mboni wina wochokera mumzinda wa Berlin, ku Germany, dzina lake Ilonca anati: “Anyamata ena awiri anabwera kudzatenga mabuku. Koma patangodutsa 30 minitsi anabwera kudzatipatsa buledi monga mphatso. Iwo ananena kuti panalibenso china chomwe akanatipatsa posonyeza kuthokoza.”

“Zikomo Kwambiri, Tathokoza”

Ogwira ntchito yothandiza anthu pakampuyi, akuluakulu a m’derali komanso anthu a pafupi, akuyamikira a Mboni chifukwa chogwira ntchito yothandiza anthuwa mongodzipereka. Bambo wina wogwira ntchito pamalowa ananena kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa choganizira alendowa.” Wogwira ntchito winanso pakampuyi anayamikira a Mboni chifukwa chopereka mabuku othandiza anthuwo m’chinenero chawo. Iye ananena kuti akuyamikira chifukwa anthuwa “akalandira chakudya cha m’mawa, masana ndi madzulo, basi sakhalanso ndi zochita zina.”

A Marion ndi amuna awo a Stefan, omwe amakhala ku Austria anauza apolisi omwe anabwera kudzayendera malowa za cholinga cha ntchito yawo. Apolisiwo anawathokoza kwambiri ndipo anawapempha mabuku awiri. A Marion anati: “Apolisiwo anatithokoza mobwerezabwereza chifukwa cha ntchito yathu.”

Mayi wina wa ku Austria, amene amakonda kupereka katundu kukampuyi, ankaona kuti a Mboni ankabwerabe kudzathandiza anthuwa kaya nyengo ikhale yotani. Tsiku lina mayiyu anauza a Mboniwa kuti: “N’zoona kuti anthuwa amafuna chakudya, malo okhala komanso zinthu zina, koma chimene amafuna kwambiri ndi kuwathandiza kukhala ndi chiyembekezo, ndipo n’zimene inuyo mukuchita.”