Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuthandiza Anthu Amene Ali M’ndende

Kuthandiza Anthu Amene Ali M’ndende

Tsiku lililonse, anthu amene ali m’ndende m’dziko la United States of America amalemba makalata opita kumaofesi a Mboni za Yehova, opempha kuti athandizidwe kuti adziwe zimene Baibulo limaphunzitsa.

Pofuna kuthandiza anthuwa, timakonza dongosolo lakuti anthu ena a Mboni za Yehova a mumpingo wa m’deralo, azikathandiza anthu m’malo ngati kundende, m’zipatala, m’malo a achinyamata komanso kumalo othandizirako anthu omwe ali ndi vuto logwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Kundende zina, anthu a Mboni za Yehova amenewo nthawi zonse amachititsa misonkhano ya mpingo. Mwachitsanzo, kundende ina anthu okwana 32 anasonkhana n’kumvetsera nkhani ya onse imene inakambidwa pamabwalo awiri a ndendeyo.

Ntchito imeneyi ikubereka zipatso zabwino. Mwachitsanzo, munthu wina amene ali m’ndende ina ku Indiana, yemwe anaweruzidwa kuti akhale m’ndende moyo wake wonse chifukwa chopezeka wolakwa pa mlandu wakupha, anasintha kwambiri mpaka anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Pali munthu winanso amene ali m’ndende ina yoopsa kwambiri ku California. Ponena za munthu ameneyu, wa Mboni amene anaphunzira Baibulo ndi munthuyo anati: “Ndikudziwa kumene munthuyu wachokera komanso mmene wasinthira. Wasintha kwambiri kuti ayenerere kubatizidwa.

Anthu ambiri amene ali m’ndende avomereza kuphunzira mfundo zoona za m’Baibulo ngakhale kuti akudziwa kuti zimene asankhazo zikhoza kuchititsa kuti moyo wawo ukhale pangozi m’ndendemo. Mwachitsanzo, anthu ena amene asintha n’kusiya kugwirizana ndi timagulu ta anthu ovuta kwambiri m’ndendemo afika posamutsidwira kundende zina kapena kuikidwa kumalo kwaokha n’cholinga choti asavulazidwe kapena kuphedwa kumene ndi anzawo.

Uthenga wa m’Baibulo ndi wamphamvu kwambiri ndipo umasintha anthu. Akuluakulu ena oyang’anira ndende akhala akugoma akaona akaidi ovuta kwambiri atasintha chifukwa chophunzira Baibulo. Akuluakulu ena afika popereka masatifiketi aulemu kwa anthu a Mboni za Yehova amene amaphunzira Baibulo ndi anthuwo.