Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Webusaiti ya JW.ORG Ikuthandiza Anthu Kwambiri

Webusaiti ya JW.ORG Ikuthandiza Anthu Kwambiri

Padziko lonse anthu akupindula kwambiri ndi webusaiti ya jw.org. Pansipa, pali mawu oyamikira amene anthu ena anatumiza ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova kuyambira nthawi imene webusaitiyi inakhazikitsidwa kufika mu May 2014.

Ikuthandiza Ana Aang’ono

“Nthawi zambiri mwana wanga wa kumkaka ankabwera kusukulu atatenga mapensulo, zidole komanso magalasi a anzake. Tinayesetsa kumuthandiza mobwerezabwereza kuti amvetsetse kuti zimene amachitazo m’chimodzimodzi ndi kuba ndipo kuba n’koipa. Koma zimenezi sizinaphule kanthu. Kenako tinapanga dawunilodi vidiyo yakuti Kuba N’koipa yomwe ili pa jw.org. Vidiyoyi inathandiza kwambiri mwana wathu. Ataionera anamvetsa kuti Mulungu amadana ndi kuba, moti ananena kuti akabweza zinthu zonse kwa anzakewo. N’saname, webusaitiyi yatithandiza kwambiri.”​—D. N., Africa.

“Vidiyo yakuti Kuba N’koipa yomwe ili pa jw.org . . . inathandiza kwambiri mwana wathu”

“Ana anga amaikonda kwambiri webusaitiyi. Amapanga dawunilodi timavidiyo tamakatuni timene timawathandiza kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo zokhudza kunama ndi kuba. Amaphunziranso makhalidwe abwino amene angawathandize pamoyo wawo wonse ndipo zimenezi zimapangitsa kuti akhale ana osiririka.”​—O. W., West Indies.

Ikuthandiza Ana a Sukulu

“Sukulu sinkandisangalatsa moti ndinaganiza zongoisiya. Koma tsiku lina ndinawerenga nkhani yakuti “Kodi Ndisiye Sukulu?” pa webusaiti ya jw.org. Nkhaniyi inandithandiza kuti ndizikonda sukulu. Ndinaphunziranso kuti sukulu indithandiza kuti ndikonze tsogolo langa komanso kuti ndidzakhale munthu wodalirika.”​—N. F., Africa.

“Malangizo othandiza achinyamata omwe ali pa webusaitiyi andiphunzitsa zimene ndingachite kuti ndipitirize kukhala ndi makhalidwe abwino kusukulu”

“Malangizo othandiza achinyamata omwe ali pa webusaitiyi andiphunzitsa zimene ndingachite kuti ndipitirize kukhala ndi makhalidwe abwino kusukulu. Ndaphunzira zimene ndingachite kuti ndiziika maganizo anga pa maphunziro komanso kupewa zimene zingandisokoneze.”​—G., Africa.

“Mnzanga wa kuntchito anadandaula kuti mwana wake wamkazi ankavutitsidwa kusukulu ndi mtsikana winawake. Zimenezi zinkasokoneza kwambiri mwana wakeyu moti kwa masiku angapo sanapite kusukulu chifukwa choopa. Nditakambirana ndi mnzangayu mfundo zimene zili mu vidiyo yakuti Beat a Bully Without Using Your Fists, yomwe ili pa jw.org, anasangalala kwambiri ndi malangizo akuti si bwino kubwezera anthu akamakuvutitsa. Kenako anakakambirana ndi mwana wake zimene angachite anthu akamamuvutitsa. Zimenezi zinathandiza mwanayo kuti asamaopenso kupita kusukulu. Patapita nthawi mtsikana uja anasiya kumuvutitsa moti ankatha kucheza naye.”​—V. K., Eastern Europe.

Ikuthandiza Achinyamata

“Zikomo kwambiri chifukwa cholemba nkhani yakuti, ‘N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?’ pa jw.org. Ineyo ndakhala ndikulimbana ndi vuto limeneli kwa nthawi yaitali. Ndinkaganiza kuti ndine ndekha amene ndimachita zimenezi ndiye ndinkaona kuti ndikauza anthu ena sangandimvetse. Zitsanzo zimene zili m’nkhaniyi zinandithandiza kwambiri. Panopa ndaona kuti alipo amene amamvetsa vuto langali.”​—Mtsikana wa ku Australia.

“Zitsanzo zimene zili m’nkhaniyi zinandithandiza kwambiri. Panopa ndaona kuti alipo amene amamvetsa vuto langali”

“Webusaiti ya jw.org yandithandiza kupeza nkhani zothandiza achinyamatafe. Mwachitsanzo, nkhani ina inandithandiza kuzindikira magulu a nkhanza zokhudza kugonana moti ndinazindikira kuti nanenso ndinachitidwapo nkhanza zokhudza kugonana. Ndaphunziranso zimene ndingachite ngati ndingakumane ndi vutoli.”​—T. W., West Indies.

Ikuthandiza Makolo

“Mwana wanga wamwamuna ali ndi matenda omwe amamuchititsa kuti asamakhazikike, azisangalala mopitirira malire komanso kuti azichita zinthu mojijirika kwambiri. Zimenezi zinkandithetsa nzeru ndipo zinkapangitsa kuti tisamalankhulane bwino. Tsiku lina ndinapita pa jw.org n’kusankha gawo lofotokoza za mabanja ndi makolo. Ndinapeza nkhani zambiri zogwirizana ndi zimene ndinkakumana nazo ndipo ndinaphunzira zimene ndingachite kuti ndizilankhulana bwino ndi mwana wanga. Iyenso wapindula kwambiri ndi webusaitiyi. Panopa amandiuza momasuka zinthu zimene zikumudetsa nkhawa komanso zimene zikumusangalatsa.”​—C. B., Africa.

“Nthawi zambiri pa jw.org pamapezeka nkhani yogwirizana ndendende ndi vuto limene ana athu akukumana nalo komanso mmene tingalithetsere”

“Webusaiti ya jw.org yathandiza makolofe kuphunzitsa ana athu m’njira yosangalatsa kwambiri. Mwachitsanzo, vidiyo yamakatuni ojambula yokhudza kupeza anthu abwino ocheza nawo yathandiza ana athu kuti asamangosankha anzawo mwachisawawa, koma kuti azisankha anthu abwino omwe angawathandize kukhala ndi makhalidwe abwino. Nthawi zambiri pa jw.org pamapezeka nkhani yogwirizana ndendende ndi vuto limene ana athu akukumana nalo komanso mmene tingalithetsere. Kunena zoona, jw.org ndi nkhokwe ya malangizo othandiza.”​—E. L., Europe.

Ikuthandiza Anthu Apabanja

“Ine ndi mkazi wanga takhala m’banja kwa zaka 6. Mofanana ndi mabanja onse, ifenso takhala tikuyesetsa kuti tizolowerane pa nkhani ya kulankhulana bwino, mmene tinaleredwera komanso mmene timaonera zinthu. Nditatsegula webusaiti ya jw.org, ndinachita chidwi ndi nkhani yakuti ‘Kodi Mungatani Kuti Muzimvetsera Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akamalankhula?’ Nkhaniyi ili ndi mfundo zomwe zingathandize kuti anthu okwatirana azimvetserana. Ndinakambirana mfundo za m’nkhaniyi ndi mkazi wanga ndipo tinayamba kutsatira zimene tinakambiranazo.”​—B. B., West Indies.

“Kupanda webusaitiyi banja langa bwenzi litatha”

“Ndakhala ndikusonkhana ndi a Mboni za Yehova kwa chaka chimodzi tsopano ndipo ndikufuna kunena mmene webusaiti ya jw.org yandithandizira. Ndaphunzira zambiri pa webusaitiyi monga zimene ndingachite kuti ndiziugwira mtima komanso kuti ndikhale mwamuna komanso bambo wabwino. Kunena moona mtima, kupanda webusaitiyi banja langa bwenzi litatha.”​—L. G., West Indies.

Ikuthandiza Anthu Ovutika Kumva

“Webusaiti ya jw.org yandithandiza kuti ndizidziona kuti ndine munthu ngati wina aliyense. Mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku America andithandiza kuti ndidziwe kwambiri chinenero chamanja. Ndinkadziona kuti sindingakhale ndi zolinga zothandiza pamoyo. Koma nditaonera vidiyo yakuti Seeing God’s Word in My Language, ndinakhudzika mtima kwambiri ndipo ndinayamba kuganizira kwambiri zinthu zabwino zokhudza moyo wanga.”​—J. N., Africa.

“Webusaiti ya jw.org yandithandiza kuti ndizidziona kuti ndine munthu ngati wina aliyense”

“Webusaiti ya jw.org, ndi chida chothandiza kwambiri. Ndimagwira ntchito yongodzipereka yothandiza anthu ovutika kumva, makamaka achinyamata. Zinthu zankhaninkhani za m’chinenero chamanja zomwe zili pa webusaitiyi zandithandiza kuti nanenso ndidziwe kwambiri chinenero chamanja. Ndadziwanso mmene ndingathandizire anthu amene akukumana ndi mavuto am’banja komanso amene akufuna kupeza mabwenzi abwino.”​—K. J., West Indies.

Ikuthandiza Ovutika Kuona

“Ndine wakhungu ndipo webusaiti ya jw.org yandithandiza kwambiri. Yandithandiza kudziwa zinthu zomwe zikananditengera miyezi yambiri kuti ndizidziwe. Yathandizanso kuti zinthu ziziyenda bwino m’banja mwathu komanso kuti ndikhale munthu wodalirika m’dera la kwathu. Chinanso n’choti webusaitiyi yapangitsa kuti ndizidziwa zinthu pa nthawi yofanana ndi anzanga omwe savutika kuona.”​—C. A., South America.

“Yathandizanso kuti zinthu ziziyenda bwino m’mbanja mwathu komanso kuti ndikhale munthu wodalilira m’dera la kwathu”

“Kwa anthu amene satha kuwerenga zilembo za akhungu kapena sangakwanitse kugula mabuku a zilembozi, jw.org ndi chuma cha mtengo wapatali. Munthu wakhungu akhoza kumvetsera nkhani zimene zajambulidwa ndipo zimenezi zingamuthandize kuti adziwe zinthu zambiri. Webusaitiyi inakonzedwa mwanjira yoti anthu onse azitha kugwiritsa ntchito, mosatengera kuti anthuwo ndi otani. Mwachitsanzo, anthu osaona ngati ineyo yatithandiza kudziona kuti ndife ofunika komanso kuti tizidziwa zinthu mofanana ndi anthu ena onse.”​—R. D., Africa.

Ikuthandiza Anthu Ofuna Kudziwa Mulungu

“Webusaiti yanu ndi yosiyana ndi mawebusaiti a zipembedzo zina chifukwa nkhani zake sizikhala ndi mawu ovuta a chipembedzo omwe ansembe okha ndi omwe angawamvetse. Komanso siifotokoza zinthu zambirimbiri nthawi imodzi moti iwe mpaka kulephera kuzilumikiza. Webusaiti yanuyi ndi yosavuta komanso imanena zinthu momveka bwino. Chinanso n’choti sipangitsa munthu kuona kuti n’zovuta kudziwa Mulungu komanso kumukhulupirira. Koma imathandiza munthu aliyense kudziwa kuti akhoza kukhulupirira Mulungu.”​—A. G., Asia.

“Webusaiti yanuyi ndi yosavuta komanso imanena zinthu momveka bwino . . . Imathandiza munthu aliyense kudziwa kuti akhoza kukhulupirira Mulungu”

“Ndikanakhala ndani ine kupanga jw.org. Webusaitiyi ili ngati kuwala kondiunikira m’dziko la m’dima wauzimuli. Ndimatha kupeza mosavutikira nkhani zofotokoza maganizo a Mulungu pa nkhani zosiyanasiyana komanso ndimapeza mayankho a mafunso ambiri okhudza moyo.”​—J. C., West Indies.

“Ndikuyamikira zinthu zonse zondithandiza kudziwa Mulungu zomwe ndimazipeza ngakhale kuti ndimakhala kumidzi ya ku South America. Sindikanadziwa Mulungu kupanda webusaitiyi.”​—M. F., South America.