Pitani ku nkhani yake

A Mboni za Yehova Amaphunzitsa Makolo ndi Ana Mmene Angapewere Anthu Ogwiririra Ana

A Mboni za Yehova Amaphunzitsa Makolo ndi Ana Mmene Angapewere Anthu Ogwiririra Ana

Baibulo limanena kuti makolo ayenera kukonda ana awo, kuwatsogolera, kuwateteza komanso kumawaona kuti ndi mphatso imene Mulungu anawapatsa. (Salimo 127:3; Miyambo 1:8; Aefeso 6:1-4) Masiku ano kukuchitika zinthu zoopsa zambiri monga kugwiririra ana. Choncho makolo ayenera kuyesetsa kuteteza ana awo kwa anthu oterewa.

Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akulemba komanso kufalitsa nkhani zimene zimathandiza kuti aliyense azisangalala m’banja. Akhalanso akutulutsa nkhani zimene zimathandiza makolo kuteteza ana awo kwa achidyamakanda komanso kuwaphunzitsa zokhudza anthu ogwiririra ana. M’munsimu muli zina mwa nkhani zimene a Mboni za Yehova atulutsapo zimene zili ndi malangizo othandiza okhudza kuteteza ana kwa achidyamakanda. Tasonyezanso kuchuluka kwa magazini ndi mabuku komanso zinenero zimene nkhanizi zinatulutsidwa. *

 • Mitu: Minkhole Yopanda Liŵongo ya Kuchitira Nkhanza Ana; Mabala Obisika a Kuchitira Nkhanza Ana

  • Magazini: Galamukani! ya October 8, 1991

  • Omwe anasindikizidwa: 12,980,000

  • Zinenero: 64

 • Mitu: Mwana Wanu Ali Paupandu!; Kodi Tingatetezere Motani Ana Athu?; Chitetezo m’Nyumba

  • Magazini: Galamukani! ya October 8, 1993

  • Omwe anasindikizidwa: 13,240,000

  • Zinenero: 67

 • Mutu: Mmene Yesu Anatetezedwera

  • Buku: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, mutu 32 linafalitsidwa mu 2003

  • Omwe anasindikizidwa: 39,746,022

  • Zinenero: 141

 • Mitu: Nkhani Imene Ikudetsa Nkhawa Kwambiri Makolo; Mmene Mungatetezere Ana Anu; Tetezani Ana M’Banja Lanu

  • Magazini: Galamukani! ya October 2007

  • Omwe anasindikizidwa: 34,267,000

  • Zinenero: 81

 • Mitu: Kodi Ndingadziteteze Bwanji kwa Anthu Ogwiririra?; Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa: Kodi Ndizikambirana ndi Mwana Wanga Nkhani Zogonana?

  • Buku: Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa Buku Loyamba Mutu 32 ndi Zakumapeto, lofalitsidwa mu 2011.

  • Omwe anasindikizidwa: 18,381,635

  • Zinenero: 65

 • Mutu: Kodi Makolo Angatani Kuti Aphunzitse Ana Awo Nkhani Zokhudza Kugonana?

  • Ikupezeka pa: Webusaiti ya jw.org, nkhani yomwe inatuluka pa September 5, 2013,

  • Zinenero: 64

A Mboni za Yehova apitiriza kuphunzitsa makolo ndi ana awo kuti atetezeke kwa anthu ogwiririra.

^ ndime 3 Chaka chimene tasonyeza ndi chomwe nkhanizo zinatuluka m’Chingelezi.