Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni Akulimbikitsa ndi Kutonthoza Okalamba

A Mboni Akulimbikitsa ndi Kutonthoza Okalamba

Mofanana ndi mayiko ambiri, ku Australia kuli anthu okalamba ambiri. Ena amakakhala kunyumba zosamalirako anthu okalamba ndipo amasamaliridwa mwachikondi komanso kupatsidwa zofunika za pamoyo wawo ndi chithandizo chamankhwala.

Komatu okalamba ambiri amafunikiranso kuwachitira zambiri kuposa pamenepa. Nthawi zina amaboweka, amasowa wocheza naye kapenanso wowathandiza. Choncho, mlungu uliwonse a Mboni za Yehova amayendera nyumba zosungirako okalamba ziwiri zomwe zili ku Portland, m’tauni ya Victoria ku Australira.

Mfundo za M’Baibulo Zothandiza Anthu Achikulire

A Mboni akafika kumalowa amakambirana nkhani za m’Baibulo ndi kagulu ka okalamba ndipo nkhani zina zimakhala zokhudza zomwe zinachitika m’moyo wa Yesu. A Jason ananena kuti: “Timawerengera okalambawa nkhani inayake ya m’Baibulo kenako timakambirana zomwe tawerengazo.” Ndiye poti ambiri mwa okalambawa amadwaladwala, a Mboni amawalimbikitsa pokambirana nawo zimene Mulungu analonjeza kuti adzachotsa matenda ndi imfa.

A Tony omwe ndi a Mboni za Yehova anati: “Poyamba tinkacheza nawo kwa 30 minitsi koma okalambawa ananena kuti nthawiyi yachepa kwambiri. Moti panopa timacheza nawo kwa ola limodzi ngakhale kuti mayi wina ananena kuti titha kumacheza nawo kwa maola awiri.” Ena mwa achikulirewa ali ndi vuto losaona, sangathe kugwira zinthu ndi manja komanso ena amakhala ali chigonere. Koma a Mboni amawathandiza ndi kuwalimbikitsa kuti pa nthawi yonse imene akukambirana nawo, nawonso azitha kuyankhulapo.

A Mboniwa amathanso kuimba nyimbo zingapo zotamanda Mulungu ndipo okalamba ena amawapempha kuti aimbe nyimbo zambiri. A John, * omwenso amasungidwa kumalowa anati: “Nyimbo zanu timazikonda kwambiri. Zimatithandiza kulemekeza Mulungu komanso kumudziwa bwino.” A Judith omwe ali ndi vuto losaona analoweza mawu a nyimbo zomwe amazikonda.

A Mboni amafuna kuthandiza wokalamba aliyense. A Brian omwe ndi a Mboni anati okalambawa akakhala kuti sakupeza bwino, a Mboni amakawaona m’zipinda zawo. Iwo ananenanso kuti: “Timacheza nawo kuti tione kuti akupezako bwanji. Nthawi zina timatha kupitanso tsiku lotsatira kuti tikaone odwala.”

“Mulungu Ndi Amene Wakutumizani Kuno”

Okalamba ambiri amasangalala a Mboni akapita kukawaona. A Peter omwe amaphunzira ndi a Mboni mlungu uliwonse anati: “Ndikungoona kuchedwa kuti tidzaphunzirenso.” A Judith amauza anthu omwe amawasamalira kuti: “Lero ndi Lachitatu! Musachedwe kundithandiza kukonzekera paja timaphunzira Baibulo. Sindikufuna kuchedwa.”

Okalambawa amakondanso kwambiri zimene akuphunzira ndipo amaona kuti kuphunziraku kukuwathandiza kuyandikira Mulungu. Tsiku lina pambuyo pokambirana zimene Yesu ankaphunzitsa, a Robert anati: “Nkhani imeneyi sindinkaimvetsa. Koma panopa ndaimvetsa!” A David azindikira kuti kupemphera n’kofunika kwambiri ndipo anati: “Kuphunziraku kwandithandiza kuti ndiyambe kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo ndimamuona kuti ndi mnzanga weniweni.”

A Lynette omwenso amasungidwa kumalowa anauza a Mboni kuti: “Zikomo kwambiri potiuza uthenga wotonthozawu kuchokera m’Baibulo.” Wokalamba winanso anati: “Mulungu ndi amene wakutumizani kuno.” Umenewu ndi umboni wosonyeza kuti okalambawa amasangalala kwambiri akamva uthenga wotonthoza wonena za m’tsogolo.

A Margaret amasangalala kwambiri kuphunzira ndi a Mboni ndipo tikunena pano amapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova nthawi zonse. Komatu ndi akhama kwambiri chifukwa amadwaladwala komanso amayenda movutikira. Iwo anauza a Mboni kuti: “Aliyense wa ife mwamuthandiza kudziwa chinthu chofunika kwambiri chimene ayenera kumachita pamoyo.”

‘Mukugwira Ntchito Yabwino Kwambiri’

Ogwira ntchito panyumba zosungira okalambawa amayamikira kwambiri a Mboni chifukwa choyendera anthuwa. Wa Mboni wina dzina lake Anna anati: “Ogwira ntchito pamalowa amalimbikitsa okalamba omwe amawasamalira kuti azibwera kudzaphunzira Baibulo chifukwa aona kuti okalambawa amasangalala kwambiri akaphunzira.” A Brian ananenanso kuti: “Anthu ogwira ntchito pamalowa ndi ochezeka komanso osavuta. Iwo amachita zambiri pofuna kuthandiza.”

Achibale a okalambawa amasangalala kwambiri kuona kuti abale awowa akusangalala ndi zimene akuphunzira. Mwana wamkazi wa mayi ena okalamba anathokoza a Mboni ndipo anawauza kuti: “Mayi anga mukuwachitira zinthu zabwino kwambiri.”

^ ndime 7 Maina a anthu omwe ali ku nyumba zosungirako okalamba tawasintha m’nkhaniyi.