Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

“Ndinu Anthu Achitsanzo Chabwino Kwambiri”

“Ndinu Anthu Achitsanzo Chabwino Kwambiri”

A MBONI ZA YEHOVA a m’tauni ya Saponara, yomwe ili ku Sicily, analandira mendulo yaulemu chifukwa cha ntchito yothandiza anthu yomwe anagwira madzi osefukira otawononga zinthu m’deralo.

Pa November 22, 2011, madzi osefukira oopsa kwambiri anawononga matauni ndi midzi ya m’dera la Messina. Madzulo a tsiku lomwelo ku Saponara, matope omwe amakokoloka anapha anthu atatu. Pa anthuwo, panali akuluakulu awiri ndi mwana m’modzi.

Patangopita masiku angapo ngoziyi itachitika, a Mboni za Yehova anasonkhana n’kupanga magulu amene anadzipereka n’kuyamba kugwira ntchito yothandiza anthu komanso kuchotsa matope m’madera amene anakhudzidwa kwambiri ndi ngoziyo.

Magulu a anthu a Mboni za Yehovawo anagwira ntchito mothandizana ndi akuluakulu aboma pothandiza anthu amene anakhudzidwa kwambiri ndi ngoziyo. A Mboni amene anagwira nawo ntchitoyi analipo pafupifupi 80 ndipo anagwira ntchitoyi kwa milungu yambiri ngakhale kuti ena ankachokera m’madera a kutali kwambiri pa mtunda wamakilomita oposa 97.

Anthu ambiri a m’dera limene munachitika tsokali anayamikira kwambiri a Mboniwo. Mwachitsanzo, bwanamkubwa wa mzindawo ankanena mobwerezabwereza kuti, “Ndinu anthu achitsanzo chabwino kwambiri.

Patapita miyezi 5, mkulu wina wa mzindawo dzina lake Fabio Vinci, anapereka mendulo yaulemu kumpingo wa Mboni za Yehova wa m’deralo.