Pitani ku nkhani yake

Bukhu la Nkhani za Baibulo Layamba Kugwiritsidwa Ntchito Kusukulu

Bukhu la Nkhani za Baibulo Layamba Kugwiritsidwa Ntchito Kusukulu

Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lomwe linatulutsidwa m’chaka cha 2012 m’chinenero cha Chipangasinani, likugwiritsidwa ntchito kuphunzitsira ana asukulu a ku Philippines omwe amalankhula chinenerochi. Izi zili choncho chifukwa Dipatimenti Yoona za Maphunziro ku Philippines inanena kuti ana aang’ono aziphunzitsidwa m’chinenero cha makolo awo akangoyamba kumene sukulu.

Ku Philippines anthu amalankhula zinenero zoposa 100, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti kwa nthawi yaitali pakhale kusagwirizana pa nkhani ya chinenero chimene chizigwiritsidwa ntchito m’kalasi. M’chaka cha 2012, Dipatimenti Yoona za Maphunziro inanena kuti “ana asukulu akamaphunzitsidwa m’chinenero chamakolo awo, amaphunzira zinthu bwino komanso mwachangu.” Zimenezi zinapangitsa kuti boma likhazikitse lamulo lakuti ana ongoyamba kumene sukulu aziphunzitsidwa m’chinenero chimene chimalankhulidwa m’dera limene akukhala.

Chipangasinani chinali m’gulu la zinenero zimene zinasankhidwa kuti zizigwiritsidwa ntchito kusukulu. Koma panali vuto linalake. Mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ina ananena kuti panali mabuku ochepa achipangasinani oti ana asukulu olankhula chinenerochi azigwiritsa ntchito pophunzira. Choncho buku lakuti, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo la m’chinenerochi linatuluka pa nthawi yoyenera. Bukuli linatuluka pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova mu November 2012.

Mabuku pafupifupi 10,000 anakonzedwa kuti agawidwe pamisonkhano yachigawo imene inachitika m’chakachi. Ana aang’ono pamodzi ndi makolo awo anasangalala kwambiri atalandira buku la m’chinenero chawo. Banja lina linanena kuti: “Ana athu akulikonda kwambiri bukuli chifukwa akulimvetsa bwino.”

Msonkhanowu utangotha, anthu angapo a Mboni anatenga mabuku awo n’kupita nawo kusukulu yomwe ili mumzinda wa Dagupan City. Aphunzitsi a pasukuluyo, omwe ankafunafuna mabuku achipangasinani, anasangalala kwambiri ataona bukuli ndipo mabuku oposa 340 anagawiridwa pasukuluyi. Atangolandira, nthawi yomweyo aphunzitsiwo anayamba kuphunzitsa ana kuwerenga m’chinenero cha makolo awo.

A Mboni za Yehova akusangalala kwambiri chifukwa chakuti bukuli likuthandiza pophunzitsa ana aang’ono. Munthu wina amene anamasulira nawo bukuli ananena kuti: “Kuyambira kalekale, takhala tikudziwa kuti anthu amamvetsa bwino mabuku a m’chinenero chawo. N’chifukwa chake gulu lathu la Mboni limayesetsa kumasulira Mabaibulo ndi mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero zambirimbiri.”