Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anthu Akuthandizidwa Kusintha Moyo Wawo: Mkaidi Anasintha

Anthu Akuthandizidwa Kusintha Moyo Wawo: Mkaidi Anasintha

Ku Spain, a Mboni za Yehova amayendera ndende zokwana 68 ndipo akaidi pafupifupi 600 amaphunzira Baibulo.

Miguel ali m’gulu la anthu a Mboni amene amayendera akaidiwo ndipo iyeyu anakhala m’ndende kwa zaka 12 asanakhale wa Mboni. Panopa, iye amapitanso kundendeko mlungu uliwonse kuti akathandize akaidi ena kusintha moyo wawo ngati mmene iyeyo anathandizidwira.

Kwa zaka zoposa 8 zapitazo, Miguel wakhala akuphunzira Baibulo ndi anthu ambiri amene ali m’ndende. Iya anati: “Ndimasangalala kwambiri ndikamathandiza akaidi amene ali mu ndende imene ndinalimo poyamba komanso ndikamawaona akufunitsitsa kusintha moyo wawo.”

Pamene Miguel anali ndi zaka 4, bambo ake anagundidwa ndi galimoto n’kuferatu. Ngoziyi inachitika chifukwa dalaivala wa galimotoyo anali ataledzera. Kenako amayi ake anayamba ntchito ndipo ankagwira kwa maola ambiri patsiku n’cholinga choti azitha kusamalira ana awo.

Miguel ndi mkulu wake anayamba kujomba kusukulu. Anayambanso kuba katundu ndi ndalama m’magalimoto ndi m’nyumba za eni. Pamene Miguel amafika zaka 12 n’kuti ali chigawenga. Atafika zaka 15, anali atayamba kupeza ndalama zambiri chifukwa ankagulitsa mankhwala ozunguza bongo. Popeza ankakonda kwambiri kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, ankabaso kwambiri kuti azipeza ndalama zogulira mankhwalawo. Pamene amafika zaka 16 n’kuti ali chigawenga choopsa komanso kabwerebwere wa kundende. Pofotokoza mmene moyo wake unalili, Miguel anati: “Sindinkakayikira ngakhale pang’ono kuti ndidzafera kundende kapena ndidzafa ndi mankhwala ozunguza bongo. Ndinkaona kuti ndakodwa mumsampha wa makhalidwe oipawa moti sindikanatha kuchokamo.”

Koma mu 1994, mnzake wina wa Miguel anapempha munthu wina wa Mboni kuti amulembere kalata Miguel, yemwe pa nthawiyo anali m’ndende. M’kalatayo, Miguel anaphunzira zoti Mulungu ali ndi cholinga choti akonzenso dziko lapansili kuti likhale Paradaiso. Wa Mboniyo analimbikitsa Miguel kuti asinthe moyo wake n’cholinga choti adzasangalale ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Ponena za kalatayo, Miguel anati: “Mawu ake anandikhudza mtima kwambiri. Kungoyambira tsiku lomwelo chilichonse chinasintha pa moyo wanga. Ndinaganiza zoti ndiyambe kuphunzira Baibulo ngakhale kuti ndinkadziwa zoti kuchita zimenezo sikukhala kophweka.”

Miguel anadziwa zimenezi chifukwa ankakonda kwambiri kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo komanso kusuta fodya, ndipo sankavutika kupeza zinthu zimenezi. Tsiku lililonse akaidi anzake m’ndendemo ankamupatsa mankhwala ozunguza bongo. Miguel anayamba kupemphera pafupipafupi kuti Mulungu amuthandize kuthana ndi khalidwe lake lokonda kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo. M’kupita kwa nthawi, Miguel anakwanitsa kuthana ndi khalidwe loipali.

Patangopita miyezi itatu, Miguel anayamba kuuza akaidi anzake zimene anayamba kukhulupirira. Chaka chotsatira, iye anatulutsidwa m’ndende ndipo anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Kenako anakumana ndi mtsikana wina wa Mboni n’kugwirizana zoti amange banja. Koma patangotsala mwezi umodzi kuti amangitse ukwati, panabuka vuto lina lalikulu. Khoti lina linalamula Miguel kuti akakhale m’ndende zaka 10 chifukwa cha milandu ina yambirimbiri imene anapalamula m’mbuyomo. Koma atangokhala m’ndende kwa zaka zitatu ndi hafu, iye anatulutsidwa chifukwa cha khalidwe lake labwino. Kenako anamangitsa ukwati wake. Panopa Miguel anasiyiratu khalidwe lauchigawenga.