Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Aphunzitsi ku Philippines Anaona Kuti Webusaiti ya JW.ORG Ndi Yothandiza

Aphunzitsi ku Philippines Anaona Kuti Webusaiti ya JW.ORG Ndi Yothandiza

Mu 2016, a Mboni za Yehova anali ndi mwayi wosonyeza gulu la aphunzitsi a m’chigawo cha Zamboanga del Norte ku Philippines, kuti mavidiyo komanso nkhani za pawebusaiti ya jw.org zingathandize anthu kuphunzira zambiri. Asanakumane ndi aphunzitsiwo, a Mboniwo anakumana kaye ndi a mu Dipatimenti Yoona za Maphunziro a m’chigawochi omwe ali mu mzinda wa Dipolog. Akuluakulu a dipatimentiyo anasangalala kwambiri ndi webusaiti ya jw.org ndipo anaitana a Mboniwo kuti pamisonkhano itatu yotsatira ya aphunzitsi ochokera m’madera a ku Zamboanga del Norte, adzafotokoze zokhudza webusaitiyi kwa 30 minitsi.

Kodi a Mboni anafotokoza bwanji zokhudza webusaitiyi?

A Mboniwo anaonetsa mavidiyo ndi nkhani zapawebusaiti kwa aphunzitsi okwana 300 omwe ankapezeka pamsonkhano uliwonse. Aphunzitsiwo anasangalala kwambiri ndi nkhani yamutu wakuti, “Zimene Mungachite Ngati Muli Ndi Ngongole.” Aphunzitsi ambiri anaona kuti zimene a Mboni anafotokozazo sizithandiza ana a sukulu okha, koma zithandizanso aphunzitsiwo. Aphunzitsi onse analandira kapepala kakuti Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo? komwe kakusonyeza nkhani zambiri zochititsa chidwi komanso zothandiza zomwe zimapezeka pa webusaiti ya jw.org. Ena mwa aphunzitsiwo anapanga dawunilodi mavidiyo pawebusaitiyi.

Zimene a Mboni anafotokoza pamisonkhano itatuyi zinali zabwino kwambiri moti a Dipatimenti Yoona za Maphunziro anakonza zoti a Mboniwo adzafotokozenso zokhudza webusaitiyi kwa anthu pafupifupi 600 omwe amalangiza ana a sukulu ndi aphunzitsi enanso. Zimenezi zitachitika, anthu ambiri anayamikiranso a Mboniwo.

“Webusaitiyi ndi yothandiza kwambiri”

Kenako, ena mwa aphunzitsi ananena mmene webusaiti ya jw.org komanso zimene a Mboniwo anafotokoza zawathandizira. Mphunzitsi wina wamkazi anati: “Ndikufuna kukuyamikirani. Ndaona kuti webusaitiyi ndi yothandiza kwambiri ndikamaphunzitsa ana asukulu.” Mphunzitsi winanso wamkazi anati: “Pali zinthu zambiri zoti ndiphunzire, makamaka pa nkhani yolimbana ndi nkhawa. Webusaitiyi ndi yothandiza kwambiri, osati achinyamata okha, komanso ngakhale akuluakulu.”

Aphunzitsi oposa 350 omwe analipo pamene a Mboni ankafotokoza zokhudza jw.org ankafuna kudziwa zambiri. A Mboniwo anawathandiza powapatsa mabuku oonjezera komanso kusonyeza malangizo othandiza a m’Baibulo kwa onse amene ankafuna malangizowo.

A Mboni za Yehova ndi osangalala kuti aphunzitsi oposa 1,000 analipo pamene iwo ankafotokoza zokhudza webusaiti ya jw.org ku Zamboanga del Norte ndipo anaphunzira mmene webusaiti ya jw.org ingawathandizire pophunzitsa ana asukulu. Webusaitiyi ingathandizenso aphunzitsi padziko lonse chifukwa ili ndi mfundo zambiri zothandiza pa nkhani ya zoyenera ndi zosayenera, makhalidwe, komanso malangizo ochokera kwa Mulungu. *

^ ndime 9 Ku Philippines, sikuti masukulu ali ndi udindo wongophunzitsa ana zinthu zokhudza sukulu basi, koma alinso ndi udindo “wolimbikitsa makhalidwe abwino ndi nkhani zachipembedzo komanso kuthandiza ana kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kuwalangiza.”​—Malamulo Oyendetsera Dziko la Philippines, a 1987 Mutu XIV, Gawo 3.2.