Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anthu Ambiri Aphunzira Kuwerenga ndi Kulemba

Anthu Ambiri Aphunzira Kuwerenga ndi Kulemba

Mu 2011, Mboni za Yehova zinathandiza anthu 5,700 kudziwa kuwerenga ndi kulemba.

Ghana:

Zaka 25 zapitazi, tathandiza anthu oposa 9,000 kuphunzira kuwerenga ndi kulemba.

Zambia:

Kuyambira mu 2002, anthu pafupifupi 12,000 aphunzira kuwerenga ndi kulemba mwaluso. Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka 82, dzina lake Agnes, ananena kuti: “Kumpingo atalengeza kuti kukuyambika kalasi yophunzitsa kuwerenga ndi kulemba, ndinasangalala kwambiri ndipo ndinalembetsa. Tsiku loyamba kuphunzira lenilenilo, ndinaphunzira kulemba dzina langa.

Peru:

Mayi wina wa zaka 55 analemba kuti: “Sindinkaganiza kuti ndingadziwe kuwerenga ndi kulemba chifukwa makolo anga sanandipititse kusukulu.”

Mozambique:

Anthu oposa 19,000 aphunzira kuwerenga m’zaka zoposa 15 zapitazi. Mlongo wina amene anaphunzira kuwerenga, dzina lake Felizarda, ananena kuti: “Ndikusangalala kwambiri chifukwa panopa ndimatha kuwerengera ena Baibulo. Poyamba sindinkatha kuchita zimenezi.

Solomon Islands:

Ofesi ya nthambi inalemba kuti: “M’mbuyomu, anthu ambiri akumidzi analibe mwayi wopita kusukulu. Komanso atsikana ambiri sanapite patali ndi sukulu. Choncho sukulu imeneyi yathandiza kwambiri anthu kuphunzira kuwerenga ndi kulemba, makamaka azimayi. Anthu ambiri akadziwa kuwerenga ndi kulemba amachita zinthu molimba mtima.