Pitani ku nkhani yake

Kulalikira kwa Anthu a Mtundu wa Sinti ndi Roma ku Germany

Kulalikira kwa Anthu a Mtundu wa Sinti ndi Roma ku Germany

M’dziko la Germany, muli anthu ambiri a mtundu wa Sinti ndi Roma. * Posachedwapa a Mboni za Yehova anatulutsa timabuku, timapepala ndi mavidiyo m’chinenero cha Romany chimene anthuwa amayankhula. *

Kuyambira mu September mpaka mu October 2016, a Mboni za Yehova anagwira ntchito yapadera yolalikira pogwiritsa ntchito mabuku ndi zinthu zina za chinenero cha Romany kwa a Sinti ndi a Roma omwe amakhala m’mizinda yosiyanasiyana m’dziko la German. Ina mwa mizindayi ndi monga Berlin, Bremerhaven, Freiburg, Hamburg ndi Heidelberg. Anakonzanso zokamba nkhani za onse m’chinenerochi M’nyumba za Ufumu za Mboni m’maderawa.

Anthu Ambiri Anasangalala

Anthu ambiri a mtundu wa Sinti ndi Roma anadabwa komanso kusangalala kwambiri ndi zimene a Mboni anachita. A Andre ndi akazi awo a Esther omwe anagwira nawo ntchito yolalikirayi ananena kuti: “Anthu anasangalala kwambiri chifukwa tinachita khama kuti tikambirane nawo m’chinenero chawo.” Ndipo anthu ambiri anakhudzidwa kwambiri atamva ndi kuwerenga uthenga wa m’Baibulo m’chinenero chawo. Mayi wina ataonera vidiyo ya mutu wakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? m’chinenero cha chi Romany anadabwa kwambiri ndipo ananena mokweza maulendo angapo kuti, “N’chinenero changa ka ichi!”

Wa Mboni wina dzina lake Matthias, yemwenso anagwira nawo ntchitoyi ku Hamburg anati: “Ine ndi mkazi wanga tinali pagulu la anthu 8 ndipo tinakalalikira m’dera lomwe kumakhala a Sinti ndi a Roma pafupifupi 400. Aliyense amene tinakambirana naye ankapempha buku linalake.” Mayi wina dzina lake Bettina yemwenso anadzipereka kugwira nawo ntchitoyi ku Hamburg anati: “Anthu ena anafika polira chifukwa choona kuti a Mboni apanga mabuku m’chinenero cha chi Romany.” Anthu ambiri ankati akalandira buku, pompo amayamba kuliwerenga mokweza ndipo enanso ankatenga mabuku angapo kuti akapatse anzawo.

Anthu enanso a mtundu wa Sinti ndi Roma ataitanidwa ku misonkhano ya mpingo anapita. Ndipo ku Hamburg anthu amene anasonkhana analipo 94 koma ambiri kanali koyamba kusonkhana M’nyumba ya Ufumu. Ku Reilingen komwe ndi kufupi ndi mzinda wa Heidelberg anthu amene anasonkhana anali 123. Pambuyo pa misonkhano anthu 5 oyankhula chi Romany anapempha kuti akufuna kuphunzira Baibulo.

Pa nthawi ya ntchito yapaderayi, a Mboni za Yehova anagawira timapepala ndi timabuku pafupifupi 3,000. Komanso a Mboniwa anakambirana ndi anthu a mtundu wa Sinti ndi Roma opitirira 360 ndiponso anayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu 19. Anthu ambiri omwe anamva uthengawu ankangoti, “Zili bwino kwambiri kuti nafenso Mulungu watiganizira.”

^ ndime 2 Anthu a mtundu wa Sinti anachokera ku mtundu wa Roma ndipo amakhala chigawo chakumadzulo ndi chapakati cha dziko la Europe. M’nkhaniyi, mtundu wa “Roma” ukuimira gulu la anthu omwe anachokera ku chigawo chakum’mawa ndiponso kum’mwera chakum’mawa kwa Europe.

^ ndime 2 Buku lina la pa intaneti linanena kuti zinenero za ku Roma zili ndi “zinenero zinanso zing’onozing’ono zopitirira 60 zomwe ndi zosiyanasiyana” (Encyclopædia Britannica Online). Pofuna kuti timvetse bwino nkhaniyi, tikamalemba kuti chinenero cha “Romany” tikutanthauza chimene amayankhula a Sinti ndi a Roma omwe amakhala ku Germany.