Mu November m’chaka cha 2011, anthu ena a Mboni za Yehova anayamba kugwira ntchito yatsopano yomwe cholinga chake n’kuthandiza anthu a m’tauni ya Manhattan kuti adziwe uthenga wa m’Baibulo. Pa ntchitoyi, a Mboni akumaika mabuku awo pamatebulo okongola kwambiri omwe akumawaika m’malo osiyanasiyana komanso mabuku ena akumawaika m’ngolo zokokedwa ndi galimoto. A Mboni ayamba kugwira ntchito yapaderayi m’dera lakum’mwera m’tauni ya Manhattan, yomwe ndi yakale kwambiri. M’tauniyi mumachitika zinthu zambiri poyerekezera ndi zimene zimachitika m’matauni onse a mumzinda wa New York City.

Anthuwa akugwira ntchitoyi m’zigawo zinayi za tauniyi. M’chigawo chilichonse muli malo angapo amene akumaikapo tebulo la mabuku kapena ngolo yokhala ndi mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo n’cholinga choti anthu odutsa azitha kuima. Pamalo alionse pakumakhala munthu wa Mboni za Yehova wa m’deralo yemwe amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Matebulo ndi ngolo zambiri akumaziika pamalo monga okwerera basi kapena sitima, ndipo pamalo amenewa pamadutsa anthu masauzande ambirimbiri tsiku lililonse.

Pamalo amenewa, anthu akumatha kudziwa mayankho a mafunso ambiri a m’Baibulo. Ndipo anthu omwe alibe nthawi yokwanira akumangotenga buku kapena magazini kuti akawerenge nthawi ina.

Pamalo oterewa pakumakhala mabuku a zinenero zosiyanasiyana. Ngati munthu akufuna buku la chinenero chomwe pamalopo palibe, akhoza kuliitanitsa n’kudzatenga pakapita masiku angapo.

Akuluakulu a boma komanso anthu ena akusangalala kwambiri ndi ntchito imeneyi. Mwachitsanzo, wapolisi wina anati: “Mumachedwa kuti? Ntchito yanuyi ikuthandiza kwambiri anthu.

Munthu winanso anaima mwadzidzidzi atangoona buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Iye ananena kuti anaona anthu angapo akuwerenga bukuli m’njira. Choncho iye ankangodzifunsa kuti, ‘Kodi anthuwa alitenga kuti bukuli?’ Koma munthuyo anadziwa yankho la funsolo atafika pamalo pomwe panaikidwa mabukuwo.

Tsiku lililonse popita kuntchito, mnyamata wina ankadutsa pamalo ena pamene pankaikidwa tebulo yokhala ndi mabuku. Mnyamatayo anachita zimenezi kwa milungu 6, koma tsiku lina anaima n’kunena kuti, “Kodi mungandigawireko buku?” Anthu a Mboni za Yehova amene ankagawa mabukuwo anamuthandizadi. Iwo anam’patsa Baibulo n’kumusonyeza mmene angaligwiritsire ntchito.

Anthu achidwi akhala akuima kuti akambirane nkhani zokhudza Mulungu. Mwezi umodzi wokha posachedwapa, ntchito imeneyi yathandiza kuti anthu alandire magazini okwana 3,797 ndiponso mabuku okwana 7,986.