Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kuonetsa Miyala Yamtengo Wapatali ku Botswana

Kuonetsa Miyala Yamtengo Wapatali ku Botswana

Kuyambira pa 22 August  mpaka 28 August, 2016, a Mboni za Yehova ku Botswana, komwe ndi kuchimake kwa miyala ya dayamondi, anaonetsa miyala yosiyanasiyana yamtengo wapatali kwa anthu amene anabwera kuchionetsero cha zamalonda m’dzikolo. Amboniwo anaonetsa zinthu monga webisayiti ya jw.org, mabuku osiyanasiyana ofotokoza Baibulo komanso mavidiyo omwe amathandiza kuti mabanja akhale olimba. Makolo komanso ana amene anabwera pamalowa anasangalala kwambiri ndi mavidiyo a Khalani Bwenzi la Mulungu, omwe amathandiza anthu kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Popeza kuti pali mavidiyo ochepa m’chinenero cha Chisetwana chimene anthu ambiri amalankhula m’dzikolo, anthu ambiri anafuna kudziwa mmene angapezere mavidiyo amenewa.

Alendo omwe anabwera pamalowa kuchokera m’madera osiyanasiyana a dzikolo analandira pafupifupi mabuku ndi zinthu zina pafupifupi 10,000, ndipo anthu 120 anapempha kuti munthu Wamboni aziphunzira nawo Baibulo kwaulere. Anthu ambiri anadabwa kuona kuti a Mboni za Yehova a mipingo yolankhula Chingerezi komanso Chisetwana akugwira ntchito mogwirizana pa chionetserocho.

Akuluakulu oyendetsa chiwonetserochi atafufuza zinthu zosiyanasiyana zimene anthu ankaonetsa anapereka mphoto yoyamba kwa a Mboni za Yehova.