Chaposachedwa, anthu 23 a Mboni za Yehova a m’tauni ya Queens ku New York, anayamba kuphunzira Chibengali m’kalasi yophunzitsa chinenero. Kalasiyi inakonzedwa ndi a Mboni za Yehova ndipo imathandiza anthu ena a Mboni kuphunzira chinenero chatsopano kwa masiku ochepa. Chinenero cha Chibengali chimalankhulidwa ku Bangladesh ndi mbali zina za dziko la India.

Kalasi yophunzitsa Chibengali ndi imodzi mwa makalasi ambiri ophunzitsa zinenero amene ali ku United States komanso m’mayiko ena. Cholinga cha makalasi amenewa n’kuthandiza anthu ena a Mboni kuti aphunzire zinenero zina kuti azitha kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu amene amalankhula zinenerozo.

Mlongo wina dzina lake Magaly, yemwe ankaphunzira nawo m’kalasi ya Chibengali, ananena kuti: “Anthu olankhula Chibengali m’dera lathu akuchuluka kwambiri. Anthu akufuna mayankho a mafunso ofunika kwambiri, monga funso lakuti, N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri? Ndikamauza anthu za madalitso osangalatsa amene Mulungu walonjeza m’tsogolomu, m’pamenenso anthuwo amafuna kudziwa zambiri. Koma nthawi zina ndimalephera kuwauza chifukwa vuto limakhala chinenero.”

Pofuna kuthandiza anthu kuti aphunzire mwachangu chinenero chatsopano, aphunzitsi amaphunzitsa m’njira yoti ophunzirawo azisangalala. Nthawi zina aphunzitsiwo amagwiritsa ntchito zitsanzo za zinthu zooneka pofuna kuthandiza ophunzirawo kuti azikumbukira zimene aphunzirazo.

Tsiku lililonse akamaliza kuphunzira chinenero, anthuwo amagwiritsa ntchito zimene aphunzirazo popita kukalalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu olankhula Chibengali m’deralo. Magaly anati: “Anthu amasangalala kwambiri ndipo amafuna kudziwa chimene chandichititsa kuti ndiziphunzira chinenero chawo. Ndipotu anthu akaganizira zoti timapatula nthawi yophunzira chinenero chawo, ankaona kuti uthenga wathuwo ndi wofunika kwambiri.”

A Mboni za Yehova sikuti amangophunzira zinenero zachilendo basi koma amaphunzitsidwanso kuti akhale aphunzitsi a zinenero zinanso. Mwachitsanzo, m’gawo limene limayang’aniridwa ndi ofesi ya Mboni za Yehova ya ku United States lokha, munachitika makalasi 38 ophunzitsa anthu kuti akhale aphunzitsi a zinenero zina. Makalasi amenewa anachitika kuyambira mu January 2006 mpaka mu January 2012 ndipo anthu 2,244 anaphunzitsidwa m’makalasi amenewa. Pomafika mu September 1, 2012, a Mboni za Yehova a m’gawo la ofesi yawo ya ku United States anali atachititsa makalasi oposa 1,500 ophunzitsa zinenero 37.