Pitani ku nkhani yake

Chiwerengero cha Mboni za Yehova Chakwera Kwambiri

Chiwerengero cha Mboni za Yehova Chakwera Kwambiri

Mu 1987, a Lyman Swingle, omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anakamba nkhani ku Plaza Monumental, lomwe ndi bwalo la masewera omenyana ndi ng’ombe. Bwaloli lili ku Valencia, m’dziko la Venezuela. Anthu amene anamvetsera nkhani yomwe anakamba a Swingle analipo 63,580 ndipo ambiri anayenda pabasi usiku wonse kuti akamvetsere nkhaniyi. M’bale Swingle anauza gulu la anthu amene anasonkhanawo kuti: “Panopa nthambi yanuyi si yaing’ononso. Ikukula ndithu ndipo mmene zikuonekera, posachedwapa ikhala m’gulu la nthambi zomwe zili ndi ‘ofalitsa 100,000.’”

Pa nthawiyi, ku Venezuela kunali a Mboni za Yehova oposa 38,000, omwe ankalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu. Ndipo mayiko 8 okha ndi omwe anali ndi anthu olalikira za Ufumu oposa 100,000.

Chiwerengero cha Mboni za Yehova padziko lonse chakwera mofulumira kwambiri. Mwachitsanzo, pambuyo pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, panali anthu ochepa omwe ankalalikira za Ufumu wa Yehova. Koma malinga ndi lipoti limene linatulutsidwa mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1943, zinthu zinasintha. Lipotili linati: “Ngakhale kuti sitinalandire lipoti lonse lachaka cha 1942 chifukwa cha nkhondo, lipotili ndi labwino. . . , chifukwa likusonyeza kuti padziko lonse, pawonjezereka anthu oposa 106,000 omwe akulalikira mwakhama uthenga wabwino.” Pa nthawi yomwe nkhondo yachiwiri inkamenyedwa, anthu ambiri ankamvetserabe uthenga wa m’Baibulo. Mwachitsanzo, mu 1950 chiwerengero cha anthu olalikira uthenga wa Ufumu ku United States kokha chinadutsa 100, 000.

Dziko la Nigeria linali lachiwiri kukhala ndi anthu 100,000 olalikira uthenga wa Ufumu ndipo zimenezi zinachitika mu 1974.

Mu 1975, mayiko a Brazil ndi Germany nawonso anakhala ndi anthu olalikira uthenga wa Ufumu oposa 100,000. Kuchuluka kwa a Mboni m’mayikowa ndi umboni wakuti anthu ambiri amakonda choonadi cha m’Baibulo.

Chiwerengero cha anthu okonda uthenga wabwino padziko lonse chikupitirizabe kukwera. Zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo wakuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.”​—Yesaya 60:22.

Lipoti la chaka chautumiki cha 2014 linasonyeza kuti pali mayiko 24 omwe ali ndi a Mboni oposa 100,000. Limodzi mwa mayikowa ndi la Venezuela, ndipo chiwerengero cha a Mboni m’dzikoli chinafika 100,000 mu 2007. Padziko lonse lapansi pali a Mboni 8,201,545 komanso mipingo 115,416.

Mayiko amene kuli a Mboni oposa 100,000

Chigawo

Dziko

Ofalitsa

Africa

Angola

108,607

Congo, Democratic Republic of

216,024

Ghana

125,443

Nigeria

362,462

Zambia

178,481

Asia

Japan

215,703

Korea, Republic of

100,641

Philippines

196,249

Europe

Britain

138,515

France

127,961

Germany

166,262

Italy

251,650

Poland

123,177

Russia

171,268

Spain

112,493

Ukraine

150,906

North America

Canada

116,312

Mexico

829,523

United States of America

1,243,387

South America

Argentina

150,171

Brazil

794,766

Colombia

166,049

Peru

123,251

Venezuela

140,226