Pali anthu pafupifupi 500,000 omwe amagwira ntchito m’masitima kuzungulira padziko lonse. Ndiyeno popeza kuti anthu ogwira ntchito m’masitimawa amayenda pamadzi ndipo amangoima m’madoko, kodi a Mboni za Yehova angatani kuti aziwalalikira? Sitima ikangofika padoko, a Mboni omwe anaphunzitsidwa bwino amalowa musitimamo kukaphunzira Baibulo ndi anthuwo kapenanso kuwagawira mabuku m’chiyankhulo chimene akufuna.

Kodi a Mboniwa amalandiridwa bwanji m’masitimawa? Bambo wina wa Mboni dzina lake Stefano yemwe amalalikira padoko la Vancouver, ku Canada, anati: “Anthu ena amaganiza kuti anthu onse ogwira ntchito m’masitima ndi opanda ulemu komanso ovuta. N’zoona kuti ochepa chabe ali ndi makhalidwe amenewa koma ambiri amene timakumana nawo ndi odzichepetsa komanso ofunitsitsa kuphunzira. Anthuwa amatilandira bwino chifukwa ambiri amakhulupirira Mulungu ndipo amafuna kuti aziwadalitsa.” Ku Vancouver kokha, a Mboni za Yehova analoledwa kulalikira m’masitima maulendo opitirira 1,600, kuyambira mu September 2015 mpaka mu August 2016. Ogwira ntchito m’masitima analandira mabuku a zinenero zambiri ndipo anthu opitirira 1,100 anayamba kuphunzira Baibulo.

Kodi zimatheka bwanji kuti ogwira ntchito musitima apitirize kuphunzira Baibulo?

A Mboni za Yehova amatha kupezeka m’madoko ambiri padziko lonse, choncho ogwira ntchito m’masitima omwe akufuna kupitiriza kuphunzira angapemphe kuti wa Mboni wina azikaphunzira nawo Baibulo akafika padoko lotsatira. Mwachitsanzo, mu May 2016, a Mboni za Yehova ku Vancouver anakumana ndi Warlito yemwe amagwira ntchito yophika mu sitima ina yonyamula katundu. A Mboniwo anamuonetsa vidiyo ya mutu wakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Warlito anasangalala kwambiri ndipo ankafuna kupitiriza kuphunzira Baibulo, koma vuto linali loti doko lotsatira linali kutali ku Paranaguá m’dziko la Brazil.

Patadutsa mwezi umodzi, sitima yawo inakafika ku Paranaguá. Ndipo Warlito anadabwa kwambiri kuona a Mboni awiri atalowa m’sitimayo n’kumafunsa za iyeyo. Iwo anamuuza kuti a Mboni anzawo a ku Vancouver ndi omwe anawatumizira uthenga woti iyeyo akufuna kuphunzira. Warlito anasangalala kwambiri atakumana ndi a Mboniwo ndipo anayamikira a Mboni a ku Vancouver chifukwa chokonza zoti a Mboni a ku Paranaguá akumane naye. Iye anavomera kupitiriza kuphunzira Baibulo ndi a Mboni enanso padoko lotsatira.