Kumayambiriro kwa mwezi wa July 2013, gulu la a Mboni za Yehova okwana 28 ku Brazil, linachoka m’tauni ya São Félix do Xingu n’kuyamba ulendo wopita kudera la amwenye otchedwa Cayapo ndi enanso otchedwa Yuruna. Iwo anakwera boti lotalika mamita 15 ndipo anadutsa mumtsinje wa Xingu kulowera kumene unayambira. Mtsinjewo ndi wautali makilomita 2,092 kukafika kumpoto kumene kuli mtsinje wa Amazon.

Gulu la a Mboniwa linali paulendo wokalalikira za Ufumu wa Mulungu kwa anthu a m’midzi ya m’mbali mwa mtsinje. Atayenda kwa masiku atatu, a Mboniwa anafika pamudzi wina wotchedwa Kokraimoro. Pamudziwo, analandiridwa ndi anthu ansangala komanso ochereza. Mayi wina wa m’mudzimu ankangowakodola. Munthu wina wa m’dera la komweko yemwe ankawatsogolera pa ulendowu anafotokoza kuti mayi yemwe ankawakodolayo amawauza kuti: “Nonsenu bwerani kuno tikudziweni.”

A Mboniwa anayesetsa kulankhula ndi aliyense. Ena ankalankhula nawo m’Chipwitikizi ndipo ena ankalankhula nawo pongogwiritsa ntchito zizindikiro kapena manja. Zithunzi zokongola za m’mabuku amene a Mboniwa anabweretsa zinathandiza chifukwa anthu ambiri analandira mabuku, makamaka kabuku kakuti Mverani Mulungu.

Bambo wina wa Mboni dzina lake Gerson, yemwe amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse, amakhala m’tauni ya São Félix do Xingu. Bamboyu akukumbukira zimene munthu wa m’mudzi winawake anachita atalandira Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Bamboyu anati: “Analiyang’anitsitsa kenako analigwira mwamphamvu ndi manja awiri ndipo sankafuna kulisiya ngakhale pang’ono.”

Gulu la a Mboni za Yehovawo anagawa mabuku 500, komanso magazini ndi timabuku, kwa anthu amene ankawafuna okhala m’mbali mwa mtsinje. Anthu a m’mudzi wina wotchedwa Kawatire, anamvetsera mwachidwi malonjezo a m’Baibulo okhudza dziko latsopano la paradaiso. Munthu wina wachimwenye amenenso amakonda kuchereza alendo, dzina lake Tonjaikwa, ankauza anthu ena kuti: “Anthu m’paradaiso azidzachita zinthu ngati ife.”

Anthu ambiri a m’tauni ya São Félix do Xingu anadziwa zoti m’derali mwabwera anthu a Mboni. Mayi Simone, omwe anali nawo pa ulendowu, anafotokoza kuti anthu ena a m’tauni yakwawo ankakayikira ngati gulu la a Mboniwa akalandiridwe m’midzi yomwe anakalalikiramoyo. Komabe panalibe vuto lililonse limene a Mboniwa anakumana nalo. Mayi Simone anati: “Tinkalandiridwa bwino ndipo anthu onse tinawalalikira.”