Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kulalikira Mumzinda wa Paris

Kulalikira Mumzinda wa Paris

Pa 30 November mpaka pa 12 December 2015, anthu ochokera m’mayiko 195, anakumana mumzinda wa Paris m’dziko la France kudzachita msonkhano wa bungwe la United Nations. Msonkhanowu unali wokambirana za kusintha kwa nyengo komanso mmene angapewere kuwononga chilengedwe. Anthu pafupifupi 38,000 anapezeka pamsonkhanowo ndipo ena mwa iwo anali akuluakulu aboma, asayansi, akatswiri a zachilengedwe ndi akuluakulu a bizinezi. Anthu masauzande ambiri anasonkhana pamalo ena apafupi kuti akamve zambiri zokhudza nkhani ya kusintha kwa nyengo.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova sanakapezeke nawo pamsonkhanowo, nawonso amachita chidwi kwambiri ndi zachilengedwe. Pa nthawi imeneyo, a Mboni za Yehova ambiri mumzinda wa Paris anali pa ntchito yapadera yolalikira uthenga woti posachedwapa anthu sadzawononganso chilengedwe padzikoli.

Wa Mboni wina ali m’basi, analankhula ndi munthu wina wa ku Peru yemwe anavala zovala zachikhalidwe cha kwawo. Munthuyo anafotokoza kuti ngakhale ali ndi thanzi labwino komanso kuti amakhala kudera lokongola lamapiri, amakhala ndi nkhawa akaganizira za tsogolo la dziko lapansili. Uthenga umene wa Mboni uja anamuuza unamusangalatsa kwambiri moti anatenga khadi lodziwitsa anthu za webusaiti ya www.jw.org.

A Mboni ena awiri ali mu sitima, analalikira katswiri wina wa zachilengedwe wa ku America. Katswiriyu anadabwa atamva kuti kawiri konse a Mboni za Yehova analandira mphoto kuchokera ku bungwe loona zoteteza chilengedwe. Bungweli linapereka mphotozi a Mboni za Yehova atamanga nyumba ziwiri zatsopano zomwe zinamangidwa pogwiritsa ntchito njira zatsopano zoteteza chilengedwe. Nyumbazi zinamangidwa ku Wallkill m’dziko la United States. Katswiriyu anasangalala kwambiri moti nayenso analandira khadi la webusaiti ya jw.org.

Anthu ambiri ataona kuti a Mboni za Yehova amachita chidwi kwambiri ndi zachilengedwe, analonjeza kuti akatsegula webusaiti yathu. Mayi wina amene anachokera ku Canada, atamva kuti a Mboni anayesetsa kuteteza malo omwe kumakhala mtundu winawake wa mbalame, pamene ankamanga likulu lawo latsopano ku Warwick, ananena kuti: “Ndisanayambe ntchito yoteteza chilengedwe, ndinkagwira ntchito yoteteza mbalame. Sindinkadziwa kuti a Mboni za Yehova mumaona kuti zamoyo ndi zofunika kwambiri. Ndikabwerera, ndikawerenga mabuku anu ndipo ndikatsegula webusaiti yanu kuti ndidziwe zambiri za a Mboninu.”