Pitani ku nkhani yake

Amadutsa Pamchenga wa Pansi pa Nyanja Kupita Kokalalikira

Amadutsa Pamchenga wa Pansi pa Nyanja Kupita Kokalalikira

M’nyanja ya North Sea muli tizilumba totchedwa Halligen tomwe tili patalipatali. Tizilumbati tili pafupi ndi dziko la Germany ndipo pamakhala anthu pafupifupi 300. Ndiye kodi a Mboni za Yehova amatani kuti akalalikire kutizilumba timeneti?​—Mateyu 24:14.

Amboni ena amakwera boti kuti akafike kutizilumba tina. Koma kagulu kena ka a Mboni kamayenda pamchenga wa pansi pa nyanja kuti akalalikire kutizilumba tinato. Iwo amayenda wapansi pa mtunda wa makilomita 5. Kodi zimatheka bwanji kuchita zimenezi?

Amachitika Mwayi Madzi Akaphwera

Madzi akudera la tizilumbati amakhala akuya pafupifupi mamita atatu. Koma tsiku lililonse pa nthawi inayake, madziwo amaphwera moti a Mboniwo amatha kuyenda wapansi kuti akafike kutizilumba titatu ta m’derali.

Kodi amayenda bwanji? Munthu amene amawatsogolera dzina lake Ulrich anati: “Timayenda pafupifupi maola awiri kuti tikafike ku Halligen. Nthawi zambiri timayenda osavala nsapato chifukwa ndi njira yabwino yoyendera pamalowa. Koma m’nyengo yozizira timavala nsapato.”

Tikulalikira pakachilumba kena ka Halligen

Malowa amaoneka achilendo kwambiri. Ulrich anati: “Zimangokhala ngati muli kupulaneti ina. Malo ena amakhala ndi matope, ena miyala ndipo ena amakhala ndi udzu. Mumaonanso mbalame zosiyanasiyana, nkhanu ndi zinyama zina.” Nthawi zina timayenera kuoloka timitsinje timene timatsala madzi akaphwera.

Anthu amene amadutsa m’malowa amakumana ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, Ulrich anati: “Munthu akhoza kusochera mosavuta kukakhala nkhungu. N’chifukwa chake timagwiritsa ntchito zipangizo zina zotithandiza kudziwa njira. Timayesetsanso kubwerera pa nthawi yake komanso kuyenda mwachangu kuti tidutse madzi asanayambe kudzaza.”

Kodi khama la anthuwa limangopita pachabe? Ulrich anafotokoza za bambo wina wazaka zoposa 90 amene amakonda kuwerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anati: “Tsiku lina nthawi inatithera ndipo tinaona kuti n’zosatheka kupita kwa bambowo. Koma tisananyamuke iwo anatilondola pa njinga n’kutifunsa kuti: ‘Kodi lero simundipatsa Nsanja ya Olonda yanga?’ Izi zinatisangalatsa kwambiri ndipo tinawapatsa magaziniyo.”