Kuyambira pa August 22 mpaka 28, 2016, ku Botswana kunali chionetsero cha zinthu zosiyanasiyana. Dzikoli lili ndi migodi yambiri ya miyala yamtengo wapatali ya dayamondi. Pa chionetserochi, a Mboni za Yehova nawonso anapeza malo omwe anaonetserapo chuma china chamtengo wapatali. Pamalo awopo panaonetsedwa mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo, webusaiti ya jw.org, ndi mavidiyo omwe amathandiza anthu kuti mabanja awo akhale olimba.

Makolo ndi ana omwe anafika pamalowa anachita chidwi kwambiri ndi mavidiyo a makatuni a mutu wakuti Khalani Bwenzi la Yehova omwe amathandiza anthu kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Koma popeza kuti mavidiyowa analipo ochepa mu Chitswana chomwe ndi chinenero chachikulu m’dzikolo, anthu ambiri ankafunsa kuti angawapeze bwanji.

Alendo ochokera m’madera osiyanasiyana m’dzikoli anatenga mabuku pafupifupi 10,000 ndipo anthu 120 anapempha kuti akufuna kuphunzira Baibulo kwaulere. Ndipo ambiri anachita chidwi kuona kuti a Mboni za Yehova a m’mipingo ya Chitswana ndi Chingelezi amagwirira ntchito limodzi pachionetserochi.

Woyang’anira chionetsero atayendera malo onse omwe anthu ankaonetserapo zinthu zawo, anapereka mphoto yoyamba kwa Mboni za Yehova.