Pitani ku nkhani yake

A Mboni za Yehova Akulalikira M’madera Akutali Kwambiri

A Mboni za Yehova Akulalikira M’madera Akutali Kwambiri

M’chaka cha 2014, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linapereka malangizo onena zoti a Mboni azipita kumadera akutali kwambiri a kumpoto kwa dziko lapansi kuti azikalalikira uthenga wabwino. (Machitidwe 1:8) Ntchitoyi inkafunika kugwiridwa kumadera a ku Alaska (U.S.A.), ku Lapland (Finland), ku Nunavut komanso m’madera a kumpoto kwa dziko la Canada.

A Mboni za Yehova akhala akulalikira kumadera amenewa kwa nthawi yaitali. Komabe a Mboni amene ankapita kukalalikira kumadera amenewa sankakhalitsako ndipo nthawi zambiri ankangogawira mabuku ofotokoza Baibulo basi.

Kenako panakhazikitsidwa dongosolo latsopano ndipo maofesi anthambi omwe amayang’anira madera amenewo anapempha apainiya okhazikika (amenewa ndi anthu omwe amalalikira maola oposa 70 pamwezi) kuti azipita kukalalikira kumaderawa kwa miyezi itatu kapena kuposa. Anakonza zoti ngati anthu ambiri a m’dera limene akulalikira atasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, apainiyawo azikhala komweko kwa kanthawi ndithu n’kumachititsa misonkhano.

N’zoona kuti kulalikira kumaderawa n’kovuta kwambiri. Mwachitsanzo, apainiya ena awiri anauzidwa kuti azikalalikira m’dera la Barrow ku Alaska. Pa apainiyawa wina anachokera ku California ndipo wina anachokera ku Georgia m’dziko la United States. Itafika nyengo yozizira, abalewa ankafunika kupirira chifukwa kunja kunkazizira kuposa m’firiji. Ngakhale ankakumana ndi mavuto amenewa, patangodutsa miyezi yochepa, apainiyawa analalikira pafupifupi nyumba zonse zomwe zili m’dera Barrow. Apainiyawo ankaphunzira ndi anthu 4 ndipo mmodzi wa anthuwo dzina lake linali John. John pamodzi ndi chibwenzi chake amaphunzira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndiponso amauza anzake komanso anthu akuntchito kwake zimene waphunzira. Tsiku lililonse amawerenga kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku pafoni yake yomwe ili ndi pulogalamu ya JW Library.

M’dera la Rankin Inlet, kulibe misewu ndipo zimakhala zovuta kuyenda kuti ukalalikire. Apainiya awiri omwe ndi banja, anapita kuderali pandege ndipo anayamba kuphunzira ndi anthu angapo. Ataonetsa bambo wina vidiyo yakuti, Kodi Panyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? bamboyo anawafunsa kuti adzamanga liti Nyumba ya Ufumu m’deralo. Anawauzanso kuti: “Ngati ndingadzakhale ndili moyo mukadzamanga Nyumba ya Ufumu yanuyo, ndizidzabwera kumisonkhano yanu.”

Apainiya ena anatumizidwa kudera la Savukoski ndipo lili ku Finland. Kuderali kuli mphalapala zochuluka kwambiri kuposa anthu. Mpainiya wina amene anapita kuderali anati: “Kunja kunkazizira osati pang’ono komanso kumagwa sinowo wambiri.” Komabe apainiyawo ananena kuti nthawi imene anapitayo inali yabwino kwambiri. Iwo anati: “Tinalalikira pafupifupi paliponse m’derali. Sitinkavutika kuyenda chifukwa anthu a m’derali ankachotsa sinowo m’misewu. Komanso chifukwa cha kuzizira anthu ambiri ankapezeka pakhomo.”

Dongosolo limeneli lathandiza kwambiri anthu akumadera akutali amenewa kuti adziwe Yehova. Mwachitsanzo, apainiya awiri analalikira mayi wina yemwe ndi meya wa mzinda wina wa ku Alaska. Mayiyu anasangalala kwambiri ndi zimene anamva ndipo analemba uthenga pa Intaneti wonena za zimene anakambirana ndi apainiyawo. Komanso anaika pa Intanetipo chithunzi cha kapepala ka Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Apainiya ena omwe anatumizidwa m’dera la Haines ku Alaska, analalikira anthu ambiri omwe ankafuna kudziwa zambiri moti anthuwo anayamba kufika pamisonkhano yomwe inkachitikira palaibulale ina. Nyuzipepala ina inadziwitsa anthu a m’derali kuti, m’tauni ya Haines mwabwera anthu awiri, wina wachokera ku Texas ndipo wina wachokera ku North Carolina. Inawauza kuti anthuwo akuphunzitsa anthu Baibulo. Chidziwitsochi chinamaliza ndi mawu awa: “Kuti mudziwe zambiri, pitani pa jw.org.”