Pitani ku nkhani yake

Zithunzi Zothandiza Kuti Nkhani Zikhale Zosangalatsa

Zithunzi Zothandiza Kuti Nkhani Zikhale Zosangalatsa

Kodi anthu ojambula zithunzi za m’mabuku athu, amatani kuti zithunzizo zikhale zothandiza komanso zosangalatsa? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione zimene anachita pokonza chithunzi chapachikuto cha Galamukani! ya September 2015. *

  • Pokonzekera. Poyamba anthu a m’Dipatimenti ya Zithunzi ku Patterson, m’dziko la United States anawerenga nkhani yakuti, “Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?” Ndiyeno anayamba kujambula pamanja zithunzi zomwe ankaona kuti zingakhale zogwirizana ndi nkhaniyi. Kenako anaonetsa zithunzizo kwa anthu a m’Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku kuti asankhe chimene chiyenera kujambulidwa.

  • Malo ojambulira zithunzi. Anthu ojambulawa anasankha kujambula chithunzichi pamalo olandirira alendo ku Patterson. Iwo anangosintha malowa kuti aoneke ngati banki, m’malo mojambula chithunzichi pabanki yeniyeni. *

  • Anthu amene anajambulidwa. Anthu onsewa ndi a Mboni za Yehova ndipo anasankhidwa kuti adzaoneke ngati anthu osiyanasiyana amene angapezeke pabanki imene ili mumzinda waukulu. Mayina a anthu amene amajambulidwa amasungidwa kuti asamangogwiritsa ntchito anthu omwewo nthawi zonse.

  • Zinthu zofunika m’zithunzi. Anthu a Dipatimenti ya Zithunzi anagwiritsa ntchito ndalama za dziko lina kuti zioneke ngati bankiyo si ya ku United States. Ojambulawa anagwiritsa ntchito zinthu zomwe zinathandiza kuti malowo aoneke ngati banki yeniyeni. Munthu wina wojambula dzina lake Craig anati: “Timayesetsa kuganizira mbali iliyonse tikamajambula chithunzi.”

  • Zovala komanso zophodaphoda. Pojambula chithunzi chapabanki, anthu ojambulidwawa anavala zovala zawo. Komabe a Dipatimenti ya Zithunzi akamajambula zithunzi zosonyeza zochitika zakale komanso zina zapadera, amafufuza kapena kupanga okha zoyenera kuvala. Anthu odziwa za zophodaphoda amathandiza anthu amene akukajambulidwa kuti aonek

    e mogwirizana ndi nthawi, malo komanso zochitika zomwe zikufunika pachithunzicho. Craig ananenanso kuti: “Popeza kuti zojambulira zamakono ndi zamphamvu, chilichonse chimene timajambula chimaonekera kwambiri. Ndiye timafunika kusamala kuti tisalakwitse chilichonse pazithunzi zathu.”

  • Pojambula chithunzi. Ojambula chithunzicho anaonetsetsa kuti m’bankimo mukhale mowala n’cholinga choti musaoneke ngati madzulo. Nthawi zonse ojambula zithunzi amaonetsetsa kuti malo amene akujambulawo akhale owala mogwirizana ndi zimene akufuna kujambula. Mwachitsanzo, nthawi zina angafune kuti kuwale ngati masana, nthawi zina ngati madzulo ndipo nthawi zina ngati kuli magetsi. Craig anati: “Mosiyana ndi mavidiyo, chithunzi chimodzi chimafunika kwambiri kuti tichijambule pamalo owala moyenera n’cholinga choti anthu adzamvetse zimene zikuchitika.”

  • Kusintha zinthu zina m’chithunzi. Chithunzicho chitajambulidwa, anachisintha kuti ndalamazo zisaoneke kwambiri. Anachita zimenezi n’cholinga choti anthu asamaone kuti ndalamazo ndi za dziko liti koma azichita chidwi ndi anthu a m’chithunzicho. Pamalo ojambulirawo, mtundu wa maferemu a chitseko ndi mawindo anali ofiira koma pachithunzichi anawasintha kuti akhale agirini. Anachita zimenezi kuti zigwirizane ndi mtundu umene unagwiritsidwa ntchito pamagaziniyo.

Kuwonjezera pa zithunzi zimene zimajambulidwa ku Patterson, pali enanso amene amajambula zithunzi zomwe zimapezeka m’mabuku athu. Anthuwa ali kumaofesi a nthambi osiyanasiyana monga ku Australia, Brazil, Canada, Germany, Japan, Korea, Malawi, Mexico ndi ku South Africa. Mwezi uliwonse a m’Dipatimenti ya Zithunzi ku Patterson amawonjezera zithunzi zokwana 2,500 pa zimene amasunga. Zina mwa zithunzizi zimagwiritsidwa ntchito m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndipo m’chaka cha 2015, magazini okwana 115 miliyoni ankafalitsidwa mwezi uliwonse. Ngati mukufuna kudziwa zambiri zimene timachita, mukhoza kubwera kuno ku Patterson kapena kunthambi ina iliyonse ya Mboni za Yehova padziko lapansi ndipo tidzakulandirani.

Akulalikira pogwiritsa ntchito magaziniyi

^ ndime 2 Timajambula zithunzi zambiri kuti tipeze chimodzi choti tigwiritse ntchito. Koma zina zimene sitinazigwiritse ntchito pa nthawiyo, timasunga ndipo timazigwiritsa ntchito pa nthawi ina.

^ ndime 4 Ngati tikufuna kujambula zithunzi pamsewu wa mumzinda winawake, timapempha chilolezo ku boma. Timawauza kuchuluka kwa anthu amene adzakhalepo komanso zipangizo zomwe tidzagwiritse ntchito.