“Ndikufuna kuti upite ku New York City, kusitudiyo yotchedwa Columbia Studios, kuti ukajambule nyimbo yathu imodzi. Koma chonde usauze aliyense nkhani imeneyi.”

Bambo William Mockridge

Mu 1913, a William Mockridge anachitadi ntchito yapaderayi, yomwe anapatsidwa ndi a Charles Taze Russell. * Nyimboyi ambiri amaitchula m’Chingelezi kuti “The Sweet By-and-By” ndipo inajambulidwa mwa pamwamba kwambiri. Patapita nthawi, bambo Mockridge anazindikira kuti nyimbo imene anaimba ija, idzagwiritsidwa ntchito mu “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” M’sewerolo munali nkhani za m’Baibulo ndiponso nyimbo zimene anaziphatikiza ndi zithunzi zoyenda. “Sewero la Pakanema” limeneli linaonetsedwa koyamba mu January 1914, ku New York City.

Nyimbo imene a William anaimba, inali imodzi mwa nyimbo 50 zimene zinkaimbidwa m’madera amene kunkaonetsedwa “Sewero la Pakanema” lachingelezi. Ngakhale kuti nyimbo zambiri zinaimbidwa ndi anthu ena, koma ndi zochepa chabe, kuphatikizapo ya a William, zimene Ophunzira Baibulo anasankha kuti zikhale m’seweroli. Nyimbozi zinali ndi mawu ochokera m’buku lawo la nyimbo lakuti Hymns of the Millennial Dawn.

Kusintha Mawu a Nyimbo

Kwa zaka zambiri a Mboni za Yehova akhala akugwiritsa ntchito nyimbo zolembedwa ndi anthu ena. Choncho mawu ena ankawasintha kuti agwirizane ndi mfundo za m’Baibulo, ngati zinali zofunika kutero.

Mwachitsanzo, nyimbo imodzi imene inkaimbidwa mu “Sewero la Pakanema” inali ndi mutu wakuti, “Mfumu Yathu Ikupita Ikuguba.” Mawuwa anatengedwa m’nyimbo inayake yonena za nkhondo. Mawu oyamba a m’nyimboyo anali akuti: “Maso anga aona ulemelero wa kubwera kwa Ambuye.” Koma Ophunzira Baibulo anasintha mawuwa ndipo anayamba kumveka kuti: “Maso anga aona ulemelero wa kukhalapo kwa Ambuye.” Anasintha mawuwa kuti agwirizane ndi zimene amakhulupirira, zakuti ulamuliro wa Yesu Khristu ukukhudzanso nthawi ya kukhalapo kwake, yomwe ndi yaitali, osati kubwera kwake kokha.Mateyu 24:3.

Mu 1966 anatulutsa buku la nyimbo lakuti, Kuyimba ndi Kutsagana ndi Nyimbo za Malimba M’mitima Mwanu. M’bukuli anachotsamo nyimbo zonse zimene zinachokera ku zipembedzo zina. M’chaka chimenecho, a Mboni za Yehova anakonza zoti pakhale gulu la oimba, kuti liimbe ndi kujambula nyimbo zokwana 119 za m’bukuli. Mipingo inkagwiritsa ntchito nyimbozo poimba pa misonkhano yawo, ndipo anthu ambiri ankasangala kumazimvetsera akhala kunyumba kwawo.

Mu 2009 a Mboni za Yehova anatulutsa buku lawo la nyimbo latsopano lotchedwa, Imbirani Yehova. Ndipo panopa nyimbo za mawu m’zinenero zosiyanasiyana zochokera m’bukuli, zajambulidwa. Kwa nthawi yoyamba mu 2013, a Mboni za Yehova anayamba kutulutsa mavidiyo a nyimbo za ana. Vidiyo imodzi ili ndi mutu wakuti Pempherani Nthawi Iliyonse. Pa mwezi, nyimbo zomwe zili pawebusaiti ya jw.org, zimapangidwa dawunilodi maulendo mamiliyoni ambirimbiri.

Anthu ochuluka akuyamikira kwambiri nyimbo zimenezi. Pofotokoza zokhudza nyimbo za m’buku la Imbirani Yehova, mayi wina dzina lake Julie, analemba kuti: “Nyimbo zatsopanozi n’zosangalatsa. Ndikakhala ndekha, ndimakonda kumvetsera nyimbo zimene zimandifika pamtima kwambiri. Zimenezi zandithandiza kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ulimbe kwambiri, komanso kuti ndizimutumikira ndi mtima wanga wonse.”

Pofotokoza za vidiyo ya Pempherani Nthawi Iliyonse, mayi wina dzina lake Heather, analemba mmene vidiyoyi yathandizira mwana wake wamwamuna wa zaka 7 ndi mwana wake wamkazi wa zaka 9. Mayiyu analemba kuti: “Vidiyoyi yathandiza ana anga kuti azipemphera kwa Yehova nthawi ina iliyonse imene akufuna, osati chabe pamene kwacha m’mawa kapena pamene ali ndi ife makolo awo.”

^ ndime 3 Charles Taze Russell anakhala ndi moyo kuyambira mu 1852 mpaka mu 1916, ndipo ankatsogolera a Mboni za Yehova, omwe ankadziwika kuti Ophunzira Baibulo pa nthawiyo.